Miyambo 5:1-23

  • Chenjezo lokhudza akazi amakhalidwe oipa (1-14)

  • Sangalala ndi mkazi wako (15-23)

5  Mwana wanga, tchera makutu ako ku mawu anga anzeru. Mvetsera mosamala zimene ndikukuphunzitsa zokhudza kukhala wozindikira,+  2  Kuti uteteze luso lako loganiza bwino,Ndiponso kuti milomo yako iteteze kudziwa zinthu.+  3  Chifukwa milomo ya mkazi wamakhalidwe oipa* imakha uchi ngati chisa cha njuchi,+Ndipo mʼkamwa mwake ndi mosalala kuposa mafuta.+  4  Koma pamapeto pake amawawa kwambiri ngati chitsamba chowawa.+Ndipo amakhala wakuthwa ngati lupanga lakuthwa konsekonse.+  5  Mapazi ake amatsikira ku imfa. Miyendo yake imalowera ku Manda.*  6  Iye saganizira zimene zingamuthandize kukapeza moyo. Amangoyendayenda, osadziwa kumene akulowera.  7  Tsopano mwana wanga,* ndimvere,Ndipo usapatuke pa zimene ndikukuuza.  8  Ukhale kutali kwambiri ndi iye.Usayandikire pakhomo la nyumba yake,+  9  Kuti usapereke ulemu wako kwa anthu ena+Komanso kuti usakumane ndi mavuto mʼzaka zotsala za moyo wako.*+ 10  Ndiponso kuti alendo asakuwonongere zinthu zako,*+Komanso kuti zinthu zimene unazipeza movutikira zisapite kunyumba ya mlendo. 11  Ukapanda kumvera, udzabuula kumapeto kwa moyo wako,Mphamvu zako zikadzatha komanso ukadzawonda kwambiri.+ 12  Ndipo udzanena kuti: “Ndinkadana ndi malangizo* ine! Ndipo mtima wanga sunkamvera, ena akandidzudzula. 13  Sindinamvere mawu a alangizi anga,Kapena kutchera khutu kwa aphunzitsi anga. 14  Ndangotsala pangʼono kutheratuPakati pa mpingo wonse.”*+ 15  Imwa madzi ochokera mʼchitsime chako,Komanso madzi oyenderera kuchokera pakasupe wako.+ 16  Kodi akasupe ako amwazike panja?Ndipo kodi mitsinje yako ya madzi imwazike mʼmabwalo amumzinda?+ 17  Zimenezi zikhale zako zokhaosati uzigawana ndi anthu achilendo.+ 18  Kasupe wako akhale wodalitsidwa,*Ndipo uzisangalala ndi mkazi amene unamukwatira udakali wachinyamata.+ 19  Iye akhale ngati mbawala yaikazi yachikondi komanso ngati kamwana ka mbuzi zamʼmapiri kokongola.+ Mabere ake azikukhutiritsa* nthawi zonse. Chikondi chake chizikusangalatsa kwambiri nthawi zonse.+ 20  Ndiye mwana wanga, kodi pali chifukwa chilichonse choti uzisangalalira ndi mkazi wamakhalidwe oipa,*Kapena choti uzikumbatirira chifuwa cha mkazi wachiwerewere?*+ 21  Chifukwa maso a Yehova amaona chilichonse chimene munthu akuchita,Ndipo iye amafufuza njira zake zonse.+ 22  Woipa amakodwa ndi zolakwa zake zomwe,Ndipo adzamangidwa ndi zingwe za tchimo lake lomwe.+ 23  Iye adzafa chifukwa chosamvera malangizo,Ndipo adzasochera chifukwa cha kuchuluka kwa uchitsiru wake.

Mawu a M'munsi

^ Mʼchilankhulo choyambirira, “wachilendo.”
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ana anga.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “kuti usapereke zaka zako ku zinthu zankhanza.”
^ Kapena kuti, “mphamvu zako.”
^ Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga kapena uphungu.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Pakati pa msonkhano komanso mpingo.”
^ Kapena kuti, “Pamene umatunga madzi ako pakhale podalitsidwa.”
^ Kapena kuti, “azikusangalatsa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “wachilendo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “wachilendo.”