Salimo 70:1-5
-
Anapempha kuti amuthandize mwamsanga
-
“Ndithandizeni mwamsanga” (5)
-
Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide. Nyimbo ya chikumbutso.
70 Inu Mulungu, ndipulumutseni,Inu Yehova, ndithandizeni mofulumira.+
2 Amene akufuna kuchotsa moyo wangaAchititsidwe manyazi komanso anyozeke.
Amene akusangalala ndi tsoka langaAbwerere mwamanyazi.
3 Onse amene akunena kuti: “Eyaa! Eyaa!”
Abwezedwe mwamanyazi.
4 Koma amene akufunafuna inu,Akondwere ndi kusangalala chifukwa choti akudziwani.+
Amene amasangalala ndi njira imene mumapulumutsira anthu, nthawi zonse azinena kuti:
“Mulungu alemekezeke.”
5 Koma ine ndine munthu wovutika komanso wosauka.+Inu Mulungu, ndithandizeni mwamsanga.+
Inu ndi amene mumandithandiza komanso kundipulumutsa.+Inu Yehova musachedwe.+