Miyambo 20:1-30

  • Womwa vinyo wambiri amayamba kunyoza (1)

  • Waulesi salima nthawi yozizira (4)

  • Maganizo amumtima mwa munthu ali ngati madzi akuya (5)

  • Chenjezo pa nkhani yolumbira usanaganize bwino (25)

  • Ulemerero wa anyamata ndi mphamvu zawo (29)

20  Munthu amene amamwa vinyo wambiri amayamba kunyoza+ ndipo amene amamwa mowa wambiri amachita zosokoneza.+Aliyense amene amasochera ndi zinthu zimenezi alibe nzeru.+  2  Kuopsa kwa mfumu kuli ngati kubangula kwa mkango wamphamvu.+Aliyense woputa mkwiyo wake akuika moyo wake pangozi.+  3  Munthu amalemekezeka akapewa mkangano,+Koma aliyense wopusa amafulumira kuyambitsa mkangano.+  4  Waulesi salima nthawi yozizira,Choncho iye azidzapemphapempha nthawi yokolola chifukwa adzakhala alibe kanthu.*+  5  Maganizo amumtima* mwa munthu ali ngati madzi akuya,Koma munthu wozindikira ndi amene amawatunga.  6  Anthu ambiri amanena kuti ali ndi chikondi chokhulupirika,Koma ndi ndani amene angapeze munthu wokhulupirika?  7  Munthu wolungama amachita zinthu mokhulupirika.+ Ana ake ndi osangalala.+  8  Mfumu ikakhala pampando wachifumu kuti iweruze,+Maso ake amazindikira* anthu onse oipa.+  9  Ndi ndani anganene kuti: “Ndayeretsa mtima wanga.+Ndine woyera ku tchimo langa”?+ 10  Miyala yachinyengo yoyezera komanso miyezo yachinyengo,*Zonsezi nʼzonyansa kwa Yehova.+ 11  Ngakhale mwana* amadziwika ndi zochita zake,Ngati khalidwe lake lili loyera ndiponso labwino.+ 12  Khutu lakumva ndiponso diso loona,Zonsezi anazipanga ndi Yehova.+ 13  Usamakonde tulo chifukwa ungasauke.+ Tsegula maso ako ndipo udzakhala ndi chakudya chambiri.+ 14  Wogula amanena kuti, “chinthu ichi si chabwino, si chabwino chimenechi!”Kenako amachoka ndipo amayamba kudzitama.+ 15  Pali golide komanso miyala yambiri yamtengo wapatali ya korali,*Koma milomo yodziwa zinthu ndi yamtengo wapatali.+ 16  Ngati munthu walonjeza kuti akhala chikole kwa mlendo, umulande chovala chake.+Komanso umulande chikole ngati walonjeza zimenezi kwa mkazi wachilendo.+ 17  Chakudya chimene munthu wachipeza mwachinyengo chimamukomera,Koma pambuyo pake mʼkamwa mwake mumadzaza miyala.+ 18  Anthu akakambirana zolinga zawo zimakwaniritsidwa,*+Ndipo uzitsatira malangizo anzeru pomenya nkhondo yako.+ 19  Wonenera anzake zoipa amayendayenda nʼkumaulula zinsinsi.+Usamagwirizane ndi munthu amene amakonda kunena miseche.* 20  Aliyense amene amatemberera bambo ake komanso mayi ake,Nyale yake idzazimitsidwa kukagwa mdima.+ 21  Munthu akapeza cholowa mwadyera,Pamapeto pake Mulungu sadzamudalitsa.+ 22  Usanene kuti: “Ndidzabwezera choipa.”+ Yembekezera Yehova+ ndipo iye adzakupulumutsa.+ 23  Miyala yachinyengo* yoyezera ndi yonyansa kwa Yehova,Ndipo masikelo achinyengo si abwino. 24  Yehova ndi amene amatsogolera mapazi a munthu.+Ndiye munthu payekha angadziwe bwanji njira yoyenera kuyenda? 25  Umakhala msampha munthu akathamangira kufuula kuti, “Nʼzoyera!”+ Koma pambuyo polonjeza nʼkuyamba kuganiziranso bwino zimene walonjezazo.+ 26  Mfumu yanzeru imazindikira anthu oipa,+Ndipo imawaponda ndi wilo lopunthira mbewu.+ 27  Mpweya wa munthu ndi nyale ya Yehova.Imafufuza zinthu zamkati mwa mtima wake. 28  Kukhulupirika komanso chikondi chokhulupirika zimateteza mfumu.+Mfumuyo ikamasonyeza chikondi chokhulupirika, mpando wake wachifumu umakhazikika.+ 29  Ulemerero wa anyamata ndi mphamvu zawo,+Ndipo ulemerero wa anthu achikulire ndi imvi zawo.+ 30  Mabala obwera chifukwa chopatsidwa chilango amachotsa zoipa,+Ndipo zikwapu zimayeretsa mtima wa munthu.

Mawu a M'munsi

^ Mabaibulo ena amati, “Pa nthawi yokolola adzafunafuna zinthu koma sadzazipeza.”
^ Kapena kuti, “Zolinga zamumtima.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Malangizo amumtima.”
^ Kapena kuti, “amapeta.”
^ Kapena kuti, “Miyala iwiri yosiyana yoyezera ndiponso zinthu ziwiri zosiyana zoyezera.”
^ Kapena kuti, “mnyamata.”
^ Kapena kuti, “zimakhazikika.”
^ Kapena kuti, “amene amakonda kukopa ena ndi milomo yake.”
^ Kapena kuti, “miyala iwiri yosiyana yoyezera.”