Miyambo 29:1-27

  • Mwana womulekerera amachititsa manyazi (15)

  • Ngati anthu sakutsogoleredwa amachita zinthu motayirira (18)

  • Munthu wosachedwa kukwiya amayambitsa mkangano (22)

  • Munthu wodzichepetsa adzapeza ulemerero (23)

  • Kuopa anthu ndi msampha (25)

29  Munthu amene amaumitsa khosi lake* pambuyo podzudzulidwa mobwerezabwereza+Adzathyoledwa mwadzidzidzi ndipo sadzachira.+  2  Olungama akachuluka, anthu amasangalala,Koma munthu woipa akamalamulira, anthu amabuula.+  3  Munthu amene amakonda nzeru amasangalatsa bambo ake,+Koma woyenda ndi mahule amawononga chuma chake.+  4  Mfumu ikamachita zinthu zachilungamo dziko limalimba,+Koma munthu wokonda ziphuphu amaligwetsa.  5  Munthu amene amayamikira mnzake mwachiphamasoAkuyalira ukonde mapazi ake.+  6  Tchimo la munthu woipa limamutchera msampha,+Koma munthu wolungama amafuula mokondwera ndipo amasangalala.+  7  Wolungama amafunitsitsa kuti anthu osauka aziweruzidwa mwachilungamo,+Koma woipa safuna kuchita zimenezi.+  8  Anthu odzitama ali ngati anthu amene amayatsa tauni,+Koma anthu anzeru amaletsa mkwiyo.+  9  Munthu wanzeru akayamba kukangana ndi chitsiru,Pamangokhala phokoso ndi kunyozana, ndipo munthu wanzeruyo sapindula chilichonse.+ 10  Anthu okonda kukhetsa magazi amadana ndi munthu aliyense wosalakwa,+Ndipo amafuna kuchotsa moyo wa anthu owongoka mtima.* 11  Munthu wopusa amatulutsa mkwiyo wake wonse,+Koma wanzeru amakhala wodekha ndipo amalamulira mkwiyo wake.+ 12  Wolamulira akamamvera mabodza,Antchito ake onse adzakhala oipa.+ 13  Munthu wosauka komanso munthu wopondereza ena ndi ofanana* pa chinthu chimodzi ichi: Yehova amachititsa kuti maso a onsewa aziona kuwala.* 14  Mfumu ikamaweruza anthu osauka mwachilungamo,+Idzapitiriza kulamulira mpaka kalekale.+ 15  Chikwapu* komanso kudzudzula nʼzimene zimapereka nzeru,+Koma mwana womulekerera amachititsa manyazi mayi ake. 16  Oipa akachuluka, machimo amachuluka,Koma olungama adzaona oipawo akugwa.+ 17  Langa mwana wako ndipo adzakupatsa mpumuloKomanso adzakusangalatsa kwambiri.+ 18  Ngati anthu sakutsogoleredwa ndi Mulungu, amachita zinthu motayirira,+Koma osangalala ndi amene amatsatira chilamulo.+ 19  Wantchito safuna kusintha ndi mawu okha,Chifukwa ngakhale atamvetsa mawuwo, safuna kuwatsatira.+ 20  Kodi waona munthu amene amafulumira kulankhula asanaganize?+ Munthu wopusa ali ndi chiyembekezo chachikulu kuposa munthu ameneyu.+ 21  Ngati munthu akusasatitsa kapolo wake kuyambira ali mwana,Mʼtsogolo adzakhala wosayamika. 22  Munthu wosachedwa kukwiya amayambitsa mkangano.+Aliyense amene sachedwa kupsa mtima amakhala ndi machimo ambiri.+ 23  Kudzikuza kwa munthu kudzamutsitsa,+Koma amene ali ndi mtima wodzichepetsa adzapeza ulemerero.+ 24  Amene amathandiza munthu wakuba amadzibweretsera mavuto. Iye angamve kuitana kuti akapereke umboni,* koma osakanena chilichonse.+ 25  Kuopa anthu ndi msampha,*+Koma amene amakhulupirira Yehova adzatetezedwa.+ 26  Anthu ambiri amafunitsitsa kuonana ndi wolamulira,*Koma kwa Yehova nʼkumene munthu amapeza chilungamo.+ 27  Munthu wopanda chilungamo ndi wonyansa kwa anthu olungama,+Koma munthu amene amachita zabwino ndi wonyansa kwa munthu woipa.+

Mawu a M'munsi

^ Kapena kuti, “amene safuna kusintha.”
^ Mabaibulo ena amati, “Koma anthu owongoka mtima amasamalira moyo wa anthu opanda cholakwawo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amakumana pamodzi.”
^ Kutanthauza kuti amawapatsa moyo.
^ Kapena kuti, “Chilango.”
^ Kapena kuti, “lumbiro limene linalinso ndi mawu otemberera.”
^ Kapena kuti, “kumatchera msampha.”
^ Mabaibulo ena amati, “amafunitsitsa kuti wolamulira awakomere mtima.”