Salimo 9:1-20
Kwa wotsogolera nyimbo, pa Mutilabeni.* Nyimbo ya Davide.
א [Aleph]
9 Ndidzakutamandani inu Yehova ndi mtima wanga wonse.Ndidzafotokoza za ntchito zanu zonse zodabwitsa.+
2 Ndidzakondwera ndi kusangalala chifukwa cha inu,Ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu, inu Wamʼmwambamwamba.+
ב [Beth]
3 Adani anga akathawa,+Adzapunthwa nʼkuwonongedwa pamaso panu.
4 Chifukwa mumanditeteza kuti mlandu wanga uweruzidwe mwachilungamo.Mwakhala pampando wanu wachifumu ndipo mukuweruza mwachilungamo.+
ג [Gimel]
5 Mwadzudzula mitundu ya anthu+ ndipo mwawononga anthu oipa,Nʼkufufuta dzina lawo kwamuyaya.
6 Mdani wawonongedwa mpaka kalekale.Mwawononganso mizinda yawo,Ndipo sadzakumbukiridwanso.+
ה [He]
7 Koma Yehova ndi mfumu mpaka kalekale.+Iye akupitiriza kulamulira ndipo nthawi zonse amaweruza mwachilungamo.+
8 Iye adzaweruza anthu okhala padziko lapansi mwachilungamo.+Adzapereka zigamulo zolungama pa milandu ya mitundu ya anthu.+
ו [Waw]
9 Yehova adzakhala malo otetezeka* komwe anthu oponderezedwa angathawireko,+Malo otetezeka othawirako pa nthawi ya mavuto.+
10 Anthu odziwa dzina lanu adzakukhulupirirani.+Simudzasiya anthu amene amakufunafunani, inu Yehova.+
ז [Zayin]
11 Imbani nyimbo zotamanda Yehova, amene akukhala mu Ziyoni.Dziwitsani mitundu ya anthu za ntchito zake.+
12 Mulungu adzakumbukira anthu ovutika ndipo adzabwezera anthu amene anawapha.+Iye sadzaiwala kulira kwa anthu ovutikawo.+
ח [Heth]
13 Ndikomereni mtima inu Yehova. Inu amene mukundichotsa pakhomo la imfa,+Onani mmene anthu amene akudana nane akundizunzira,
14 Kuti ndilengeze ntchito zanu zotamandika pamageti a mwana wamkazi wa Ziyoni,*+Komanso kuti ndisangalale chifukwa mwandipulumutsa.+
ט [Teth]
15 Mitundu ya anthu yagwera mʼdzenje limene anakumba okha.Phazi lawo lakodwa mu ukonde umene anatchera okha.+
16 Yehova amadziwika ndi ziweruzo zimene amapereka.+
Woipa wakodwa mumsampha umene watchera yekha.+
Higayoni.* (Selah)
י [Yod]
17 Anthu oipa adzapita ku Manda,*Anthu a mitundu yonse amene aiwala Mulungu adzapita kumeneko.
18 Koma Mulungu sadzaiwala anthu osauka,+Ndiponso chiyembekezo cha anthu ofatsa sichidzatha.+
כ [Kaph]
19 Nyamukani, inu Yehova! Musalole kuti munthu apambane.
Mitundu ya anthu iweruzidwe pamaso panu.+
20 Achititseni mantha, inu Yehova,+Chititsani kuti mitundu ya anthu idziwe kuti iwo ndi anthu basi. (Selah)
Mawu a M'munsi
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “malo okwezeka achitetezo.”
^ Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.