Miyambo 11:1-31

  • Anthu odzichepetsa ndi amene ali ndi nzeru (2)

  • Wampatuko amawononga anthu ena (9)

  • “Zinthu zimayenda bwino ngati pali alangizi ambiri” (14)

  • Munthu wopereka mowolowa manja zinthu zidzamuyendera bwino (25)

  • Munthu amene amadalira chuma chake adzakumana ndi mavuto (28)

11  Yehova amanyasidwa ndi masikelo achinyengo,Koma sikelo imene imayeza molondola imamusangalatsa.*+   Kudzikweza kukafika manyazi amafikanso,+Koma anthu odzichepetsa ndi amene ali ndi nzeru.+   Kukhulupirika kwa anthu owongoka mtima nʼkumene kumawatsogolera,+Koma wochita zinthu mwachinyengo adzawonongedwa chifukwa cha mabodza ake.+   Chuma chidzakhala chopanda* phindu pa tsiku la mkwiyo woopsa,+Koma chilungamo nʼchimene chidzapulumutse munthu ku imfa.+   Chilungamo cha munthu wopanda cholakwa chimawongola njira yake,Koma woipa adzagwa chifukwa cha kuipa kwake komwe.+   Chilungamo cha anthu owongoka mtima chidzawapulumutsa,+Koma anthu ochita zinthu mwachinyengo adzagwidwa ndi zolakalaka zawo.+   Munthu woipa akafa, chiyembekezo chake chimathera pomwepo,Ndipo zonse zimene amayembekezera kuchita ndi mphamvu zake zimalephereka.+   Wolungama amapulumutsidwa ku mavuto,Ndipo mʼmalo mwake woipa ndi amene amakumana ndi mavutowo.+   Wampatuko* amawononga mnzake ndi pakamwa pake,Koma anthu olungama amapulumutsidwa chifukwa chodziwa zinthu.+ 10  Mzinda umasangalala chifukwa cha makhalidwe abwino a anthu olungama,Ndipo anthu oipa akawonongedwa anthu amafuula mosangalala.+ 11  Mzinda umakhala wapamwamba chifukwa cha madalitso a anthu olungama,+Koma umagwetsedwa chifukwa cha pakamwa pa anthu oipa.+ 12  Aliyense wopanda nzeru amasonyeza kuti akuipidwa ndi* mnzake,Koma munthu amene alidi wozindikira amakhala chete.+ 13  Wonenera anzake zoipa amayendayenda nʼkumaulula zinsinsi za anzake,+Koma munthu wokhulupirika* amasunga chinsinsi.* 14  Pakakhala popanda malangizo anzeru, anthu amagwa.Koma zinthu zimayenda bwino* ngati pali alangizi* ambiri.+ 15  Munthu amene amalonjeza kuti adzapereka ngongole ya munthu wachilendo mwiniwakeyo akadzalephera kubweza, zinthu sizidzamuyendera bwino.+Koma amene amapewa* kugwirana dzanja pochita mgwirizano adzakhala wotetezeka. 16  Mkazi wachikoka amapeza ulemu.+Koma anthu ankhanza amalanda chuma cha ena. 17  Munthu wokoma mtima* zinthu zimamuyendera bwino,*+Koma munthu wankhanza amadzibweretsera mavuto.*+ 18  Munthu woipa amapeza malipiro achinyengo,+Koma wofesa chilungamo amalandira mphoto yeniyeni.+ 19  Munthu wosasunthika pachilungamo adzapeza moyo,+Koma munthu wofunafuna zoipa adzafa. 20  Anthu amtima wopotoka, Yehova amanyasidwa nawo,+Koma amene amachita zinthu mosalakwitsa kanthu amamusangalatsa.+ 21  Musakaikire mfundo yakuti:* Munthu woipa sadzalephera kulangidwa,+Koma ana a anthu olungama adzapulumuka. 22  Mofanana ndi ndolo yagolide imene ili pamphuno ya nkhumba,Ndi mmenenso amakhalira mkazi wokongola amene amakana nzeru. 23  Zimene munthu wolungama amalakalaka zimakhala ndi zotsatira zabwino.+Koma zimene oipa amayembekezera zimabweretsa mkwiyo woopsa. 24  Munthu amapereka mowolowa manja* ndipo pamapeto pake amakhala ndi zinthu zochuluka.+Munthu wina amaumira zimene amafunika kupatsa anthu ena, koma amasauka.+ 25  Munthu wopereka mowolowa manja zinthu zidzamuyendera bwino,*+Ndipo amene amatsitsimula ena* nayenso adzatsitsimulidwa.+ 26  Wokana kugulitsa mbewu zake, anthu adzamʼtemberera.Koma wolola kuzigulitsa adzamudalitsa. 27  Munthu amene amafunitsitsa kuchita zabwino, adzakomeredwa mtima.+Koma wofunitsitsa kuchita zoipa, zoipazo zidzamʼbwerera.+ 28  Munthu amene amadalira chuma chake adzakumana ndi mavuto,+Koma anthu olungama adzasangalala ngati mtengo wa masamba obiriwira.+ 29  Aliyense wobweretsa mavuto* kwa anthu amʼbanja lake cholowa chake chidzakhala mphepo,+Ndipo munthu wopusa adzakhala wantchito wa munthu wanzeru. 30  Zotsatira za zimene munthu wolungama amachita zili ngati mtengo wa moyo,+Ndipo munthu amene amalimbikitsa ena kuchita zabwino ndi wanzeru.+ 31  Ngati wolungama padziko lapansi amapatsidwa mphoto,Ndiye kuli bwanji woipa ndi wochimwa?+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mwala woyezera wolemera mokwanira umamusangalatsa.”
Kapena kuti, “Zinthu zamtengo wapatali zidzakhala zopanda.”
Kapena kuti, “Munthu wosaopa Mulungu.”
Kapena kuti, “amanyoza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wa mzimu wokhulupirika.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amabisa nkhani.”
Kapena kuti, “Koma munthu amapulumuka.”
Kapena kuti, “aphungu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amadana ndi.”
Kapena kuti, “wachikondi chokhulupirika.”
Kapena kuti, “amachitira zabwino moyo wake.”
Kapena kuti, “manyazi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ngakhale dzanja ligwirane ndi dzanja linzake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amamwaza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzanenepetsedwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amathirira ena mosaumira.”
Kapena kuti, “manyazi.”