Kalata ya Yakobo 2:1-26

  • Kuchita zokondera ndi tchimo (1-13)

    • Chikondi ndi lamulo lachifumu (8)

  • Chikhulupiriro chopanda ntchito zake ndi chakufa (14-26)

    • Ziwanda zimakhulupirira ndipo zimanjenjemera (19)

    • Abulahamu ankadziwika kuti ndi mnzake wa Yehova (23)

2  Abale anga, kodi mukuganiza kuti mukukhulupirira Ambuye wathu Yesu Khristu, amene ndi waulemerero, pamene mukuchita zokondera?+  Munthu amene wavala mphete zagolide ndi zovala zapamwamba akafika pamsonkhano wanu, ndiye winanso wosauka amene wavala zovala zakuda akafika,  kodi mumasangalala ndi amene wavala zovala zapamwamba uja nʼkumuuza kuti, “Khalani pamalo abwinowa” koma wosauka uja nʼkumuuza kuti: “Iwe ubaima choncho,” kapena, “Khala pansipa pafupi ndi chopondapo mapazi anga”?+  Ndiye mukamachita zimenezi, kodi simukusonyeza tsankho pakati panu?+ Ndipo kodi pamenepa simunakhale oweruza amene akupereka zigamulo zoipa?+  Tamverani abale anga okondedwa. Kodi Mulungu sanasankhe anthu amene dzikoli limawaona kuti ndi osauka kuti akhale olemera mʼchikhulupiriro+ komanso kuti akhale oyenera kupatsidwa Ufumu umene Mulungu analonjeza anthu amene amamukonda?+  Koma inu simukulemekeza anthu osauka. Kodi si olemera amene amakuvutitsani+ komanso kukupititsani kumabwalo amilandu?  Kodi si omwewo amene amanyoza dzina labwino kwambiri limene munapatsidwa?  Ndiye ngati mukutsatira lamulo lachifumu lakuti, “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha,”+ ngati mmene lemba limanenera, mukuchita bwino ndithu.  Koma mukapitiriza kukhala okondera,+ mukuchita tchimo ndipo lamulo likusonyezeratu* kuti ndinu olakwa.+ 10  Aliyense amene amamvera Chilamulo akalakwitsa mbali imodzi, ndiye kuti walakwira Chilamulo chonse.+ 11  Chifukwa amene ananena kuti, “Musachite chigololo,”+ ananenanso kuti, “Musaphe munthu.”+ Ndiye ngati iwe sunachite chigololo koma wapha munthu, ndiye kuti walakwira chilamulo. 12  Muzilankhula komanso kuchita zinthu ngati anthu amene adzaweruzidwe ndi chilamulo cha anthu amene ali pa ufulu.*+ 13  Chifukwa munthu amene sasonyeza chifundo adzaweruzidwa mopanda chifundo.+ Chifundo nʼchachikulu kuposa chiweruzo. 14  Abale anga, kodi pali phindu lanji ngati wina atanena kuti ali ndi chikhulupiriro koma sachita ntchito zake?+ Kodi chikhulupiriro chimenecho chingamupulumutse?+ 15  Ngati mʼbale kapena mlongo alibe zovala* komanso chakudya chokwanira pa tsikulo, 16  koma wina mwa inu nʼkumuuza kuti, “Uyende bwino, upeze zovala ndi zakudya za tsiku lililonse,” koma osamupatsa zimene akufunikirazo kuti akhale ndi moyo, kodi pali phindu lanji?+ 17  Chimodzimodzinso chikhulupiriro pachokha, ngati chilibe ntchito zake, ndi chakufa.+ 18  Koma wina anganene kuti: “Iweyo uli ndi chikhulupiriro, koma ine ndili ndi ntchito zake. Undionetse chikhulupiriro chako popanda ntchito zake, ndipo ine ndikuonetsa chikhulupiriro changa kudzera muntchito zanga.” 19  Umakhulupirira kuti kuli Mulungu mmodzi, si choncho? Ukuchita bwino. Komatu ziwanda nazonso zimakhulupirira ndipo zimanjenjemera.+ 20  Mbuli iwe, kodi sukudziwa kuti chikhulupiriro chopanda ntchito zake nʼchopanda phindu? 21  Kodi Abulahamu atate wathu sanaonedwe kuti ndi wolungama chifukwa cha ntchito zake, atapereka mwana wake Isaki nsembe paguwa?+ 22  Nʼzoonekeratu kuti chikhulupiriro chake chinayendera limodzi ndi ntchito zake, ndipo ntchito zakezo zinachititsa kuti chikhulupiriro chakecho chikhale changwiro.+ 23  Choncho lemba linakwaniritsidwa limene limati: “Abulahamu anakhulupirira zimene Yehova* anamuuza ndipo ankaonedwa kuti ndi wolungama,”+ choncho ankadziwika kuti ndi mnzake wa Yehova.*+ 24  Mwaonatu kuti munthu amaonedwa kuti ndi wolungama chifukwa cha ntchito zake, osati chifukwa cha chikhulupiriro chokha. 25  Mofanana ndi zimenezi, kodi Rahabi amene anali hule uja, sanaonedwenso kuti ndi wolungama chifukwa cha ntchito zake, atalandira bwino anthu amene ankafufuza dziko lawo nʼkuwathandiza kuti athawe kudzera njira ina?+ 26  Ndithudi, thupi lopanda mzimu* limakhala lakufa,+ mofanana ndi zimenezi nachonso chikhulupiriro chopanda ntchito zake ndi chakufa.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “ndipo lamulo likukutsutsani.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chilamulo cha ufulu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ali maliseche.”
Kapena kuti, “mpweya.”