Miyambo 17:1-28

  • Usabwezere zoipa mʼmalo mwa zabwino (13)

  • Mkangano usanabuke, chokapo (14)

  • Mnzako weniweni amakusonyeza chikondi nthawi zonse (17)

  • “Mtima wosangalala uli ngati mankhwala amene amachiritsa” (22)

  • Munthu wozindikira amapitiriza kukhala wodekha (27)

17  Ndi bwino kudya mkate wouma pali mtendere,*+Kusiyana ndi kuchita maphwando ochuluka* mʼnyumba imene muli mikangano.+  2  Wantchito wozindikira adzalamulira mwana wa mbuye wake amene amachita zinthu zochititsa manyazi.Adzalandira nawo cholowa pamodzi ndi ana a mbuye wake.  3  Siliva amamuyengera mʼmbiya yoyengera ndipo golide amamuyengera mungʼanjo,+Koma Yehova ndi amene amayesa mitima.+  4  Munthu woipa amakonda kumvetsera mawu opweteka.Ndipo munthu wachinyengo amamvetsera lilime loyambitsa mavuto.+  5  Wonyoza munthu wosauka amanyoza amene anamupanga.+Ndipo amene amasangalala ndi tsoka la wina sadzalephera kulangidwa.+  6  Zidzukulu zili ngati chisoti chaulemu kwa anthu okalamba,Ndipo ana amalemekezeka chifukwa cha bambo awo.*  7  Sitingayembekezere kuti munthu wopusa alankhule zinthu zanzeru.*+ Ndipo nʼzosayenera kuti wolamulira* azilankhula zabodza.+  8  Mphatso ili ngati mwala wamtengo wapatali kwa mwiniwake.*+Kulikonse kumene wapita, imachititsa kuti zinthu zimuyendere bwino.+  9  Aliyense amene amakhululuka* zolakwa akufunafuna chikondi,+Koma amene amangokhalira kulankhula za nkhani inayake amalekanitsa mabwenzi apamtima.+ 10  Kudzudzula kumamufika pamtima munthu womvetsa zinthu,+Kuposa kukwapula munthu wopusa zikwapu 100.+ 11  Munthu woipa amangofuna kupanduka,Koma munthu wankhanza adzatumidwa kuti akamulange.+ 12  Ndi bwino kukumana ndi chimbalangondo chimene ana ake asowa,Kusiyana ndi kukumana ndi chitsiru chimene chimachita zopusa.+ 13  Ngati munthu amabwezera zoipa pa zabwino,Zoipa sizidzachoka panyumba yake.+ 14  Kuyambitsa ndewu kuli ngati kuboola damu kuti madzi atulukemo.*Choncho mkangano usanabuke, chokapo.+ 15  Aliyense wonena kuti munthu woipa alibe mlandu ndiponso aliyense wonena kuti munthu wolungama ndi wolakwa,+Onsewa ndi onyansa kwa Yehova. 16  Kodi pali phindu lililonse ngati munthu wopusa ali ndi njira yopezera nzeru,Pamene alibe cholinga chopeza nzeruzo?*+ 17  Mnzako weniweni amakusonyeza chikondi nthawi zonse,+Ndipo ndi mʼbale amene anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.+ 18  Munthu wopanda nzeru amagwirana dzanja ndi munthu winaNdipo amalonjeza pamaso pa mnzake kuti iye akhala chikole.+ 19  Aliyense amene amakonda mikangano amakonda zolakwa.+ Aliyense woika khomo la nyumba yake pamwamba akudziitanira mavuto.+ 20  Munthu amene mtima wake ndi wopotoka zinthu sizidzamuyendera bwino,*+Ndipo amene amalankhula mwachinyengo adzagwera mʼmavuto. 21  Bambo amene wabereka mwana wopusa adzamva chisoni.Ndipo bambo wa mwana wopanda nzeru sasangalala.+ 22  Mtima wosangalala uli ngati mankhwala amene amachiritsa,+Koma munthu akakhumudwa mphamvu zake zimatha.*+ 23  Munthu woipa amalandira chiphuphu mobisa,Kuti akhotetse chilungamo.+ 24  Munthu wozindikira amakhala ndi cholinga choti apeze nzeru,Koma maso a munthu wopusa amangoyendayenda mpaka kumalekezero a dziko lapansi.+ 25  Mwana wopusa amamvetsa chisoni bambo ake,Komanso amapweteketsa mtima wa* mayi ake amene anamubereka.+ 26  Si bwino kulanga* munthu wolungama,Ndipo kukwapula anthu olemekezeka nʼkosayenera. 27  Munthu wodziwa zinthu amayamba waganiza asanalankhule,+Ndipo munthu wozindikira amapitiriza kukhala wodekha.+ 28  Ngakhale munthu wopusa amene wakhala chete adzaonedwa ngati wanzeru,Ndipo amene watseka pakamwa pake adzaonedwa ngati wozindikira.

Mawu a M'munsi

^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi nsembe zochuluka.”
^ Kapena kuti, “popanda phokoso.”
^ Kapena kuti, “makolo awo.”
^ Kapena kuti, “wolemekezeka.”
^ Kapena kuti, “mawu abwino.”
^ Kapena kuti, “Mphatso ndi mwala umene umachititsa kuti mwiniwake akomeredwe mtima.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amaphimba.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “kutsegulira madzi.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Pamene ali wopanda nzeru?”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “sadzapeza zabwino.”
^ Kapena kuti, “mafupa ake amauma.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amakwiyitsa.”
^ Kapena kuti, “kulipiritsa chindapusa.”