Salimo 83:1-18

  • Pemphero la pa nthawi imene adani akuwaukira

    • “Inu Mulungu, musakhale chete” (1)

    • Adani akhale ngati mapesi amene amauluka ndi mphepo (13)

    • Dzina la Mulungu ndi Yehova (18)

Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+ 83  Inu Mulungu, musakhale chete.+Musakhale chete osalankhula kanthu kapena kuchita chilichonse, inu Mulungu.   Taonani! Adani anu akuchita phokoso.+Anthu amene amadana nanu akuchita zinthu modzikuza.*   Mwachinsinsi komanso mochenjera iwo amakonzera chiwembu anthu anu.Iwo amakonzera chiwembu anthu anu omwe ndi amtengo wapatali.*   Iwo akunena kuti: “Bwerani tiwawononge kuti asakhalenso mtundu,+Kuti dzina la Isiraeli lisadzakumbukiridwenso.”   Mogwirizana iwo amapangana zoti achite,*Iwo apanga mgwirizano* kuti atsutsane ndi inu+   Aedomu, mbadwa za Isimaeli, Amowabu+ komanso mbadwa za Hagara,+   Agebala, Aamoni,+ Aamaleki,Afilisiti+ pamodzi ndi anthu a ku Turo.+   Asuri nawonso agwirizana nawo,+Ndipo amathandiza* ana aamuna a Loti.+ (Selah)   Muwachitire zimene munachitira Midiyani,+Komanso zimene munachitira Sisera ndi Yabini kumtsinje wa Kisoni.*+ 10  Iwo anawonongedwa ku Eni-dori.+Anasanduka manyowa munthaka. 11  Anthu awo olemekezeka muwachititse kukhala ngati Orebi ndi Zeebi.+Ndipo akalonga* awo muwachititse kukhala ngati Zeba ndi Zalimuna.+ 12  Chifukwa iwo anena kuti: “Tiyeni tilande dziko limene Mulungu amakhala.” 13  Inu Mulungu wanga, achititseni kukhala ngati udzu wouma wouluzika ndi mphepo,+Ngati mapesi amene amauluka ndi mphepo. 14  Ngati moto umene umayatsa nkhalango,Ngati malawi a moto umene ukuyaka mʼmapiri,+ 15  Muwathamangitse ndi mphepo yanu yamphamvu,+Ndipo muwaopseze ndi mphepo yanu yamkuntho.+ 16  Phimbani* nkhope zawo ndi manyazi,Kuti afunefune dzina lanu, inu Yehova. 17  Achititsidwe manyazi ndipo akhale ndi mantha mpaka kalekale.Anyozeke ndipo atheretu. 18  Anthu adziwe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova,+Inu nokha ndinu Wamʼmwambamwamba, woyenera kulamulira dziko lonse lapansi.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “atukula mitu yawo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “omwe ndi obisika.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndi mtima wonse iwo amagawana nzeru.”
Kapena kuti, “pangano.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Amakhala ngati dzanja kwa.”
Kapena kuti, “kukhwawa la Kisoni.”
Kapena kuti, “atsogoleri.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Dzazani.”