Miyambo 25:1-28

  • Kusunga chinsinsi (9)

  • Mawu osankhidwa bwino (11)

  • Osamapitapita kunyumba kwa mnzako (17)

  • Kuunjika makala amoto pamutu pa mdani (21, 22)

  • Nkhani yabwino ili ngati madzi ozizira (25)

25  Miyambi ina ya Solomo+ imene atumiki a Hezekiya+ mfumu ya Yuda anakopera ndi iyi:  2  Kusunga chinsinsi ndi ulemerero wa Mulungu,+Ndipo ulemerero wa mafumu ndi kufufuza bwino nkhani.  3  Nʼzosatheka kufufuza kutalika kwa kumwamba komanso kuzama kwa dziko lapansi,Nʼchimodzimodzinso mitima ya mafumu.  4  Yengani siliva nʼkuchotsa zonse zosafunika,Ndipo yense adzatuluka woyengeka bwino.+  5  Chotsani woipa pamaso pa mfumu,Ndipo mpando wake wachifumu udzakhazikika chifukwa cha chilungamo.+  6  Usadzilemekeze wekha pamaso pa mfumu,+Ndipo usakhale pakati pa anthu olemekezeka,+  7  Chifukwa ndi bwino kuti mfumuyo ikuuze kuti, “Bwera udzakhale apa,” Kusiyana nʼkuti ikuchititse manyazi pamaso pa munthu wolemekezeka.+  8  Usamafulumire kupititsa mlandu kukhoti,Chifukwa udzachita chiyani mnzako akadzapereka umboni wosonyeza kuti iweyo ndi wolakwa?+  9  Thetsa nkhaniyo pokambirana ndi mnzakoyo,+Koma usaulule nkhani zachinsinsi zimene unauzidwa,*+ 10  Kuti amene akumvetsera asakuchititse manyaziKomanso kuti usafalitse nkhani yoipa* imene sungathe kuithetsa kuti isapitirize kufalikira. 11  Mawu olankhulidwa pa nthawi yoyenera+Ali ngati zipatso za maapozi agolide mʼmbale zasiliva. 12  Munthu wanzeru akamadzudzula munthu wa khutu lomvetsera+Amakhala ngati ndolo yagolide ndiponso ngati chokongoletsera chagolide woyenga bwino. 13  Nthumwi yokhulupirika kwa anthu amene aitumaIli ngati kuzizira kwa sinowo* pa tsiku lokolola,Chifukwa imatsitsimula moyo wa abwana ake.+ 14  Munthu wodzitama kuti apereka mphatso koma nʼkulephera kupereka,+Ali ngati mitambo komanso mphepo yosabweretsa mvula. 15  Chifukwa cha kuleza mtima munthu angathe kunyengerera munthu waudindo,Ndipo mawu okoma akhoza* kuthyola fupa.+ 16  Ukapeza uchi udye umene ungakukwane,Chifukwa ukadya wambiri ungathe kuusanza.+ 17  Phazi lako lisamapitepite kunyumba kwa mnzako,Kuti angatope nawe nʼkuyamba kudana nawe. 18  Munthu wopereka umboni wabodza pa mlandu wa mnzake+Ali ngati chibonga chakunkhondo, lupanga, komanso muvi wakuthwa. 19  Kukhulupirira munthu wosadalirika* pa nthawi yamavutoKuli ngati dzino lothyoka komanso phazi lotsimphina. 20  Amene amaimbira nyimbo munthu amene ali ndi chisoni mumtima mwake+Ali ngati munthu amene amavula chovala pa tsiku lozizira,Komanso ngati viniga* amene wathiridwa musoda 21  Ngati mdani wako* ali ndi njala, umʼpatse chakudya.Ngati ali ndi ludzu, umʼpatse madzi akumwa,+ 22  Ukachita zimenezi ndiye kuti ukumuunjikira makala amoto pamutu pake,*+Ndipo Yehova adzakupatsa mphoto. 23  Mphepo yakumpoto imabweretsa mvula yambiriNdipo lilime lonena miseche limachititsa kuti anthu akhale ndi nkhope zolusa.+ 24  Ndi bwino kukhala pakona ya denga la nyumbaKusiyana ndi kukhala mʼnyumba limodzi ndi mkazi wolongolola.*+ 25  Nkhani yabwino yochokera kudziko lakutali+Ili ngati madzi ozizira kwa munthu wotopa. 26  Munthu wolungama amene amagonja* nʼkuchita zofuna za munthu woipaAmakhala ngati kasupe wamatope komanso chitsime chimene chawonongedwa. 27  Si bwino kudya uchi wambiri,+Komanso si bwino kuti munthu adzifunire yekha ulemerero.+ 28  Munthu wosaugwira mtima+Ali ngati mzinda umene mpanda wake wagumulidwa.

Mawu a M'munsi

^ Kapena kuti, “usaulule zinsinsi za ena.”
^ Kapena kuti, “mphekesera zoipa.”
^ Kapena kuti, “chipale chofewa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “lilime lofewa likhoza.”
^ Mabaibulo ena amati, “munthu amene amachita zachinyengo.”
^ “Viniga” ndi chakumwa chowawasira chomwe chinkapangidwa kuchokera ku vinyo wosasa kapena zakumwa zina zoledzeretsa.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “munthu amene amadana nawe.”
^ Kutanthauza kufewetsa mtima wake komanso kumuchititsa kuti azichita zinthu zabwino.
^ Kapena kuti, “wokonda kudandaula.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amanjenjemera pamaso pa munthu woipa.”