Numeri 3:1-51

  • Ana aamuna a Aroni (1-4)

  • Alevi anasankhidwa kuti azitumikira (5-39)

  • Kuwombola ana oyamba kubadwa (40-51)

3  Iyi ndi mbiri ya mbadwa za* Aroni ndi Mose pa nthawi imene Yehova analankhula ndi Mose mʼphiri la Sinai.+ 2  Mayina a ana a Aroni anali awa: woyamba Nadabu kenako Abihu,+ Eleazara+ ndi Itamara.+ 3  Ana a Aroni mayina awo anali amenewa. Iwo anali ansembe odzozedwa amene anaikidwa* kuti akhale ansembe.+ 4  Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamaso pa Yehova atapereka moto wosaloledwa kwa Yehova+ mʼchipululu cha Sinai, ndipo iwo anafa opanda ana. Pomwe Eleazara+ ndi Itamara+ anapitiriza kutumikira monga ansembe limodzi ndi Aroni bambo awo. 5  Kenako Yehova anauza Mose kuti: 6  “Itanitsa fuko la Levi+ ndipo uwapereke kwa wansembe Aroni kuti azimutumikira.+ 7  Iwo azikwaniritsa udindo wawo pomuthandiza komanso potumikira gulu lonse pa ntchito zapachihema chokumanako. 8  Azisamalira ziwiya zonse+ zapachihema chokumanako, komanso kukwaniritsa udindo wawo wotumikira Aisiraeli pogwira ntchito zapachihema.+ 9  Upereke Alevi kwa Aroni ndi ana ake. Amenewa ndi amene aperekedwa. Aperekedwa kwa iye kuchokera kwa Aisiraeli.+ 10  Uike Aroni ndi ana ake kuti akhale ansembe, ndipo azigwira ntchito zawo zaunsembe.+ Munthu wamba* aliyense amene wayandikira malowo, aziphedwa.”+ 11  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 12  “Ine ndasankha Alevi pakati pa Aisiraeli mʼmalo mwa ana onse oyamba kubadwa* a Aisiraeli+ ndipo Aleviwo adzakhala anga. 13  Mwana aliyense woyamba kubadwa ndi wanga.+ Pa tsiku limene ndinapha mwana aliyense woyamba kubadwa mʼdziko la Iguputo,+ ndinapatula mwana aliyense woyamba kubadwa pakati pa Aisiraeli kuti akhale wanga, kuyambira munthu mpaka chiweto.+ Amenewa azikhala anga. Ine ndine Yehova.” 14  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose mʼchipululu cha Sinai+ kuti: 15  “Uwerenge ana a Levi potengera nyumba ya makolo awo komanso mabanja awo. Uwerenge mwamuna aliyense kuyambira wa mwezi umodzi kupita mʼtsogolo.”+ 16  Choncho Mose anawerenga Aleviwo pomvera zimene Yehova anamulamula. 17  Mayina a ana a Levi anali awa: Gerisoni, Kohati ndi Merari.+ 18  Mayina a ana a Gerisoni, potengera mabanja awo ndi awa: Libini ndi Simeyi.+ 19  Ana a Kohati, potengera mabanja awo, anali Amuramu, Izara, Heburoni ndi Uziyeli.+ 20  Ana a Merari, potengera mabanja awo, anali Mali+ ndi Musi.+ Mabanja a Alevi anali amenewa potengera nyumba za makolo awo. 21  Mabanja a Alibini+ ndi Asimeyi anachokera mwa Gerisoni. Amenewa ndi amene anali mabanja a Agerisoni. 22  Amuna onse amene anawerengedwa kuyambira a mwezi umodzi kupita mʼtsogolo anakwana 7,500.+ 23  Mabanja a Agerisoni ankamanga misasa yawo kumbuyo kwa chihema,+ mbali yakumadzulo. 24  Mtsogoleri wa nyumba ya Agerisoni anali Eliyasafu, mwana wa Layeli. 25  Ntchito imene ana a Gerisoni+ anapatsidwa pachihema chokumanako inali yosamalira chihema+ ndi nsalu yoyala pachihemacho, nsalu yake yophimba,+ nsalu yotchinga pakhomo,+ 26  nsalu+ za mpanda wa bwalo, nsalu yotchinga+ pakhomo la bwalo lozungulira chihema ndi guwa lansembe, zingwe za chinsalu chake, komanso ntchito zonse zokhudza zinthu zimenezi. 27  Mabanja a Aamuramu, Aizara, Aheburoni ndi Auziyeli anachokera mwa Kohati.+ Amenewa ndi amene anali mabanja a Akohati. 28  Amuna onse amene anawerengedwa, kuyambira a mwezi umodzi kupita mʼtsogolo, analipo 8,600. Amenewa ntchito yawo inali kutumikira pamalo oyera.+ 29  Mabanja a ana a Kohati ankamanga msasa wawo kumʼmwera kwa chihema.+ 30  Mtsogoleri wa nyumba ya mabanja a Akohati anali Elizafana, mwana wa Uziyeli.+ 31  Ntchito yawo inali yosamalira likasa,+ tebulo,+ choikapo nyale,+ maguwa ansembe,+ ziwiya+ zimene ankagwiritsa ntchito potumikira mʼmalo oyerawo, nsalu yotchinga+ komanso ntchito zonse zokhudza zinthu zimenezi.+ 32  Mkulu wa atsogoleri onse a Alevi anali Eleazara,+ mwana wa wansembe Aroni. Iye ndi amene ankayangʼanira anthu onse amene ankatumikira pamalo oyera. 33  Mabanja a Amali ndi Amusi anachokera mwa Merari. Amenewa ndi amene anali mabanja a Amerari.+ 34  Amuna onse amene anawerengedwa, kuyambira a mwezi umodzi kupita mʼtsogolo analipo 6,200.+ 35  Mtsogoleri wa nyumba ya mabanja a Merari anali Zuriyeli, mwana wa Abihaili. Iwo ankamanga msasa wawo kumpoto kwa chihema.+ 36  Ntchito imene ana a Merari anapatsidwa inali yosamalira mafelemu+ a chihema, ndodo+ zake, zipilala+ zake, zitsulo zokhazikapo mafelemu ndi zipilala, ziwiya zake zonse+ ndi ntchito zonse zokhudza zinthu zimenezi.+ 37  Ankasamaliranso zipilala za mpanda wozungulira bwalo, zitsulo zokhazikapo zipilalazo+ komanso zikhomo ndi zingwe zake. 38  Amene ankamanga msasa wawo kumʼmawa kwa chihema, kumbali yotulukira dzuwa, anali Mose ndi Aroni, ndiponso ana a Aroni. Ntchito yawo inali kutumikira mʼmalo opatulika, mʼmalo mwa Aisiraeli. Munthu wamba aliyense* amene wayandikira malowo, ankayenera kuphedwa.+ 39  Amuna onse afuko la Levi amene Mose ndi Aroni anawawerenga, pomvera lamulo la Yehova analipo 22,000. Anawerenga amuna onse kuyambira a mwezi umodzi kupita mʼtsogolo potengera mabanja awo. 40  Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Uwerenge ana onse aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli, kuyambira a mwezi umodzi kupita mʼtsogolo+ ndipo ulembe mayina awo. 41  Unditengere Alevi kuti akhale anga mʼmalo mwa ana onse aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli.+ Unditengerenso ziweto zonse za Alevi mʼmalo mwa ziweto zonse zoyamba kubadwa za Aisiraeli.+ Ine ndine Yehova.” 42  Mose anawerenga ana onse aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli, mogwirizana ndi zimene Yehova anamulamula. 43  Ana onse aamuna oyamba kubadwa amene anawawerenga, kuyambira a mwezi umodzi kupita mʼtsogolo, anakwana 22,273. 44  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 45  “Utenge Alevi mʼmalo mwa ana onse aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli. Utengenso ziweto za Alevi mʼmalo mwa ziweto za Aisiraeli. Aleviwo akuyenera kukhala anga. Ine ndine Yehova. 46  Monga dipo*+ la ana aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli okwana 273 omwe apitirira chiwerengero cha Alevi,+ 47  utenge masekeli* 5 pa munthu aliyense,+ mogwirizana ndi muyezo wa sekeli yakumalo oyera.* Sekeli imodzi ndi yokwana magera* 20.+ 48  Ndalamazo uzipereke kwa Aroni ndi ana ake. Zikhale dipo* lowombolera Aisiraeli amene apitirira chiwerengero cha Alevi.” 49  Choncho Mose analandira ndalama zowombolera Aisiraeli amene chiwerengero chawo chinaposa cha Alevi. 50  Kwa ana aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli, analandira ndalama zokwana masekeli 1,365, mogwirizana ndi muyezo wa sekeli yakumalo oyera. 51  Ndiyeno Mose anapereka ndalama za dipozo kwa Aroni ndi ana ake pomvera mawu a Yehova, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.

Mawu a M'munsi

^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mibadwo ya.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amene manja awo anadzazidwa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Mlendo,” kutanthauza mwamuna amene si wa mʼbanja la Aroni.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ana onse oyamba kubadwa, otsegula mimba ya mayi awo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Mlendo aliyense,” kutanthauza munthu amene si Mlevi.
^ Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.
^ Kapena kuti, “mogwirizana ndi sekeli yoyera.”
^ Gera imodzi inali yofanana ndi magalamu 0.57. Onani Zakumapeto B14.