Miyambo 9:1-18

  • Nzeru yeniyeni ikuitana (1-12)

    • “Chifukwa ine ndidzachulukitsa masiku a moyo wako” (11)

  • Mkazi wopusa akuitana (13-18)

    • “Madzi akuba amatsekemera” (17)

9  Nzeru yeniyeni yamanga nyumba yake.Yasema zipilala zake 7.   Yakonza bwinobwino nyama yake,*Yasakaniza vinyo wake.Yayalanso patebulo pake.   Yatuma antchito ake aakaziKuti apite pamalo okwera amumzinda kukaitana anthu kuti:+   “Aliyense wosadziwa zinthu abwere kuno.” Aliyense wopanda nzeru, nzeru ikumuuza kuti:   “Bwera udzadye chakudya changaNdipo udzamwe nawo vinyo amene ndasakaniza.   Leka kukhala munthu wosadziwa zinthu kuti upitirize kukhala ndi moyo.+Lola kuti kumvetsa zinthu kukutsogolere.”+   Amene amalangiza wonyoza amachititsidwa manyazi,+Ndipo aliyense wodzudzula woipa adzavulazidwa.   Usadzudzule wonyoza chifukwa angadane nawe.+ Dzudzula munthu wanzeru ndipo adzakukonda.+   Pereka malangizo kwa munthu wanzeru ndipo adzawonjezera nzeru zake.+ Phunzitsa munthu wolungama ndipo adzapitiriza kuphunzira. 10  Kuopa Yehova ndi chiyambi cha nzeru,+Ndipo ngati ungadziwe Mulungu, yemwe ndi Woyera Koposa,+ udzakhala womvetsa zinthu. 11  Chifukwa ine ndidzachulukitsa masiku a moyo wako,+Ndipo ndidzawonjezera zaka za moyo wako. 12  Ukakhala wanzeru, iweyo ndi amene umapindula ndi nzeruzo,Koma ngati ndiwe wonyoza, iweyo ndi amene udzavutike. 13  Mkazi wopusa amakhala wolongolola.+ Iye ndi woperewera nzeru ndipo sadziwa chilichonse. 14  Amakhala pampando pakhomo la nyumba yakePamalo okwera amumzinda,+ 15  Nʼkumaitana anthu odutsaAmene akungodziyendera panjira kuti: 16  “Aliyense amene ali wosadziwa zinthu abwere kuno.” Aliyense wopanda nzeru, mkaziyo akumuuza kuti:+ 17  “Madzi akuba amatsekemera,Ndipo chakudya chodya mobisa chimakoma.”+ 18  Koma mwamunayo sakudziwa kuti kumeneko kuli akufa,Ndiponso kuti alendo a mkaziyo ali mʼdzenje la Manda.*+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Yapha nyama yake.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.