Miyambo 23:1-35

  • Muzichita zinthu mozindikira akakuitanirani chakudya (2)

  • Musamafunefune chuma (4)

  • Chuma chikhoza kuuluka nʼkupita kutali (5)

  • Usakhale mʼgulu la zidakwa (20)

  • Mowa umaluma ngati njoka (32)

23  Ukakhala pansi kuti udye ndi mfumu,Uzionetsetsa zimene zili pamaso pako.   Uzidziletsa*Ngati umadya kwambiri.   Usalakelake chakudya chake chokoma,Chifukwa ndi chakudya chachinyengo.   Usadzitopetse pofuna kupeza chuma.+ Leka kuchita zimenezi, mʼmalomwake uzisonyeza kuti ndiwe womvetsa zinthu.*   Ukayangʼana pamene panali chumacho, umapeza kuti palibe,+Chifukwa ndithu chimamera mapiko ngati chiwombankhanga nʼkuulukira mʼmwamba.+   Usadye chakudya cha munthu womana.*Usalakelake chakudya chake chokoma,   Chifukwa iye ali ngati munthu amene amakuyangʼanitsitsa kuti adziwe kuchuluka kwa chakudya chimene wadya. Iye amakuuza kuti: “Idya ndi kumwa,” koma salankhula zimenezo ndi mtima wonse.   Mbamu imene wadya udzaisanzaNdipo mawu ako oyamikira adzangopita pachabe.   Usayese kuphunzitsa munthu wopusa,+Chifukwa iye adzanyoza mawu ako anzeru.+ 10  Usamasunthe chizindikiro chakalekale cha malire,+Kapena kulowerera munda wa ana amasiye. 11  Chifukwa amene akuwateteza* ndi wamphamvu.Iye adzawateteza pa mlandu wawo ndi iwe.+ 12  Yesetsa ndi mtima wonse kumvetsera malangizo ndi kuwagwiritsa ntchito,Ndipo khutu lako limvetsere mawu anzeru. 13  Mwana usalephere kumupatsa chilango.*+ Ngakhale utamukwapula ndi chikwapu, sangafe. 14  Umukwapule ndi chikwapu,Kuti upulumutse moyo wake ku Manda.* 15  Mwana wanga, mtima wako ukakhala wanzeru,Ndithu mtima wanga udzasangalala.+ 16  Milomo yako ikamalankhula zinthu zabwino,Ndidzasangalala kuchokera pansi pa mtima.* 17  Mtima wako usamasirire anthu ochimwa,+Koma iwe uziopa Yehova tsiku lonse.+ 18  Chifukwa ukatero udzakhala ndi tsogolo labwino,+Ndipo chiyembekezo chako sichidzawonongedwa. 19  Mwana wanga, mvera ndi kukhala wanzeru,Ndipo tsogolera mtima wako panjira yabwino. 20  Usakhale mʼgulu la anthu amene amamwa vinyo wambiri.+Usakhale mʼgulu la anthu amene amadya nyama mosusuka,+ 21  Chifukwa chidakwa komanso munthu wosusuka adzasauka,+Ndipo kuwodzera kudzaveka munthu nsanza. 22  Uzimvera bambo ako amene anakubereka,Ndipo usanyoze mayi ako chifukwa chakuti akalamba.+ 23  Gula* choonadi ndipo usachigulitse,+Chimodzimodzinso nzeru, malangizo ndi kumvetsa zinthu.+ 24  Bambo a munthu wolungama ndithu adzasangalala.Aliyense amene anabereka mwana wanzeru adzakondwera naye. 25  Bambo ako ndi mayi ako adzasangalala,Ndipo mayi amene anakubereka adzakondwera. 26  Mwana wanga, ndipatse mtima wako,Ndipo maso ako asangalale ndi njira zanga.+ 27  Chifukwa hule lili ngati dzenje lakuya,Ndipo mkazi wachiwerewere* ali ngati chitsime chachingʼono.+ 28  Iye amabisalira anthu panjira ngati wachifwamba.+Amachititsa kuti chiwerengero cha amuna osakhulupirika chiwonjezereke. 29  Ndi ndani amene akuvutika? Ndi ndani amene ali ndi nkhawa? Ndi ndani amene ali pa mikangano? Ndi ndani amene ali ndi madandaulo? Ndi ndani amene ali ndi mabala popanda chifukwa? Ndi ndani amene ali ndi maso ofiira? 30  Ndi amene amakhala nthawi yaitali akumwa vinyo,+Amene amafunafuna* vinyo wosakaniza. 31  Usakopeke ndi kufiira kwa vinyo,Pamene akunyezimira mʼkapu nʼkumatsetserekera kukhosi mwamyaa! 32  Chifukwa pamapeto pake amaluma ngati njoka,Ndipo amatulutsa poizoni ngati mphiri. 33  Maso ako adzaona zinthu zachilendo,Ndipo mtima wako udzalankhula zinthu zokhota.+ 34  Udzakhala ngati munthu amene wagona pakatikati pa nyanja,Komanso ngati munthu amene wagona pansonga ya mtengo* wa ngalawa. 35  Udzanena kuti: “Andimenya koma sindinamve kupweteka. Andikuntha koma sindinadziwe chilichonse. Kodi ndidzuka nthawi yanji?+ Ndikufuna ndikamwenso wina.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Uziika mpeni pakhosi pako.”
Mabaibulo ena amati, “Leka kudzidalira kuti ndiwe womvetsa zinthu.”
Kapena kuti, “cha aliyense amene diso lake ndi loipa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Wowawombola.”
Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “chilango” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga kapena uphungu.
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Impso zanga zidzasangalala.”
Kapena kuti, “Peza.”
Kapena kuti, “wachilendo.” Onani Miy. 2:16.
Kapena kuti, “Amene amasonkhana kuti alawe.”
Kapena kuti, “mlongoti.”