Kalata ya Yakobo 4:1-17

  • Musachite ubwenzi ndi dziko (1-12)

    • Tsutsani Mdyerekezi (7)

    • Yandikirani Mulungu (8)

  • Anawachenjeza kuti apewe kunyada (13-17)

    • “Yehova akalola” (15)

4  Kodi nkhondo ndi ndewu zimene zikuchitika pakati panu zikuchokera kuti? Kodi sizikuchokera mʼzilakolako za thupi lanu zimene zikulimbana kuti zizilamulira matupi anu?*+  Mumalakalaka, koma simulandira zimene mukulakalakazo. Mukupitiriza kupha anthu ndiponso mumasirira mwansanje koma simupeza kanthu. Mukupitiriza kukangana komanso kuchita nkhondo.+ Simunalandire chifukwa chakuti simunapemphe.  Mukapempha, simulandira chifukwa mumapempha ndi cholinga choipa, kuti mukhutiritse zilakolako za matupi anu.  Achigololo inu,* kodi simukudziwa kuti kuchita ubwenzi ndi dziko nʼkudziika pa udani ndi Mulungu? Choncho aliyense amene akufuna kukhala bwenzi la dziko akudzipangitsa kuti akhale mdani wa Mulungu.+  Kapena kodi mukuganiza kuti lemba limanena popanda chifukwa kuti: “Mzimu umene wakhazikika mwa ife umalakalaka mwansanje zinthu zosiyanasiyana”?+  Komabe, kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu amapereka kumaposa khalidwe limeneli. Nʼchifukwa chake lemba limati: “Mulungu amatsutsa odzikuza,+ koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.”+  Choncho gonjerani Mulungu,+ koma tsutsani Mdyerekezi+ ndipo adzakuthawani.+  Yandikirani Mulungu ndipo iyenso adzakuyandikirani.+ Yeretsani manja anu ochimwa inu,+ ndipo yeretsani mitima yanu+ okayikakayika inu.  Imvani chisoni ndipo lirani.+ Kuseka kwanu kusanduke kulira ndipo chisangalalo chanu chisanduke chisoni. 10  Dzichepetseni pamaso pa Yehova*+ ndipo iye adzakukwezani.+ 11  Abale, musiye kunenerana zoipa.+ Aliyense amene akunenera zoipa mʼbale wake kapena kumuweruza, akunenera zoipa komanso kuweruza lamulo. Ndiye ngati ukuweruza lamulo, sukuchita zimene lamulo limanena koma ndiwe woweruza. 12  Komatu Wopereka Malamulo komanso Woweruza alipo mmodzi yekha,+ amenenso akhoza kupulumutsa ndi kuwononga.+ Ndiye iwe ndiwe ndani kuti uziweruza mnzako?+ 13  Tamverani inu amene mumanena kuti: “Lero kapena mawa tipita kumzinda wakutiwakuti ndipo tikatha chaka kumeneko. Tikachita malonda kumeneko nʼkupeza phindu.”+ 14  Mumanena zimenezi chonsecho simukudziwa kuti moyo wanu udzakhala wotani mawa.+ Chifukwa muli ngati nkhungu imene imangooneka kwa kanthawi kochepa kenako nʼkuzimiririka.+ 15  Mʼmalomwake muzinena kuti: “Yehova* akalola,+ tikhala ndi moyo ndipo tichita zakutizakuti.” 16  Koma inu mumakonda kunyada komanso kudzitama. Kudzitama konse koteroko ndi koipa. 17  Choncho ngati munthu akudziwa kuchita chabwino koma sakuchichita, akuchimwa.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “ziwalo zanu.”
Kapena kuti, “Anthu osakhulupirika inu.”