Salimo 39:1-13
Kwa wotsogolera nyimbo. Aimbe nyimboyi pa Yedutuni.*+ Nyimbo ya Davide.
39 Ine ndinanena kuti: “Ndidzakhala wosamala ndi zochita zangaKuti ndisachimwe ndi lilime langa.+
Ndidzaphimba pakamwa panga kuti ndisalankhule+Nthawi zonse pamene woipa ali pamaso panga.”
2 Ndinakhala chete osalankhula kanthu.+Sindinalankhule kanthu ngakhale kokhudza zinthu zabwino,Koma ululu wanga unali waukulu.
3 Mumtima mwanga munayaka moto.*
Ndili mkati moganizira,* moto unapitiriza kuyaka.
Kenako ndinanena kuti:
4 “Inu Yehova, ndithandizeni kuzindikira kuti moyo wanga ndi waufupi,Komanso kudziwa chiwerengero cha masiku anga,+Kuti ndidziwe kuti moyo wanga ndi waufupi bwanji.*
5 Ndithudi, mwachepetsa masiku a moyo wanga,+Ndipo masiku a moyo wanga si kanthu pamaso panu.+
Ndithudi, munthu aliyense ngakhale ataoneka kuti ndi wotetezeka, amangokhala ngati mpweya.+ (Selah)
6 Zoonadi, moyo wa munthu aliyense umangodutsa ngati chithunzithunzi.
Iye amangovutika* popanda phindu.
Amaunjika chuma, osadziwa kuti amene adzasangalale nacho ndi ndani.+
7 Ndiyeno inu Yehova, kodi ine ndikuyembekezera chiyani?
Chiyembekezo changa ndi inu nokha.
8 Ndipulumutseni ku zolakwa zanga zonse.+
Musalole kuti munthu wopusa azindinyoza.
9 Ndinakhala chete.Sindinatsegule pakamwa panga,+Chifukwa inu ndi amene munachita zimenezi.+
10 Ndichotsereni mliri umene mwandigwetsera.
Mphamvu zanga zatha chifukwa inu mwandipatsa chilango.
11 Mumathandiza munthu kuti asinthe pomupatsa chilango chifukwa cha zolakwa zake.+Mumawononga zinthu zake zamtengo wapatali ngati mmene njenjete* imachitira.
Ndithudi, munthu aliyense ali ngati mpweya.+ (Selah)
12 Imvani pemphero langa, inu Yehova,Mvetserani pamene ndikulira kupempha thandizo.+
Musanyalanyaze misozi yanga.
Chifukwa ndine mlendo kwa inu,+Mlendo wongodutsa mofanana ndi makolo anga onse.+
13 Musandiyangʼane mutakwiya, kuti ndikhalenso wosangalalaNdisanamwalire nʼkuiwalika.”
Mawu a M'munsi
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “munatentha kwambiri.”
^ Kapena kuti, “Ndikuusa moyo.”
^ Kapena kuti, “kuti ndine wosakhalitsa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amangopanga phokoso.”
^ Mawu a Chiheberi amene amasuliridwa kuti “njenjete” amatanthauza mtundu winawake wa kadziwotche amene amadya zovala.