Miyambo 30:1-33

 • MAWU A AGURI (1-33)

  • Musandipatse umphawi kapena chuma (8)

  • Zinthu zimene sizikhuta (15, 16)

  • Zinthu zimene njira zake sizidziwika (18, 19)

  • Mkazi wachigololo (20)

  • Nyama ndi zanzeru mwachibadwa (24)

30  Uwu ndi uthenga wamphamvu womwe Aguri mwana wa Yake analankhula ndi Itiyeli komanso Ukali.   Ine sindidziwa zambiri poyerekeza ndi anthu ena onse,+Ndipo sinditha kumvetsa zinthu ngati mmene anthu ena amachitira.   Ine sindinaphunzire zinthu zanzeru,Ndipo sindidziwa zinthu zimene Woyera Koposa amadziwa.   Ndi ndani amene anakwerapo kumwamba kenako nʼkutsika?+ Ndi ndani amene anasonkhanitsapo mphepo mʼmanja mwake? Ndi ndani amene anamangapo madzi pachovala chake?+ Ndi ndani amene anaika malire a dziko lapansi?+ Dzina lake ndi ndani, nanga mwana wake dzina lake ndi ndani? Ndiuzeni ngati mukudziwa.   Mawu onse a Mulungu ndi oyengeka.+ Iye ndi chishango kwa onse amene amathawira kwa iye.+   Usawonjezere kanthu pa mawu ake+Kuti angakudzudzule,Nʼkuoneka kuti ndiwe wabodza.   Ndikukupemphani zinthu ziwiri. Mundipatse zinthu zimenezi ndisanafe.   Zinthu zabodza komanso mawu onama muziike kutali ndi ine.+ Musandipatse umphawi kapena chuma. Mungondipatsa chakudya chokwanira,+   Kuti ndisakhute kwambiri nʼkukukanani kuti: “Kodi Yehova ndi ndani?”+ Ndiponso kuti ndisasauke nʼkukaba ndi kuchititsa kuti dzina la Mulungu wanga linyozedwe. 10  Usanenere wantchito zoipa kwa bwana wake,Kuti angakutemberere ndipo ungapezeke wolakwa.+ 11  Pali mʼbadwo umene umatemberera bambo awoKomanso umene sudalitsa mayi awo.+ 12  Pali mʼbadwo umene umadziona kuti ndi woyera+Koma sunayeretsedwe ku zonyansa zake.* 13  Pali mʼbadwo umene maso ake ndi onyadaNdiponso umene maso ake amayangʼana modzikweza.+ 14  Pali mʼbadwo umene mano ake ndi malupangaNdiponso umene nsagwada zake ndi mipeni yophera nyama.Mʼbadwowo umapondereza anthu ovutika apadziko lapansiKomanso osauka pakati pa anthu.+ 15  Misundu* ili ndi ana aakazi awiri amene amafuula kuti, “Tipatseni! Tipatseni!” Pali zinthu zitatu zimene sizikhutaNdiponso zinthu 4 zimene sizinena kuti, “Ndakhuta!” Zinthu zake ndi izi: 16  Manda,*+ mimba yosabereka,Nthaka yopanda madziKomanso moto umene sunena kuti, “Ndakhuta!” 17  Munthu amene amanyoza bambo ake ndiponso amene samvera mayi ake,+Akhwangwala akuchigwa* adzakolowola diso lakeNdipo ana a chiwombankhanga adzalidya.+ 18  Pali zinthu zitatu zimene nʼzodabwitsa kwambiri kwa ine,Ndiponso zinthu 4 zimene sindizimvetsa. Zinthu zake ndi izi: 19  Njira ya chiwombankhanga mumlengalenga,Njira ya njoka pamwala,Njira ya sitima pakatikati pa nyanja,Ndiponso njira ya mwamuna ndi mtsikana. 20  Zimene mkazi wachigololo amachita ndi izi: Iye amadya nʼkupukuta pakamwa pakeKenako amanena kuti, “Sindinachite cholakwa chilichonse.”+ 21  Pali zinthu zitatu zimene zimagwedeza dziko lapansiNdiponso zinthu 4 zimene dziko lapansi silitha kuzipirira. Zinthu zake ndi izi: 22  Kapolo akamalamulira monga mfumu,+Munthu wopusa akamadya kwambiri, 23  Mkazi amene amadedwa* akakwatiwa,Komanso mtsikana wantchito akatenga malo a abwana ake aakazi.+ 24  Pali zinthu 4 zomwe zili mʼgulu la zinthu zingʼonozingʼono kwambiri padziko lapansiKoma ndi zanzeru mwachibadwa.* Zinthu zake ndi izi:+ 25  Nyerere si zamphamvu,Koma zimasonkhanitsa chakudya chawo mʼchilimwe.+ 26  Mbira+ si nyama zamphamvuKoma zimamanga nyumba zawo pathanthwe.+ 27  Dzombe+ lilibe mfumuKoma limauluka lonse litagawikana mʼmagulumagulu.+ 28  Nalimata+ amagwira zinthu ndi mapazi akeNdipo amalowa mʼnyumba yachifumu. 29  Pali zinthu zitatu zimene zimayenda mochititsa chidwiNdiponso zinthu 4 zimene zimasangalatsa zikamayenda. Zinthu zake ndi izi: 30  Mkango umene ndi wamphamvu kwambiri panyama zonse zakutchireNdiponso umene suopa chilichonse nʼkubwerera mʼmbuyo,+ 31  Galu wosaka kapena mbuzi yamphongo,Ndiponso mfumu imene ili limodzi ndi asilikali ake. 32  Ngati wachita zinthu zopusa nʼkudzikweza,+Kapena ngati ukufuna kuchita zimenezo,Gwira pakamwa pako.+ 33  Chifukwa mkaka ukaukhutchumula umatulutsa mafuta,Mphuno ukaifinya imatulutsa magazi,Ndipo kukolezera mkwiyo kumayambitsa mkangano.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “ku ndowe zake.”
“Msundu” ndi mtundu wa nyongolotsi zimene zimakhala mʼmadzi ndipo zimaluma anthu kapena zinyama nʼkumayamwa magazi.
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “akukhwawa.”
Kapena kuti, “sakondedwa.”
Kapena kuti, “ndi zanzeru kwambiri.”