Miyambo 2:1-22

  • Ubwino wa nzeru (1-22)

    • Ufunefune nzeru ngati chuma chobisika (4)

    • Kuganiza bwino kumateteza (11)

    • Khalidwe lachiwerewere limabweretsa mavuto (16-19)

2  Mwana wanga, ukamvera mawu angaNdi kusunga malamulo anga+ ngati chuma chamtengo wapatali,   Potchera khutu lako kuti umvetsere mawu anzeru+Ndiponso kutsegula mtima wako kuti ukhale wozindikira,+   Komanso ukapempha kuti ukhale womvetsa zinthu+Ndi kuchonderera kuti ukhale wozindikira,+   Ukapitiriza kuzifunafuna ngati siliva,+Ndi kuzifufuza ngati chuma chobisika,+   Udzamvetsa tanthauzo la kuopa Yehova+Ndipo udzamudziwadi Mulungu.+   Chifukwa Yehova ndi amene amapereka nzeru.+Kudziwa zinthu komanso kuzindikira zimatuluka mʼkamwa mwake.   Anthu owongoka mtima, amawasungira nzeru zopindulitsa.Iye ndi chishango kwa anthu amene amachita zinthu mokhulupirika.+   Amayangʼanira njira za anthu amene amachita zachilungamo,Ndipo adzateteza njira ya anthu ake okhulupirika.+   Ukachita zimenezi udzamvetsa zinthu zolungama, zolondola komanso zabwino.Udzamvetsa njira yabwino yoyenera kuyendamo.+ 10  Nzeru zikalowa mumtima mwako,+Ndipo kudziwa zinthu kukakhala kosangalatsa kwa iwe,+ 11  Kuganiza bwino kudzakuyangʼanira,+Ndipo kuzindikira kudzakuteteza, 12  Kuti zikupulumutse kunjira yoipa,Komanso kwa munthu wolankhula zinthu zopotoka,+ 13  Kwa anthu amene amasiya njira zowongokaKuti ayende mʼnjira zamdima.+ 14  Zidzakupulumutsanso kwa anthu amene amasangalala akamachita zoipa,Amene amakondwera ndi zinthu zoipa komanso zachinyengo, 15  Amene njira zawo ndi zokhotaNdiponso amene zochita zawo zonse ndi zachinyengo. 16  Nzeru zidzakupulumutsa kwa mkazi wamakhalidwe oipa.*Zidzakupulumutsa ku mawu okopa a mkazi wachiwerewere,*+ 17  Amene amasiya mnzake wapamtima* wapachitsikana chake+Ndiponso amene amaiwala pangano limene anachita ndi Mulungu wake. 18  Chifukwa kupita kunyumba yake kuli ngati kupita kokafa,Ndipo njira yopita kunyumba yake ndi njira yakumanda.+ 19  Onse ogona naye* sadzabwereraNdipo sadzapezanso njira zopita kumoyo.+ 20  Choncho uziyenda mʼnjira za anthu abwinoNdipo upitirize kuyenda mʼnjira za anthu olungama,+ 21  Chifukwa owongoka mtima okha ndi amene adzakhale padziko lapansi,Ndipo opanda cholakwa* ndi amene adzatsalemo.+ 22  Koma anthu oipa adzachotsedwa padziko lapansi+Ndipo achinyengo adzazulidwamo.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “wachilendo.” Kutanthauza munthu amene amachita makhalidwe amene sasangalatsa Mulungu.
Mʼchilankhulo choyambirira, “wachilendo.” Kutanthauza munthu amene ndi wotalikirana ndi Mulungu chifukwa cha makhalidwe ake oipa.
Kapena kuti, “amasiya mwamuna wake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene amapita kwa iye.”
Kapena kuti, “amene amachita zinthu mokhulupirika.”