Miyambo 19:1-29

  • Kuzindikira kumachititsa kuti munthu abweze mkwiyo wake (11)

  • Mkazi wolongolola ali ngati denga lodontha (13)

  • Mkazi wanzeru amachokera kwa Yehova (14)

  • Langa mwana wako padakali chiyembekezo (18)

  • Ubwino womvetsera malangizo (20)

19  Ndi bwino kukhala wosauka nʼkumachita zinthu mokhulupirika+Kusiyana nʼkukhala munthu wopusa nʼkumalankhula mabodza.+  2  Munthu wosadziwa zinthu si wabwino,+Ndipo amene amachita zinthu mopupuluma* akuchimwa.  3  Kupusa kwa munthu nʼkumene kumapotoza njira yake,Ndipo mtima wake umakwiyira Yehova.  4  Chuma chimachititsa kuti munthu akhale ndi anzake ambiri,Koma munthu wosauka amasiyidwa ngakhale ndi mnzake weniweni.+  5  Mboni yonama sidzalephera kulangidwa,+Ndipo amene amalankhula zabodza zokhazokha sadzathawa chilango.+  6  Anthu ambiri amafuna kukondedwa ndi munthu wolemekezeka,*Ndipo aliyense ndi bwenzi la munthu wopereka mphatso.  7  Abale ake onse a munthu wosauka amadana naye,+Kuwonjezera pamenepo anzake amamupewa,+ Iye amawachonderera kuti amuthandize, koma palibe amene amamuyankha.  8  Munthu amene wapeza nzeru amakonda moyo wake.+ Amene amaona kuti kukhala wozindikira nʼkofunika kwambiri zinthu zidzamuyendera bwino.+  9  Mboni yonama sidzalephera kulangidwa,Ndipo amene amalankhula zabodza zokhazokha adzawonongedwa.+ 10  Nʼzosayenera kuti munthu wopusa azikhala moyo wawofuwofu.Chimodzimodzinso kuti munthu wantchito alamulire anthu audindo!+ 11  Kuzindikira kumachititsa kuti munthu abweze mkwiyo wake,+Ndipo kunyalanyaza cholakwa kumamʼchititsa kukhala wokongola.+ 12  Mkwiyo wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango wamphamvu,+Koma kukoma mtima kwake kuli ngati mame pazomera. 13  Mwana wopusa amabweretsa mavuto kwa bambo ake,+Ndipo mkazi wolongolola* ali ngati denga limene silisiya kudontha.+ 14  Nyumba komanso chuma ndi cholowa chochokera kwa makolo,Koma mkazi wanzeru amachokera kwa Yehova.+ 15  Ulesi umabweretsa tulo tofa nato,Ndipo munthu waulesi adzakhala ndi njala.+ 16  Amene amasunga lamulo amasunga moyo wake.+Amene amachita zinthu mosasamala adzafa.+ 17  Amene amakomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova,+Ndipo adzamʼbwezera* zimene anachitazo.+ 18  Langa mwana wako padakali chiyembekezo,+Ndipo usakhale ndi mlandu wochititsa* kuti afe.+ 19  Munthu wosachedwa kupsa mtima ayenera kulipira,Chifukwa ukayesa kumʼpulumutsa, uzichita zimenezi kawirikawiri.+ 20  Mvera uphungu ndipo utsatire malangizo*+Kuti udzakhale wanzeru mʼtsogolo.+ 21  Munthu amakhala ndi mapulani ambiri mumtima mwake,Koma zolinga za Yehova nʼzimene zidzakwaniritsidwe.+ 22  Chinthu chosiririka mwa munthu ndi chikondi chake chokhulupirika,+Ndipo ndi bwino kukhala wosauka kusiyana nʼkukhala munthu wonama. 23  Kuopa Yehova kumathandiza munthu kuti apeze moyo.+Munthu amene amachita zimenezi amagona tulo tokoma ndipo zoipa sizimugwera.+ 24  Munthu waulesi amapisa dzanja lake mʼmbale ya chakudya,Koma nʼkulephera kulibweretsa pakamwa.+ 25  Menya munthu wonyoza+ kuti wosadziwa zinthu achenjere,+Ndipo dzudzula munthu womvetsa zinthu kuti awonjezere zimene akudziwa.+ 26  Munthu amene amazunza bambo ake ndiponso kuthamangitsa mayi ake,Ndi mwana wochititsa manyazi ndi wonyozetsa.+ 27  Mwana wanga ukasiya kumvera malangizo,Udzasochera nʼkusiya kutsatira mawu anzeru. 28  Mboni yopanda pake imanyoza chilungamo,+Munthu woipa amasangalala kuchita zoipa ngati mmene amasangalalira ndi chakudya.+ 29  Zilango amazisungira anthu onyoza,+Ndipo zikwapu ndi zokwapulira msana wa anthu opusa.+

Mawu a M'munsi

^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amayenda mofulumira ndi mapazi ake.”
^ Kapena kuti, “wowolowa manja.”
^ Kapena kuti, “wokonda kudandaula.”
^ Kapena kuti, “adzamʼpatsa mphoto pa.”
^ Kapena kuti, “Ndipo usalakelake.”
^ Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga kapena uphungu.