1 Mbiri 22:1-19

  • Davide anakonzekera zinthu zomangira kachisi (1-5)

  • Davide anapereka malangizo kwa Solomo (6-16)

  • Akalonga analamulidwa kuti athandize Solomo (17-19)

22  Kenako Davide anati: “Malo ano ndi nyumba ya Yehova Mulungu woona ndipo lili apali, ndi guwa lansembe zopsereza za Isiraeli.”+ 2  Atatero, Davide analamula kuti asonkhanitse alendo okhala mʼdziko la Isiraeli.+ Alendowo anawapatsa ntchito yosema miyala, kuti azisema miyala yomangira nyumba ya Mulungu woona.+ 3  Komanso Davide anasonkhanitsa zitsulo zambirimbiri zopangira misomali ya zitseko za mageti ndiponso zopangira zida zopanira zinthu. Anasonkhanitsanso kopa* wambirimbiri wosatheka kumuyeza kulemera kwake.+ 4  Davide anasonkhanitsanso matabwa osawerengeka a mkungudza,+ popeza Asidoni+ ndi anthu a ku Turo+ anali atamubweretsera matabwa ambirimbiri a mkungudza. 5  Kenako Davide anati: “Mwana wanga Solomo ndi wamngʼono komanso sadziwa zambiri+ ndipo nyumba yoti adzamangire Yehova idzakhala yaikulu, yokongola+ ndi yogometsa+ nʼcholinga choti idzakhale yodziwika padziko lonse.+ Ndiye ndimukonzera zipangizo zoti adzagwiritsire ntchito.” Choncho Davide asanafe, anasonkhanitsa zipangizo zambirimbiri pokonzekera ntchitoyo. 6  Komanso anaitana mwana wake Solomo ndipo anamupatsa malangizo okhudza ntchito yomanga nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli. 7  Davide anauza mwana wake Solomo kuti: “Ineyo ndinkafunitsitsa kumanga nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wanga.+ 8  Koma Yehova anandiuza kuti: ‘Iweyo wapha anthu* ambirimbiri ndipo wamenya nkhondo zikuluzikulu. Sudzamanga nyumba ya dzina langa,+ chifukwa wapha anthu ambirimbiri pamaso panga padziko lapansi. 9  Tamvera, udzabereka mwana.+ Mwana ameneyo adzakhala munthu wokonda mtendere ndipo ndidzachititsa kuti azikhala mwamtendere komanso asamavutitsidwe ndi adani ake omuzungulira.+ Nʼchifukwa chake dzina lake adzakhala Solomo*+ ndipo mʼmasiku ake ndidzapatsa Aisiraeli bata ndi mtendere.+ 10  Iyeyo ndi amene adzamange nyumba ya dzina langa.+ Adzakhala mwana wanga ndipo ine ndidzakhala bambo ake.+ Ndidzakhazikitsa mpando wake wachifumu mu Isiraeli ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.’+ 11  Tsopano mwana wanga, Yehova akhale nawe ndipo zinthu zikuyendere bwino. Umange nyumba ya Yehova Mulungu wako, mogwirizana ndi zimene iye analankhula zokhudza iweyo.+ 12  Yehova akupatse nzeru ndi kuzindikira.+ Akupatsenso mphamvu zotsogolera Aisiraeli, kuti usunge chilamulo cha Yehova Mulungu wako.+ 13  Zinthu zidzakuyendera bwino ukamatsatira mosamala malamulo+ ndi ziweruzo zimene Yehova analamula Mose kuti apatse Aisiraeli.+ Khala wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Usaope kapena kuchita mantha.+ 14  Ndayesetsa mwakhama kusonkhanitsa golide womangira nyumba ya Yehova wokwana matalente* 100,000 ndi siliva wokwana matalente 1 miliyoni. Koma nʼzosatheka kuyeza kulemera kwa kopa ndi zitsulo+ chifukwa nʼzochuluka kwambiri. Ndasonkhanitsanso matabwa ndi miyala+ pokonzekera, koma udzawonjezerapo zina. 15  Palinso antchito ambirimbiri. Pali osema miyala, amisiri a miyala+ ndi a matabwa ndiponso akatswiri a ntchito zosiyanasiyana.+ 16  Golide, siliva, kopa ndi zitsulo nʼzosatheka kuziwerenga.+ Yamba kugwira ntchito imeneyi ndipo Yehova akhale nawe.”+ 17  Kenako Davide analamula akalonga onse a Isiraeli kuti athandize mwana wake Solomo. Iye anati: 18  “Kodi Yehova Mulungu wanu sali nanu? Kodi sanakupatseni mtendere mʼdziko lonseli? Chifukwa wandipatsa anthu amʼdzikoli ndipo dzikoli lili mʼmanja mwa Yehova ndi anthu ake. 19  Choncho muzifunafuna Yehova Mulungu wanu+ ndi mtima wanu wonse ndiponso moyo wanu wonse. Yambani kumanga nyumba yopatulika ya Yehova Mulungu woona,+ kuti mukatenge likasa la pangano la Yehova ndi ziwiya zopatulika za Mulungu woona+ nʼkuziika mʼnyumba ya dzina la Yehova imene imangidweyo.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mkuwa.”
Kapena kuti, “wakhetsa magazi.”
Kuchokera ku mawu a Chiheberi otanthauza, “Mtendere.”
Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.