Miyambo 15:1-33

  • Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo (1)

  • Maso a Yehova ali paliponse (3)

  • Pemphero la munthu wowongoka mtima limasangalatsa Mulungu (8)

  • Mapulani sakwaniritsidwa ngati anthu sakambirana (22)

  • Kuyamba waganiza usanayankhe (28)

15  Kuyankha modekha* kumabweza mkwiyo,+Koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.+   Lilime la anthu anzeru limalankhula zabwino zimene anthuwo akudziwa,+Koma pakamwa pa zitsiru pamangolankhula mawu opusa.   Maso a Yehova ali paliponse,Amaona anthu oipa ndi abwino omwe.+   Lilime lodekha* lili ngati mtengo wa moyo,+Koma mawu achinyengo amachititsa kuti anthu ataye mtima.   Munthu wopusa amanyoza malangizo* a bambo ake,+Koma munthu wochenjera amamvera ena akamudzudzula.+   Mʼnyumba ya munthu wolungama muli chuma chambiri,Koma zokolola za munthu woipa zimamubweretsera mavuto.+   Milomo ya munthu wanzeru imafalitsa zimene akudziwa,+Koma mtima wa munthu wopusa suchita zimenezo.+   Nsembe ya munthu woipa ndi yonyansa kwa Yehova,+Koma pemphero la munthu wowongoka mtima limamusangalatsa.+   Yehova amanyansidwa ndi njira ya munthu woipa,+Koma amakonda munthu amene amachita chilungamo.+ 10  Chilango chimaoneka choipa* kwa munthu amene wasiya njira yabwino,+Koma aliyense amene amadana ndi kudzudzulidwa adzafa.+ 11  Ngati Yehova amaona bwinobwino amene ali mʼManda* ndiponso malo achiwonongeko,*+ Ndiye kuli bwanji zimene zili mʼmitima ya anthu?+ 12  Munthu wonyoza amadana ndi munthu amene akumudzudzula.+ Iye sadzapempha malangizo kwa anthu anzeru.+ 13  Mtima wachimwemwe umapangitsa kuti nkhope izioneka yosangalala,Koma munthu sasangalala ngati mtima ukumupweteka.+ 14  Anthu anzeru* amayesetsa kuti adziwe zinthu,+Koma pakamwa pa anthu opusa pamasangalala ndi zinthu zopusa.+ 15  Masiku onse a munthu amene akukumana ndi mavuto amakhala oipa,+Koma munthu amene ali ndi mtima wosangalala* amachita phwando nthawi zonse.+ 16  Ndi bwino kukhala ndi zinthu zochepa ukuopa Yehova,+Kusiyana ndi kukhala ndi chuma chambiri koma uli ndi nkhawa.*+ 17  Ndi bwino kudya zamasamba koma pali chikondi,+Kusiyana ndi kudya nyama ya ngʼombe yamphongo yonenepa* koma pali chidani.+ 18  Munthu wosachedwa kupsa mtima amayambitsa mkangano,+Koma munthu amene sakwiya msanga amaziziritsa mkangano.+ 19  Njira ya munthu waulesi ili ngati mpanda wa mitengo yaminga,+Koma njira ya munthu wowongoka mtima ili ngati msewu wosalazidwa bwino.+ 20  Mwana wanzeru amasangalatsa bambo ake,+Koma munthu wopusa amanyoza mayi ake.+ 21  Munthu wopanda nzeru amasangalala ndi uchitsiru,+Koma munthu wozindikira ndi amene amayenda panjira yabwino.+ 22  Mapulani sakwaniritsidwa ngati anthu sakambirana,*Koma alangizi akachuluka zinthu zimayenda bwino.+ 23  Munthu amasangalala akapereka yankho labwino,*+Ndipo mawu onenedwa pa nthawi yoyenera ndi abwino kwambiri.+ 24  Munthu amene ndi wozindikira ali panjira yokwezeka yopita kumoyo,+Ndipo amapewa kuyenda mʼnjira yotsikira ku Manda.*+ 25  Yehova adzagwetsa nyumba za anthu odzikuza,+Koma adzateteza malire a malo a mkazi wamasiye.+ 26  Yehova amadana ndi ziwembu za munthu woipa,+Koma mawu osangalatsa ndi oyera kwa iye.+ 27  Munthu wopeza phindu mwachinyengo amabweretsa mavuto* kwa anthu amʼbanja lake,+Koma amene amadana ndi ziphuphu adzakhalabe ndi moyo.+ 28  Mtima wa munthu wolungama umayamba waganiza usanayankhe,+Koma pakamwa pa anthu oipa pamangolankhula zoipa. 29  Yehova ali kutali ndi anthu oipa,Koma amamva pemphero la anthu olungama.+ 30  Maso owala amapangitsa* kuti mtima usangalale.Uthenga wabwino umachititsa kuti mafupa akhale amphamvu.*+ 31  Munthu amene amamvetsera chidzudzulo chopatsa moyo,Amakhala pakati pa anthu anzeru.+ 32  Aliyense amene amakana malangizo amanyoza moyo wake,+Koma amene amamvetsera akadzudzulidwa amakhala wozindikira.+ 33  Kuopa Yehova nʼkumene kumaphunzitsa munthu kuchita zinthu mwanzeru,+Ndipo ulemerero umabwera pambuyo pa kudzichepetsa.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “moleza mtima.”
Kapena kuti, “Lilime lochiritsa.”
Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga, kapena uphungu.
Kapena kuti, “chowawa kwambiri.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “ndiponso Abadoni.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amtima wanzeru.”
Kapena kuti, “wabwino.”
Kapena kuti, “koma uli wosokonezeka maganizo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “yodyetsedwa bwino.”
Kapena kuti, “sakambirana moona mtima.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amasangalala ndi yankho lochokera pakamwa pake.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “manyazi.”
Kapena kuti, “Kuyangʼana munthu ndi nkhope yachimwemwe kumapangitsa.”
Kapena kuti, “umanenepetsa mafupa.”