Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Buku la Miyambo

Machaputala

Mitu

 • 1

  • Cholinga cha miyambo (1-7)

  • Kuopsa kocheza ndi anthu amakhalidwe oipa (8-19)

  • Nzeru yeniyeni ikufuula mokweza mʼmabwalo (20-33)

 • 2

  • Ubwino wa nzeru (1-22)

   • Ufunefune nzeru ngati chuma chobisika (4)

   • Kuganiza bwino kumateteza (11)

   • Khalidwe lachiwerewere limabweretsa mavuto (16-19)

 • 3

  • Kukhala wanzeru komanso kudalira Yehova (1-12)

   • Kulemekeza Yehova pogwiritsa ntchito zinthu zamtengo wapatali (9)

  • Nzeru zimathandiza munthu kuti azisangalala (13-18)

  • Nzeru zimateteza (19-26)

  • Kuchitira ena zinthu zabwino (27-35)

   • Kuthandiza ena ngati tingathe (27)

 • 4

  • Malangizo anzeru a bambo (1-27)

   • Kuposa zonse, peza nzeru (7)

   • Kupewa njira zoipa (14, 15)

   • Njira ya wolungama imapitiriza kuwala (18)

   • “Uteteze mtima wako” (23)

 • 5

  • Chenjezo lokhudza akazi amakhalidwe oipa (1-14)

  • Sangalala ndi mkazi wako (15-23)

 • 6

  • Kukhala wosamala pa nkhani yolonjeza kubweza ngongole ya wina (1-5)

  • “Pita kwa nyerere waulesi iwe” (6-11)

  • Munthu wopanda nzeru komanso woipa (12-15)

  • Zinthu 7 zimene Yehova amadana nazo (16-19)

  • Samalani ndi mkazi wamakhalidwe oipa (20-35)

 • 7

  • Mverani malamulo a Mulungu kuti mukhale ndi moyo (1-5)

  • Mnyamata wosadziwa zinthu anakopedwa (6-27)

   • “Ngati ngʼombe yamphongo imene ikupita kukaphedwa” (22)

 • 8

  • Nzeru ikulankhula ngati munthu (1-36)

   • ‘Ine ndine woyamba kulengedwa ndi Mulungu’ (22)

   • ‘Ndinali pambali pake monga mmisiri waluso’  (30)

   • ‘Ndinkasangalala ndi ana a anthu’ (31)

 • 9

  • Nzeru yeniyeni ikuitana (1-12)

   • “Chifukwa ine ndidzachulukitsa masiku a moyo wako” (11)

  • Mkazi wopusa akuitana (13-18)

   • “Madzi akuba amatsekemera” (17)

 • MIYAMBI YA SOLOMO (10:1–24:34)

  • 10

   • Mwana wanzeru amasangalatsa bambo ake (1)

   • Wogwira ntchito mwakhama adzalemera (4)

   • Mawu akachuluka sipalephera kukhala zolakwika (19)

   • Madalitso a Yehova ndi amene amalemeretsa (22)

   • Kuopa Yehova kumatalikitsa moyo (27)

  • 11

   • Anthu odzichepetsa ndi amene ali ndi nzeru (2)

   • Wampatuko amawononga anthu ena (9)

   • “Zinthu zimayenda bwino ngati pali alangizi ambiri” (14)

   • Munthu wopereka mowolowa manja zinthu zidzamuyendera bwino (25)

   • Munthu amene amadalira chuma chake adzakumana ndi mavuto (28)

  • 12

   • Amene amadana ndi kudzudzulidwa ndi wosaganiza bwino (1)

   • “Mawu a munthu amene amalankhula asanaganize amalasa ngati lupanga” (18)

   • Amene amalimbikitsa mtendere amasangalala (20)

   • Milomo yonama imamunyansa Yehova (22)

   • Nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauweramitsa (25)

  • 13

   • Anthu amene amapempha malangizo amakhala ndi nzeru (10)

   • Chimene umayembekezera chikalephereka, mtima umadwala (12)

   • Nthumwi yokhulupirika imachiritsa (17)

   • Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru (20)

   • Chilango chimasonyeza chikondi (24)

  • 14

   • Ngati munthu mtima ukumupweteka amadziwa yekha (10)

   • Njira imene imaoneka ngati yabwino ikhoza kubweretsa imfa (12)

   • Munthu amene sadziwa zambiri amakhulupirira mawu alionse (15)

   • Munthu wolemera amakhala ndi anzake ambiri (20)

   • Mtima wodekha umapangitsa kuti thupi likhale lathanzi (30)

  • 15

   • Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo (1)

   • Maso a Yehova ali paliponse (3)

   • Pemphero la munthu wowongoka mtima limasangalatsa Mulungu (8)

   • Mapulani sakwaniritsidwa ngati anthu sakambirana (22)

   • Kuyamba waganiza usanayankhe (28)

  • 16

   • Yehova amafufuza zolinga zathu (2)

   • Zochita zako zonse uzisiye mʼmanja mwa Yehova (3)

   • Masikelo achilungamo ndi ochokera kwa Yehova (11)

   • Kunyada kumachititsa kuti munthu awonongeke (18)

   • Imvi ndi chisoti chachifumu cha ulemerero (31)

  • 17

   • Usabwezere zoipa mʼmalo mwa zabwino (13)

   • Mkangano usanabuke, chokapo (14)

   • Mnzako weniweni amakusonyeza chikondi nthawi zonse (17)

   • “Mtima wosangalala uli ngati mankhwala amene amachiritsa” (22)

   • Munthu wozindikira amapitiriza kukhala wodekha (27)

  • 18

   • Kudzipatula ndi kudzikonda komanso kupanda nzeru (1)

   • Dzina la Yehova ndi nsanja yolimba (10)

   • Chuma chili ngati chitetezo mʼmaganizo mwa munthu (11)

   • Ubwino womvetsera mbali zonse (17)

   • Mnzako amakhala nawe pafupi kuposa mʼbale wako (24)

  • 19

   • Kuzindikira kumachititsa kuti munthu abweze mkwiyo wake (11)

   • Mkazi wolongolola ali ngati denga lodontha (13)

   • Mkazi wanzeru amachokera kwa Yehova (14)

   • Langa mwana wako padakali chiyembekezo (18)

   • Ubwino womvetsera malangizo (20)

  • 20

   • Womwa vinyo wambiri amayamba kunyoza (1)

   • Waulesi salima nthawi yozizira (4)

   • Maganizo amumtima mwa munthu ali ngati madzi akuya (5)

   • Chenjezo pa nkhani yolumbira usanaganize bwino (25)

   • Ulemerero wa anyamata ndi mphamvu zawo (29)

  • 21

   • Yehova amatsogolera mtima wa mfumu (1)

   • Kuchita zinthu zachilungamo nʼkwabwino kuposa kupereka nsembe (3)

   • Khama limapindulitsa (5)

   • Amene samvetsera munthu wonyozeka nayenso sadzamvetseredwa (13)

   • Palibe nzeru zotsutsana ndi Yehova (30)

  • 22

   • Ndi bwino kusankha dzina labwino kusiyana ndi chuma chochuluka (1)

   • Ukaphunzitsa mwana zimamuyendera moyo wake wonse (6)

   • Munthu waulesi amanena kuti panja pali mkango (13)

   • Chilango chimachotsa uchitsiru (15)

   • Munthu waluso pa ntchito yake amatumikira mafumu (29)

  • 23

   • Muzichita zinthu mozindikira akakuitanirani chakudya (2)

   • Musamafunefune chuma (4)

   • Chuma chikhoza kuuluka nʼkupita kutali (5)

   • Usakhale mʼgulu la zidakwa (20)

   • Mowa umaluma ngati njoka (32)

  • 24

   • Usachitire nsanje anthu oipa (1)

   • Nzeru zimamanga nyumba ya munthu (3)

   • Munthu wolungama angagwe koma adzadzukanso (16)

   • Musamabwezere (29)

   • Kugona kumabweretsa umphawi (33, 34)

 • MIYAMBI INA YA SOLOMO IMENE ATUMIKI A MFUMU HEZEKIYA ANAKOPERA (25:1–29:27)

  • 25

   • Kusunga chinsinsi (9)

   • Mawu osankhidwa bwino (11)

   • Osamapitapita kunyumba kwa mnzako (17)

   • Kuunjika makala amoto pamutu pa mdani (21, 22)

   • Nkhani yabwino ili ngati madzi ozizira (25)

  • 26

   • Zimene anthu aulesi amachita (13-16)

   • Usamalowerere mkangano wa anthu ena (17)

   • Kupewa nthabwala zopusitsa ena (18, 19)

   • Ngati palibe nkhuni moto umazima (20, 21)

   • Mawu a munthu wonenera ena zoipa ali ngati chakudya chokoma (22)

  • 27

   • Kudzudzulidwa ndi mnzako nʼkothandiza (5, 6)

   • Mwana wanga sangalatsa mtima wanga (11)

   • Chitsulo chimanola chitsulo chinzake (17)

   • Uzidziwa bwino ziweto zako (23)

   • Chuma sichikhalitsa (24)

  • 28

   • Pemphero la munthu wosamvera ndi lonyansa (9)

   • Munthu woulula machimo ake amachitiridwa chifundo (13)

   • Amene amafuna kulemera mofulumira sadzalephera kukhala wolakwa (20)

   • Kudzudzula munthu kuli bwino kuposa kuyamikira mwachinyengo (23)

   • Munthu amene amapereka zinthu sadzasowa kanthu (27)

  • 29

   • Mwana womulekerera amachititsa manyazi (15)

   • Ngati anthu sakutsogoleredwa amachita zinthu motayirira (18)

   • Munthu wosachedwa kukwiya amayambitsa mkangano (22)

   • Munthu wodzichepetsa adzapeza ulemerero (23)

   • Kuopa anthu ndi msampha (25)

 • 30

  • MAWU A AGURI (1-33)

   • Musandipatse umphawi kapena chuma (8)

   • Zinthu zimene sizikhuta (15, 16)

   • Zinthu zimene njira zake sizidziwika (18, 19)

   • Mkazi wachigololo (20)

   • Nyama ndi zanzeru mwachibadwa (24)

 • 31

  • MAWU A MFUMU LEMUELI (1-31)

   • Ndani amene angapeze mkazi wamakhalidwe abwino? (10)

   • Amagwira ntchito mwakhama (17)

   • Kukoma mtima kuli palilime lake (26)

   • Ana ndi mwamuna wake amamutamanda (28)

   • Kuoneka bwino komanso kukongola sikuchedwa kutha (30)