Salimo 60:1-12
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira kaimbidwe ka nyimbo ya “Duwa la Chikumbutso.” Mikitamu.* Salimo la Davide. Nyimbo yophunzitsira. Pa nthawi imene Davide anali pankhondo ndi Aramu-naharaimu ndi Aramu-Zoba, ndipo Yowabu anabwerera nʼkukapha Aedomu 12,000 mʼchigwa cha Mchere.+
60 Inu Mulungu, munatikana ndipo munatigonjetsa.+
Munatikwiyira. Koma tsopano tiloleni tibwerere kwa inu.
2 Mwachititsa kuti dziko lapansi ligwedezeke ndipo mwalingʼamba.
Tsekani mingʼalu yake, chifukwa likugwa.
3 Mwachititsa kuti anthu anu akumane ndi mavuto.
Mwatimwetsa vinyo amene wachititsa kuti tiziyenda dzandidzandi.+
4 Perekani* chizindikiro kwa anthu amene amakuopaniKuti athawe ndi kuzemba uta. (Selah)
5 Kuti anthu amene mumawakonda apulumutsidwe,Tipulumutseni ndi dzanja lanu lamanja ndipo mutiyankhe.+
6 Popeza ndi woyera,* Mulungu walankhula kuti:
“Ndidzasangalala popereka Sekemu ngati cholowa,+Ndipo ndidzayezera anthu anga malo mʼchigwa cha Sukoti.+
7 Giliyadi ndi wanga, ngati mmene zilili ndi Manase,+Ndipo Efuraimu ndi chipewa choteteza* mutu wanga.Yuda akuimira mphamvu zanga zolamula.+
8 Mowabu ndi beseni langa losambiramo.+
Edomu ndidzamuponyera nsapato zanga.+
Ndidzafuula mosangalala chifukwa chogonjetsa Filisitiya.”+
9 Ndi ndani amene adzandibweretse kumzinda wozunguliridwa ndi adani?*
Ndi ndani amene adzanditsogolere mpaka kukafika ku Edomu?+
10 Kodi si inu Mulungu amene munatikana,Mulungu wathu, amene simukutsogoleranso magulu athu ankhondo?+
11 Tithandizeni pamene tikukumana ndi mavuto,Chifukwa chipulumutso chochokera kwa munthu nʼchopanda pake.+
12 Mulungu adzatipatsa mphamvu,+Ndipo adzapondaponda adani athu.+
Mawu a M'munsi
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Mabaibulo ena amati, “Mwapatsa.”
^ Mabaibulo ena amati, “Mʼmalo ake opatulika.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “malo achitetezo oteteza.”
^ Mabaibulo ena amati, “wotetezedwa.”