Miyambo 31:1-31

  • MAWU A MFUMU LEMUELI (1-31)

    • Ndani amene angapeze mkazi wamakhalidwe abwino? (10)

    • Amagwira ntchito mwakhama (17)

    • Kukoma mtima kuli palilime lake (26)

    • Ana ndi mwamuna wake amamutamanda (28)

    • Kuoneka bwino komanso kukongola sikuchedwa kutha (30)

31  Mawu a Mfumu Lemueli, uwu ndi uthenga wamphamvu umene mayi ake anamupatsa pomulangiza:+  2  Kodi ndikuuze chiyani mwana wanga?Kodi ndikuuze mawu otani iwe mwana wochokera mʼmimba mwanga?Kodi ndikuuze mawu otani iwe mwana wa malonjezo anga?+  3  Usamapereke mphamvu zako kwa akazi,+Kapena kutsatira njira zimene zimachititsa kuti mafumu awonongedwe.+  4  Nʼkosayenera kuti mafumu azimwa vinyo,Nʼkosayenera kuti mafumu azichita zimenezi, iwe Lemueli,Kapena kuti olamulira azinena kuti: “Kodi chakumwa changa chili kuti?”+  5  Chifukwa angamwe nʼkuiwala malamuloNdiponso kupondereza ufulu wa anthu onyozeka.  6  Pereka mowa kwa anthu amene akuwonongedwa+Komanso vinyo kwa anthu amene ali ndi nkhawa.*+  7  Asiyeni amwe kuti aiwale umphawi wawo,Ndipo asakumbukirenso mavuto awo.  8  Lankhula poteteza anthu amene sangathe kudziteteza okha.Teteza ufulu wa anthu onse amene akuwonongedwa.+  9  Lankhula ndipo uweruze mwachilungamo.Teteza ufulu wa anthu onyozeka komanso osauka.*+ א [Aleph] 10  Kodi ndi ndani amene angapeze mkazi wamakhalidwe abwino?*+ Ndi wamtengo wapatali kuposa miyala ya korali.* ב [Beth] 11  Mwamuna wake amamudalira ndi mtima wonse,Ndipo mwamunayo amapeza chilichonse chimene akufunikira. ג [Gimel] 12  Masiku onse a moyo wake,Mkaziyo amachitira mwamuna wakeyo zinthu zabwino osati zoipa. ד [Daleth] 13  Amatenga ulusi ndi nsalu,Ndipo amasangalala kugwira ntchito ndi manja ake.+ ה [He] 14  Iye ali ngati sitima zapamadzi za munthu wamalonda,+Amabweretsa chakudya chake kuchokera kutali. ו [Waw] 15  Amadzukanso kudakali usiku,Nʼkupereka chakudya kwa banja lakeNdipo atsikana ake antchito amawapatsa gawo lawo.+ ז [Zayin] 16  Amaganizira zogula munda ndipo amauguladi.Amalima munda wa mpesa chifukwa cha khama lake.* ח [Heth] 17  Amakonzekera kugwira ntchito yovuta,*+Ndipo amalimbitsa manja ake. ט [Teth] 18  Amaonetsetsa kuti akupeza phindu pa malonda ake.Nyale yake simazima usiku. י [Yod] 19  Manja ake amagwira ndodo yokulungako ulusi,Ndipo zala zake zimagwira ndodo yopotera chingwe.+ כ [Kaph] 20  Amatambasula dzanja lake nʼkuthandiza munthu wonyozeka,Ndipo amatambasula manja ake kuti athandize wosauka.+ ל [Lamed] 21  Kukamazizira, iye sadera nkhawa za banja lakeChifukwa anthu onse a mʼbanja lake amavala zovala zotentha.* מ [Mem] 22  Iye amapanga yekha zoyala pabedi. Zovala zake zimakhala za nsalu zabwino ndiponso za ubweya wa nkhosa wapepo. נ [Nun] 23  Mwamuna wake amadziwika bwino pamageti a mzinda,+Pamene amakhala pamodzi ndi akulu amʼdzikolo. ס [Samekh] 24  Iye amapanga zovala* nʼkuzigulitsa,Ndipo amapanga malamba nʼkuwapereka kwa amalonda. ע [Ayin] 25  Iye amavala mphamvu ndi ulemerero ngati chovala,Ndipo sada nkhawa akamaganizira zamʼtsogolo. פ [Pe] 26  Amatsegula pakamwa pake mwanzeru,+Ndipo lamulo la kukoma mtima lili* palilime lake. צ [Tsade] 27  Iye amayangʼanira ntchito zapabanja pake,Ndipo sadya chakudya cha ulesi.+ ק [Qoph] 28  Ana ake amaimirira nʼkumutchula kuti ndi wosangalala.Mwamuna wake amaimirira nʼkumutamanda kuti: ר [Resh] 29  “Pali akazi ambiri amakhalidwe abwino,*Koma iweyo umaposa onsewo.” ש [Shin] 30  Munthu akhoza kuoneka ngati wabwino koma zisali choncho ndipo kukongola sikungachedwe kutha,*+Koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.+ ת [Taw] 31  Mʼpatseni mphoto chifukwa cha zimene amachita,*+Ndipo ntchito zake zimutamande mʼmageti a mzinda.+

Mawu a M'munsi

^ Kapena kuti, “amene mtima wawo ukuwawa.”
^ Kapena kuti, “Teteza anthu onyozeka komanso osauka pa mlandu wawo.”
^ Kapena kuti, “wabwino kwambiri.”
^ Kapena kuti, “pogwiritsa ntchito ndalama zimene wapeza.” Mʼchilankhulo choyambirira, “pogwiritsa ntchito zipatso za manja ake.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Amamangirira mphamvu mchiuno mwake.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “zovala ziwiri.”
^ Kapena kuti, “zovala zamkati.”
^ Kapena kuti, “Malangizo achikondi ali; Lamulo la chikondi chokhulupirika lili.”
^ Kapena kuti, “abwino kwambiri.”
^ Kapena kuti, “kukhoza kukhala kopanda phindu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Mupatseni kuchokera pa zipatso za manja ake.”