Miyambo 3:1-35

  • Kukhala wanzeru komanso kudalira Yehova (1-12)

    • Kulemekeza Yehova pogwiritsa ntchito zinthu zamtengo wapatali (9)

  • Nzeru zimathandiza munthu kuti azisangalala (13-18)

  • Nzeru zimateteza (19-26)

  • Kuchitira ena zinthu zabwino (27-35)

    • Kuthandiza ena ngati tingathe (27)

3  Mwana wanga, usaiwale zimene ndimakuphunzitsa,*Ndipo mtima wako uzisunga malamulo anga.  2  Ukamachita zimenezi, udzakhala ndi masiku ochulukaKomanso moyo wazaka zambiri ndi mtendere.+  3  Usalole kuti chikondi chokhulupirika komanso kukhulupirika* zichoke mwa iwe.+ Uzimange mʼkhosi mwakoNdi kuzilemba pamtima pako.+  4  Ukachita zimenezi, Mulungu ndi anthu+Adzakukomera mtima ndipo adzakuona kuti ndiwe wozindikira.  5  Uzikhulupirira Yehova+ ndi mtima wako wonse,Ndipo usamadalire* luso lako lomvetsa zinthu.+  6  Uzimukumbukira mʼnjira zako zonse,+Ndipo iye adzawongola njira zako.+  7  Usamadzione kuti ndiwe wanzeru.+ Uziopa Yehova ndi kupatuka pa choipa.  8  Zimenezi zidzachiritsa thupi lako*Ndi kutsitsimutsa mafupa ako.  9  Uzilemekeza Yehova ndi zinthu zako zamtengo wapatali+Ndiponso ndi zipatso zako zonse zoyambirira.*+ 10  Ukatero nyumba zako zosungiramo zinthu zidzadzaza kwambiri,+Ndipo zoponderamo mphesa zako zidzasefukira ndi vinyo watsopano. 11  Mwana wanga, usakane malangizo* a Yehova+Ndipo usanyansidwe ndi kudzudzula kwake,+ 12  Chifukwa Yehova amadzudzula munthu amene amamukonda,+Ngati mmene bambo amadzudzulira mwana amene amasangalala naye.+ 13  Wosangalala ndi munthu amene amapeza nzeru,+Ndiponso munthu amene amaphunzira zinthu zimene zingamuthandize kukhala wozindikira. 14  Chifukwa kupeza nzeru nʼkwabwino kuposa kupeza siliva,Ndipo kukhala nazo monga phindu nʼkwabwino kuposa kukhala ndi golide.+ 15  Nʼzamtengo wapatali kuposa miyala ya korali,*Palibe chimene umalakalaka chimene chingafanane nazo. 16  Mʼdzanja lake lamanja muli moyo wautali.Mʼdzanja lake lamanzere muli chuma ndi ulemerero. 17  Kuyenda mʼnjira zake kumasangalatsa,Ndipo kuyenda mʼmisewu yake kumabweretsa mtendere.+ 18  Munthu akagwiritsitsa nzeru, zidzakhala ngati mtengo wa moyo kwa iye,Ndipo anthu amene amazigwiritsitsa adzatchedwa osangalala.+ 19  Yehova anayala maziko a dziko lapansi mwanzeru.+ Anakhazikitsa kumwamba mozindikira.+ 20  Chifukwa chakuti iye amadziwa zinthu, anagawa madzi akuyaNdipo kumwamba kwa mitambo kunagwetsa mame.+ 21  Mwana wanga, zimenezi* zisachoke pamaso pako. Uteteze nzeru zopindulitsa ndiponso kuganiza bwino. 22  Zidzakupatsa moyoKomanso zidzakhala zokongoletsera mʼkhosi mwako. 23  Ukatero udzayenda panjira yako popanda chokuopseza,Ndipo phazi lako silidzapunthwa.*+ 24  Ukagona sudzaopa chilichonse.+Udzagona ndithu, ndipo tulo tako tidzakhala tokoma.+ 25  Sudzaopa zoopsa zilizonse zadzidzidzi,+Kapena mphepo yamkuntho imene ikubwera pa oipa.+ 26  Chifukwa uzidzadalira kwambiri Yehova,+Ndipo adzateteza phazi lako kuti lisakodwe.+ 27  Usalephere kuchitira zabwino anthu amene ukuyenera kuwachitira* zabwinozo,+Ngati ungathe kuwathandiza.*+ 28  Mnzako usamuuze kuti, “Pita, ukabwerenso mawa ndipo ndidzakupatsa,” Ngati ungathe kumupatsa nthawi yomweyo. 29  Usakonze zochitira mnzako zoipa+Pamene iye akuona kuti akukhala nawe mwamtendere. 30  Usakangane ndi munthu popanda chifukwa+Ngati sanakuchitire choipa chilichonse.+ 31  Usasirire munthu wachiwawa+Kapena kusankha kuyenda mʼnjira yake iliyonse, 32  Chifukwa Yehova amanyansidwa ndi munthu wachiphamaso,+Koma anthu owongoka mtima amakhala nawo pa ubwenzi wolimba.+ 33  Yehova amatemberera banja la munthu woipa,+Koma iye amadalitsa nyumba ya munthu wolungama.+ 34  Onyoza, iye amawanyoza,+Koma ofatsa amawakomera mtima.+ 35  Anzeru adzalandira ulemu,Koma opusa amalemekeza zinthu zimene zidzawachititse manyazi.+

Mawu a M'munsi

^ Kapena kuti, “usaiwale malamulo anga.”
^ Kapena kuti, “choonadi.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “usatsamire.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mchombo wako.”
^ Kapena kuti, “Ndiponso ndi zinthu zabwino kwambiri pa zokolola zako.”
^ Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga kapena uphungu.
^ Zikuoneka kuti akutanthauza makhalidwe a Mulungu amene atchulidwa mʼmavesi amʼmbuyomu.
^ Kapena kuti, “silidzawomba chilichonse.”
^ Kapena kuti, “Ngati dzanja lako lingathe kuchita zimenezo.”
^ Kapena kuti, “amene akufunikira.”