Miyambo 27:1-27

  • Kudzudzulidwa ndi mnzako nʼkothandiza (5, 6)

  • Mwana wanga sangalatsa mtima wanga (11)

  • Chitsulo chimanola chitsulo chinzake (17)

  • Uzidziwa bwino ziweto zako (23)

  • Chuma sichikhalitsa (24)

27  Usadzitame ndi zimene udzachite mawaChifukwa sukudziwa zimene zidzachitike mawa.*+   Munthu wina* akutamande, osati pakamwa pako.Anthu ena* akutamande, osati milomo yako.+   Mwala umalemera ndiponso mchenga umalemera,Koma mavuto ochititsidwa ndi munthu wopusa amalemera kwambiri kuposa zonsezi.+   Mkwiyo ndi wankhanza ndipo umawononga ngati madzi osefukira,Koma nsanje ndi ndani angaipirire?+   Kudzudzula munthu mosabisa mawu nʼkwabwino kusiyana ndi kumukonda koma osamusonyeza chikondicho.+   Mabala ovulazidwa ndi mnzako amakhala okhulupirika,+Koma makisi a munthu* amene amadana nawe amakhala ambiri.*   Munthu akakhuta amakana kudya* uchi wakuchisa,Koma kwa munthu wanjala, ngakhale chinthu chowawa chimatsekemera.   Mofanana ndi mbalame imene yasochera* pachisa pake,Ndi mmenenso alili munthu amene wasochera kunyumba kwake.   Mafuta ndi zofukiza zonunkhira nʼzimene zimasangalatsa mtima.Chimodzimodzinso kukhala ndi mnzako wabwino amene amakupatsa malangizo mosapita mʼmbali.+ 10  Usasiye mnzako kapena mnzawo wa bambo ako,Ndipo usalowe mʼnyumba ya mchimwene wako pa tsiku limene tsoka lakugwera.Munthu woyandikana naye nyumba amene ali pafupi ali bwino kuposa mchimwene wako amene ali kutali.+ 11  Mwana wanga, khala wanzeru ndipo usangalatse mtima wanga,+Kuti ndimuyankhe amene amanditonza.+ 12  Munthu wochenjera akaona tsoka amabisala,+Koma wosadziwa zinthu amangopitabe ndipo amakumana ndi mavuto. 13  Ngati munthu walonjeza kuti akhala chikole kwa mlendo, umulande chovala chake.Komanso umulande chikole ngati walonjeza zimenezi kwa mkazi wachilendo.+ 14  Munthu akapereka moni kwa mnzake* mokuwa mʼmamawa kwambiri,Mnzakeyo sangasangalale nazo.* 15  Mkazi wolongolola* ali ngati denga limene limadontha nthawi zonse pa tsiku la mvula.+ 16  Amene angakwanitse kumuletsa angathenso kuimitsa mphepoNdipo angathe kugwira mafuta ndi dzanja lake lamanja. 17  Chitsulo chimanola chitsulo chinzake.Chimodzimodzinso munthu amanola munthu mnzake.*+ 18  Amene amasamalira mtengo wa mkuyu adzadya zipatso zake,+Ndipo amene amasamalira mbuye wake adzalemekezedwa.+ 19  Chithunzi cha nkhope ya munthu chimaonekera mʼmadzi,Mofanana ndi zimenezi, mtima wa munthu umaonekera mumtima wa munthu wina. 20  Manda ndiponso malo achiwonongeko* sakhuta,+Nawonso maso a munthu sakhuta. 21  Siliva amamuyengera mʼmbiya yoyengera ndipo golide amamuyengera mungʼanjo,+Mofanana ndi zimenezi munthu amayesedwa ndi zimene anthu akunena pomutamanda.* 22  Ngakhale utasinja chitsiru ndi musiNgati mmene umasinjira mbewu mumtondo,Uchitsiru wake sungachichokere. 23  Uyenera kudziwa bwino maonekedwe a ziweto zako. Uzisamalira bwino* nkhosa zako,+ 24  Chifukwa chuma sichidzakhalapo mpaka kalekale+Komanso chisoti chachifumu sichidzakhalapo ku mibadwo yonse. 25  Udzu wobiriwira umapita ndipo udzu watsopano umaonekera,Komanso zomera zamʼmapiri zimasonkhanitsidwa. 26  Nkhosa zamphongo zazingʼono zimakupezetsa zovala,Ndipo mbuzi zamphongo ndi malipiro ogulira munda. 27  Udzakhala ndi mkaka wa mbuzi wokwanira woti udye,Woti udyetse banja lako komanso atsikana ako antchito.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “sukudziwa kuti tsiku libala chiyani.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mlendo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Anthu ochokera kudziko lina.”
Kapena kuti, “kupsompsona kwa munthu.”
Mabaibulo ena amati, “osachokera pansi pa mtima.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amapondaponda.”
Kapena kuti, “ikuthawa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “akadalitsa mnzake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “angaone ngati akumutemberera.”
Kapena kuti, “wokonda kudandaula.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nkhope ya mnzake.”
Kapena kuti, “Abadoni.”
Kapena kuti, “munthu amasonyeza mmene alili anthu akamamutamanda.”
Kapena kuti, “Uziika mtima wako pa; Uziyangʼanira.”