Miyambo 10:1-32

  • Mwana wanzeru amasangalatsa bambo ake (1)

  • Wogwira ntchito mwakhama adzalemera (4)

  • Mawu akachuluka sipalephera kukhala zolakwika (19)

  • Madalitso a Yehova ndi amene amalemeretsa (22)

  • Kuopa Yehova kumatalikitsa moyo (27)

10  Miyambi ya Solomo.+ Mwana wanzeru amasangalatsa bambo ake,+Koma mwana wopusa amamvetsa chisoni mayi ake.  2  Chuma chimene munthu wapeza chifukwa chochita zoipa chidzakhala chopanda phindu,Koma chilungamo nʼchimene chimapulumutsa munthu ku imfa.+  3  Yehova sadzachititsa kuti munthu wolungama akhale ndi njala,+Koma anthu oipa sadzawapatsa zimene amalakalaka.  4  Munthu waulesi adzakhala wosauka,+Koma wogwira ntchito mwakhama adzalemera.+  5  Mwana wochita zinthu mozindikira amatuta zokolola mʼchilimwe,Koma mwana wochititsa manyazi amakhala ali mʼtulo tofa nato pa nthawi yokolola.+  6  Madalitso amapita pamutu pa munthu wolungama,+Koma pakamwa pa anthu oipa pamabisa zachiwawa.  7  Zabwino zimene munthu wolungama ankachita zikakumbukiridwa* amadalitsidwa,+Koma dzina la anthu oipa lidzawola.+  8  Munthu wanzeru mumtima mwake amamvera malangizo,*+Koma wolankhula mopusa adzapeza mavuto.+  9  Munthu wochita zinthu mokhulupirika adzakhala wotetezeka,+Koma munthu wochita zinthu mwachinyengo adzadziwika.+ 10  Munthu amene amatsinzinira ena diso amachititsa ena kumva chisoni,+Ndipo amene amalankhula mopusa adzapeza mavuto.+ 11  Pakamwa pa wolungama pamachokera moyo,+Koma pakamwa pa anthu oipa pamabisa zachiwawa.+ 12  Chidani nʼchimene chimayambitsa mikangano,Koma chikondi chimaphimba machimo onse.+ 13  Nzeru imapezeka pamilomo ya munthu wozindikira,+Koma ndodo amakwapulira msana wa munthu wopanda nzeru.+ 14  Anzeru ndi amene amapitiriza kuphunzira zinthu zamtengo wapatali,+Koma pakamwa pa wopusa pamachititsa kuti awonongedwe.+ 15  Munthu wolemera amaona kuti chuma chake chili* ngati mzinda wokhala ndi mpanda wolimba. Koma anthu osauka amavutika chifukwa cha umphawi wawo.+ 16  Zochita za wolungama zimabweretsa moyo.Koma zochita za woipa zimabweretsa tchimo.+ 17  Amene amamvera malangizo* amathandiza ena kukapeza moyo,*Koma amene amanyalanyaza chidzudzulo amasocheretsa ena. 18  Munthu amene amabisa chidani mumtima mwake amalankhula mabodza,+Ndipo amene amafalitsa mphekesera zoipa ndi wopusa. 19  Mawu akachuluka sipalephera kukhala zolakwika,+Koma amene amalamulira milomo yake amachita zinthu mwanzeru.+ 20  Lilime la wolungama lili ngati siliva wabwino kwambiri,+Koma mtima wa woipa ndi wopanda phindu. 21  Milomo ya wolungama imathandiza* anthu ambiri,+Koma zitsiru zimafa chifukwa chopanda nzeru.+ 22  Madalitso a Yehova ndi amene amalemeretsa munthu,+Ndipo popereka madalitsowa Mulungu sawonjezerapo ululu.* 23  Kwa munthu wopusa, kuchita khalidwe lochititsa manyazi kuli ngati masewera,Koma munthu wozindikira amakhala ndi nzeru.+ 24  Chinthu chimene munthu woipa amaopa nʼchimene chidzamuchitikire,Koma anthu olungama adzapatsidwa zimene amalakalaka.+ 25  Mphepo yamkuntho ikawomba woipa amawonongedwa,+Koma wolungama ali ngati maziko mpaka kalekale.+ 26  Viniga* amachititsa kuti mano ayezimire ndipo utsi umapweteka mʼmaso,Izi nʼzimene munthu waulesi amachita kwa munthu amene wamutuma.* 27  Kuopa Yehova kumatalikitsa moyo,+Koma zaka za anthu oipa zidzafupikitsidwa.+ 28  Zimene anthu olungama akuyembekezera zimasangalatsa,*+Koma chiyembekezo cha anthu oipa sichidzakwaniritsidwa.+ 29  Njira ya Yehova ndi malo achitetezo kwa munthu wopanda cholakwa,+Koma anthu ochita zoipa amawonongedwa mʼnjira imeneyi.+ 30  Wolungama sadzagwetsedwa,+Koma anthu oipa sadzakhalanso padziko lapansi.+ 31  Pakamwa pa munthu wolungama pamalankhula* zanzeru,Koma lilime lolankhula zinthu zopotoka lidzadulidwa. 32  Milomo ya munthu wolungama imadziwa zinthu zosangalatsa,Koma pakamwa pa anthu oipa mʼpachinyengo.

Mawu a M'munsi

^ Kapena kuti, “Mbiri yake ikakumbukiridwa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “malamulo.”
^ Kapena kuti, “amaona kuti zinthu zake zamtengo wapatali zili.”
^ Mabaibulo ena amati, “akuyenda panjira ya kumoyo.”
^ Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga kapena uphungu.
^ Kapena kuti, “imatsogolera.”
^ Kapena kuti, “chisoni; mavuto.”
^ “Viniga” ndi chakumwa chowawasira chomwe chinkapangidwa kuchokera ku vinyo wosasa kapena zakumwa zina zoledzeretsa.
^ Kapena kuti, “kwa amene anamulemba ntchito.”
^ Kapena kuti, “Chiyembekezo cha anthu olungama chimasangalatsa.”
^ Kapena kuti, “pamabereka zipatso.”