Miyambo 6:1-35

  • Kukhala wosamala pa nkhani yolonjeza kubweza ngongole ya wina (1-5)

  • “Pita kwa nyerere waulesi iwe” (6-11)

  • Munthu wopanda nzeru komanso woipa (12-15)

  • Zinthu 7 zimene Yehova amadana nazo (16-19)

  • Samalani ndi mkazi wamakhalidwe oipa (20-35)

6  Mwana wanga, ngati walonjeza kuti udzapereka ngongole ya mnzako iye akadzalephera kubweza,+Ngati wagwirana dzanja ndi mlendo pochita mgwirizano,+   Ngati wakodwa ndi lonjezo limene unapanga,Ngati wagwidwa ndi mawu amʼkamwa mwako,+   Uchite izi mwana wanga kuti udzipulumutse,Chifukwa uli mʼmanja mwa mnzako: Pita ukadzichepetse ndipo ukamuchonderere kwambiri mnzakoyo.+   Usalole kuti maso ako agone,Kapena kuti zikope zako ziwodzere.   Dzipulumutse ngati insa mʼmanja mwa wosaka,Ndiponso ngati mbalame mʼmanja mwa wosaka mbalame.   Pita kwa nyerere waulesi iwe,+Ukaone mmene imachitira zinthu kuti ukhale wanzeru.   Ngakhale kuti ilibe mtsogoleri, kapitawo, kapena wolamulira,   Imakonza chakudya chake mʼchilimwe,+Ndipo imasonkhanitsa chakudya chake pa nthawi yokolola.   Kodi waulesi iwe, ugona pamenepo mpaka liti? Kodi udzuka nthawi yanji kutulo tako? 10  Ukapitiriza kugona pangʼono, ukapitiriza katulo pangʼono,Ukapitiriza kupinda manja pangʼono kuti upume,+ 11  Umphawi wako udzabwera ngati wachifwamba,Ndipo kusauka kwako kudzabwera ngati munthu wokhala ndi zida.+ 12  Munthu wopanda pake komanso woipa, amangoyendayenda nʼkumalankhula mabodza.+ 13  Amatsinzinira ena diso lake,+ amachita zizindikiro ndi phazi lake ndiponso amachita zizindikiro ndi zala zake. 14  Popeza mtima wake ndi wachinyengo,Nthawi zonse amakonza ziwembu+ komanso amakhalira kuyambanitsa anthu.+ 15  Choncho tsoka lake lidzabwera mwadzidzidzi.Adzathyoledwa modzidzimutsa moti sadzachira.+ 16  Pali zinthu 6 zimene Yehova amadana nazo.Zilipo zinthu 7 zimene amanyansidwa nazo: 17  Maso odzikweza,+ lilime lonama,+ manja amene amakhetsa magazi a anthu osalakwa,+ 18  Mtima umene umakonza ziwembu,+ mapazi othamangira kukachita zoipa, 19  Mboni yachinyengo imene nthawi zonse imanena mabodza,+Komanso aliyense amene amayambitsa mikangano pakati pa abale.+ 20  Mwana wanga, uzitsatira malamulo a bambo ako,Ndipo usasiye kutsatira malangizo* a mayi ako.+ 21  Uwamange pamtima pako nthawi zonseNdipo uwamange mʼkhosi mwako. 22  Ukamayenda adzakutsogolera.Ukamagona adzakulondera.Ndipo ukadzuka, adzakuuza zochita.* 23  Chifukwa lamulolo ndi nyale,+Ndipo malangizo ndi kuwala,+Komanso kudzudzula kumene kumathandiza munthu kusintha ndi njira yakumoyo.+ 24  Zidzakuteteza kwa mkazi woipa,+Komanso ku lilime lokopa la mkazi wachiwerewere.*+ 25  Usasirire kukongola kwake mumtima mwako.+Kapena kulola kuti ukopeke ndi maso ake achikoka, 26  Munthu amafika potsala ndi mkate umodzi wokha chifukwa cha hule,+Koma mkazi wa mwini amasaka moyo wako wamtengo wapatali. 27  Kodi munthu anganyamule makala a moto pachifuwa pake, zovala zake osapsa?+ 28  Kapena kodi munthu angayende pamakala a moto, mapazi ake osapsa? 29  Nʼchimodzimodzi ndi aliyense wogona ndi mkazi wa mnzake.Aliyense wokhudza mkaziyo adzalangidwa.+ 30  Anthu sanyoza munthu wakubaNgati waba kuti apeze chakudya pamene ali ndi njala. 31  Koma akapezeka, adzabweza zinthuzo kuwirikiza ka 7.Adzapereka zinthu zonse zamtengo wapatali zamʼnyumba mwake.+ 32  Aliyense wochita chigololo ndi mkazi ndi wopanda nzeru.*Amene amachita zimenezi amadzibweretsera mavuto aakulu pa moyo wake.+ 33  Adzangodzivulaza yekha ndipo anthu adzamunyoza,+Moti kunyozeka kwake sikudzafufutika.+ 34  Chifukwa nsanje imachititsa kuti mwamuna wake akwiye kwambiri.Pomubwezera sadzamva chisoni.+ 35  Iye sadzavomera chipukuta misozi chilichonse,*Ndipo sadzapepeseka ngakhale utapereka mphatso yaikulu bwanji.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “malamulo.”
Kapena kuti, “adzakupatsa malangizo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wachilendo.”
Kapena kuti, “ali ndi zolinga zoipa.”
Kapena kuti, “sadzavomera dipo lililonse.”