Kalata Yoyamba ya Petulo 5:1-14

  • Wetani gulu la nkhosa za Mulungu (1-4)

  • Mukhale odzichepetsa komanso atcheru (5-11)

    • Muzitula nkhawa zanu zonse kwa Mulungu (7)

    • Mdyerekezi ali ngati mkango wobangula (8)

  • Mawu omaliza (12-14)

5  Choncho, ine monga mkulu mnzanu, amene ndinaona mmene Khristu anavutikira komanso ndikuyembekezera kudzalandira nawo ulemerero umene udzaonekere,+ ndikupempha akulu amene ali pakati panu kuti: 2  Wetani gulu la nkhosa za Mulungu+ zomwe zili mʼmanja mwanu. Monga oyangʼanira, muzigwira ntchito yanu, osati mokakamizika koma mofunitsitsa monga atumiki a Mulungu.+ Muziigwira ndi mtima wonse, osati chifukwa chofuna kupindulapo kenakake.+ 3  Musamachite zinthu ngati mafumu pakati pa anthu a Mulungu,*+ koma muzipereka chitsanzo chabwino kwa gulu la nkhosa.+ 4  Ndipo mʼbusa wamkulu+ akadzaonekera, mudzalandira mphoto* yosawonongeka yomwe ndi yaulemerero.+ 5  Chimodzimodzinso inu achinyamata, muzigonjera amuna achikulire.*+ Komanso nonsenu muzichitirana zinthu modzichepetsa* chifukwa Mulungu sasangalala ndi anthu odzikuza. Koma anthu odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.+ 6  Choncho dzichepetseni pamaso pa Mulungu wathu wamphamvu* kuti adzakukwezeni nthawi yake ikadzakwana.+ 7  Muzichita zimenezi pamene mukumutulira nkhawa zanu zonse,+ chifukwa amakufunirani zabwino.+ 8  Khalanibe oganiza bwino ndipo khalani tcheru+ chifukwa mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda ngati mkango wobangula, kuti ameze winawake.*+ 9  Choncho mukhale ndi chikhulupiriro cholimba ndipo mulimbane naye,+ podziwa kuti abale anu padziko lonse akukumananso ndi mavuto ngati omwewo.+ 10  Mukavutika kwa nthawi yochepa, Mulungu yemwe amasonyeza kukoma mtima konse kwakukulu, amenenso anakuitanani kuti mukhale ogwirizana ndi Khristu komanso kuti mulandire ulemerero wosatha,+ adzamalizitsa kukuphunzitsani. Iye adzakupatsani mphamvu,+ adzakuthandizani kuti mukhalebe okhulupirika+ komanso adzakulimbitsani. 11  Mphamvu ndi zake mpaka muyaya. Ame. 12  Ndakulemberani kalata yachiduleyi kudzera mwa Silivano,*+ mʼbale amene ndikumuona kuti ndi wokhulupirika. Ndakulemberani zimenezi kuti ndikulimbikitseni ndi kukutsimikizirani kuti kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu nʼkumeneku, ndipo mukugwire mwamphamvu. 13  Mayi* amene ali ku Babulo, yemwe Mulungu anamusankha mwapadera ngati inuyo, komanso mwana wanga Maliko,+ akupereka moni. 14  Patsanani moni mwachikondi.* Nonse amene muli ogwirizana ndi Khristu, mukhale ndi mtendere.

Mawu a M'munsi

^ Kapena kuti, “pakati pa anthu omwe ndi cholowa cha Mulungu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “chipewa chachifumu chosawonongeka.”
^ Kapena kuti, “akulu.”
^ Kapena kuti, “muvale kudzichepetsa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “dzichepetseni pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu.”
^ Kapena kuti, “ngati mkango wobangula umene ukufunafuna winawake woti umumeze.”
^ Yemwe amadziwikanso kuti Sila.
^ Mawu akuti “mayi,” nʼkutheka kuti akutanthauza mpingo.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “popsopsonana mwachikondi.”