Salimo 55:1-23
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Masikili.* Salimo la Davide.
55 Inu Mulungu, mvetserani pemphero langa,+Ndipo musanyalanyaze pempho langa lakuti mundichitire chifundo.*+
2 Ndimvetsereni ndipo mundiyankhe.+
Mtima wanga suli mʼmalo chifukwa cha nkhawa zanga,+Ndipo ndikuvutika mumtima mwanga
3 Chifukwa cha zimene mdani wanga akunenaKomanso chifukwa chakuti woipa akundipanikiza.
Iwo andiunjikira mavuto,Ndipo mwaukali akundisungira chidani.+
4 Mtima wanga ukundipweteka kwambiri,+Ndipo ndikuopa imfa.+
5 Ndagwidwa ndi mantha ndipo ndikunjenjemera,Komanso ndikunthunthumira.
6 Nthawi zonse ndimanena kuti: “Ndikanakhala ndi mapiko ngati njiwa!
Ndikanaulukira kutali nʼkukakhala malo otetezeka.
7 Ndikanathawira kutali.+
Ndikanapita kukakhala mʼchipululu.+ (Selah)
8 Ndikanathawira kumalo otetezeka,Kutali ndi mphepo yamphamvu, kutali ndi mphepo yamkuntho.”
9 Inu Yehova, sokonezani anthu oipa, ndipo sokonezani mapulani awo,*+Chifukwa ndaona zachiwawa ndi mikangano mumzinda.
10 Masana ndi usiku amayenda pamwamba pa mpanda kuzungulira mzindawo.Ndipo mumzindawo muli chidani ndi mavuto.+
11 Mmenemo muli mavuto okhaokha.Ndipo kuponderezana ndi chinyengo sizimachoka kubwalo la mzindawo.+
12 Chifukwa amene akundinyoza si mdani.+Akanakhala mdani ndikanapirira.
Amene wandiukira si munthu wodana nane kwambiri.Akanakhala munthu wodana nane kwambiri ndikanabisala.
13 Koma ndi iwe, munthu ngati ine ndemwe,*+Mnzanga weniweni amene ndikumudziwa bwino.+
14 Tinali mabwenzi apamtima.Tinkayenda limodzi ndi gulu la anthu kupita kunyumba ya Mulungu.
15 Iwo awonongedwe!+
Atsikire ku Manda* ali amoyo.Chifukwa mʼmalo amene amakhala komanso mʼmitima yawo muli zoipa.
16 Koma ine ndidzafuulira Mulungu,Ndipo Yehova adzandipulumutsa.+
17 Usiku, mʼmawa ndi masana ndimavutika ndipo ndimabuula,*+Koma Mulungu amamva mawu anga.+
18 Iye adzandipulumutsa* kwa anthu amene akundiukira nʼkundipatsa mtendere,Chifukwa gulu la anthu landiukira.+
19 Mulungu adzamva ndipo adzawapatsa chilango,+Amene wakhala pampando wachifumu kuyambira kalekale.+ (Selah)
Iwo adzakana kusintha,Anthu amene sanaope Mulungu.+
20 Iye* anaukira anthu amene anali naye pamtendere.+Iye anaphwanya pangano lake.+
21 Mawu ake ndi osalala kuposa mafuta amumkaka,+Koma mumtima mwake amakonda nkhondo.
Mawu ake ndi osalala kuposa mafuta,Koma ali ngati malupanga akuthwa.+
22 Umutulire Yehova nkhawa zako,+Ndipo iye adzakuthandiza.+
Iye sadzalola kuti munthu wolungama agwe.*+
23 Koma inu Mulungu, mudzatsitsira oipawo mʼdzenje lakuya.+
Anthu amene ali ndi mlandu wa magazi komanso achinyengowo, sadzakwanitsa kukhala ngakhale hafu ya moyo wawo.+
Koma ine ndidzakhulupirira inu.
Mawu a M'munsi
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “Ndipo musabisale ndikamapemphera kuti mundithandize.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “sokonezani lilime lawo.”
^ Kapena kuti, “munthu wofanana ndi ine.”
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “ndimabangula.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “adzandiwombola.”
^ Ameneyu ndi mnzake wakale amene watchulidwa muvesi 13 ndi 14.
^ Kapena kuti, “adzandire.”