Salimo 122:1-9
Nyimbo Yokwerera Kumzinda. Salimo la Davide.
122 Ndinasangalala pamene anandiuza kuti:
“Tiyeni tipite kunyumba ya Yehova.”+
2 Ndipo tsopano mapazi athu aimaPamageti ako iwe Yerusalemu.+
3 Yerusalemu ndi mzinda umene wamangidwaNgati chinthu chimodzi chogwirizana.+
4 Mafuko apita kumeneko,Mafuko a Ya,*Mogwirizana ndi chilamulo chimene* Isiraeli anapatsidwaKuti azikatamanda dzina la Yehova.+
5 Chifukwa kumeneko nʼkumene kunaikidwa mipando yachiweruzo,+Mipando yachifumu ya nyumba ya Davide.+
6 Pemphererani mtendere wa Yerusalemu.+
Amene amakukonda, mzinda iwe, adzakhala otetezeka.
7 Mtendere upitirize kukhala mʼmalo ako otchingidwa ndi mpanda wolimba,Chitetezo chipitirize kukhala munsanja zako zokhala ndi mpanda wolimba.
8 Chifukwa choti ndimakonda abale anga komanso anzanga ndikunena kuti:
“Mumzindawu mukhale mtendere.”
9 Chifukwa choti ndimakonda nyumba ya Yehova Mulungu wathu,+Ndidzapitiriza kukufunira zabwino.