Salimo 17:1-15
Pemphero la Davide.
17 Imvani dandaulo langa lopempha kuti mundichitire chilungamo, inu Yehova.Mvetserani kulira kwanga kopempha thandizo.Imvani pemphero langa lopanda chinyengo.+
2 Mupereke chigamulo chachilungamo mʼmalo mwa ine.+Maso anu aone kuti ndine wolungama.
3 Mwafufuza mtima wanga, mwandifufuza ngakhale usiku,+Ndipo mwandiyenga.+Mudzapeza kuti ndinalibe zolinga zochita choipa chilichonse.Ndipo pakamwa panga sipanachimwe.
4 Kunena za ntchito za anthu,Mogwirizana ndi mawu apakamwa panu, ndapewa kuyenda mʼnjira za wachifwamba.+
5 Ndithandizeni kuti ndipitirize kuyenda mʼnjira zanu,Kuti mapazi anga asapunthwe.+
6 Ine ndikuitana inu, chifukwa mudzandiyankha,+ inu Mulungu.
Tcherani khutu* kwa ine. Imvani mawu anga.+
7 Sonyezani modabwitsa chikondi chanu chokhulupirika,+Inu Mpulumutsi wa anthu amene amathawira kudzanja lanu lamanjaKuthawa anthu amene akupandukirani.
8 Nditetezeni ngati mwana wa diso lanu,+Ndibiseni mumthunzi wa mapiko anu.+
9 Nditetezeni kwa anthu oipa amene akundiukira,Kwa adani* ochokera kufumbi amene andizungulira.+
10 Mitima yawo siimva chisoni,*Ndipo amalankhula modzikuza ndi pakamwa pawo.
11 Tsopano adaniwo atizungulira,+Akufufuza mpata kuti atigwetse.*
12 Ali ngati mkango umene ukufunitsitsa kukhadzula nyama,Ngati mkango wamphamvu umene wabisalira nyama.
13 Nyamukani, inu Yehova, mulimbane naye+ nʼkumugwetsa.Ndipulumutseni kwa woipayo ndi lupanga lanu.
14 Ndipulumutseni ndi dzanja lanu, inu Yehova,Kwa anthu amʼdzikoli* amene gawo lawo lili mʼmoyo uno,+Anthu amene mwawakhutitsa ndi zinthu zabwino zimene mumapereka+Omwe amasiyira cholowa ana awo aamuna ochuluka.
15 Koma ine ndidzaona nkhope yanu mʼchilungamo.Ndikadzuka ndimadziwa kuti muli nane* ndipo ndimakhutira.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Weramani ndi kumvetsera.”
^ Kapena kuti, “adani amene akufuna moyo wanga.”
^ Kapena kuti, “Adzikuta ndi mafuta awo omwe.”
^ Kapena kuti, “atiponyere pansi.”
^ Kapena kuti, “amʼnthawi ino.”
^ Kapena kuti, “Ndikadzuka ndimakuonani.”