Machitidwe a Atumwi 2:1-47

  • Anthu analandira mzimu woyera pa Pentekosite (1-13)

  • Nkhani imene Petulo anakamba (14-36)

  • Anthu anatsatira zimene Petulo ananena (37-41)

    • Anthu 3,000 anabatizidwa (41)

  • Akhristu ankachitira zinthu limodzi (42-47)

2  Tsopano onse anali atasonkhana pamodzi pa tsiku la Chikondwerero cha Pentekosite.+  Mwadzidzidzi, kumwamba kunamveka mkokomo ngati wa mphepo yamphamvu, ndipo phokoso lake linadzaza mʼnyumba yonse imene iwo anali.+  Kenako anaona malilime ooneka ngati malawi amoto, ndipo anagawanika nʼkukhala pa aliyense wa iwo limodzilimodzi.  Ndiyeno onsewo anadzazidwa ndi mzimu woyera+ ndipo anayamba kulankhula zilankhulo zosiyanasiyana,* mogwirizana ndi mmene mzimuwo unawachititsira kulankhula.+  Pa nthawi imeneyo, Ayuda oopa Mulungu ochokera mʼmitundu yonse yapadziko lapansi ankakhala ku Yerusalemu.+  Choncho mkokomowu utamveka, panasonkhana gulu lalikulu la anthu. Iwo anadabwa kwambiri, chifukwa aliyense anawamva akulankhula mʼchilankhulo chake.  Zimenezi zinawadabwitsa kwambiri moti anayamba kufunsana kuti: “Anthuni, kodi onse akulankhulawa si anthu a ku Galileya?+  Ndiye zikutheka bwanji kuti aliyense pagulu lathuli akumva chilankhulo chake?  Pano pali Apati, Amedi+ ndi Aelamu.+ Palinso anthu ochokera ku Mesopotamiya, ku Yudeya, ku Kapadokiya, ku Ponto ndi kuchigawo cha Asia.+ 10  Pali anthu ochokera ku Fulugiya, ku Pamfuliya, ku Iguputo ndi kumadera a Libiya amene ali pafupi ndi Kurene. Palinso alendo ochokera ku Roma, omwe ndi Ayuda ndiponso anthu amene analowa Chiyuda.+ 11  Komanso pali Akerete ndi Aluya. Tonsefe tikuwamva akulankhula zinthu zazikulu za Mulungu mʼzilankhulo zathu.” 12  Onse anadabwa kwambiri ndipo anathedwa nzeru moti ankafunsana kuti: “Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?” 13  Koma ena ankawaseka nʼkumanena kuti: “Aledzera vinyo watsopano amenewa.” 14  Koma Petulo anaimirira pamodzi ndi atumwi 11 aja.+ Iye analankhula nawo mokweza mawu kuti: “Inu anthu a ku Yudeya ndi inu nonse a mu Yerusalemu, dziwani izi ndipo mvetserani mosamala zimene ndikufuna kukuuzani. 15  Sikuti anthuwa aledzera ngati mmene inu mukuganizira, chifukwa nthawi panopa ndi 9 koloko mʼmawa.* 16  Koma zimene zikuchitikazi ndi zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yoweli kuti: 17  ‘“Ndipo mʼmasiku otsiriza,” akutero Mulungu, “ndidzapereka* mzimu wanga kwa chamoyo chilichonse, ndipo ana anu aamuna ndi aakazi adzalosera. Anyamata adzaona masomphenya ndipo amuna achikulire adzalota maloto.+ 18  Ngakhale akapolo anga aamuna ndi aakazi, ndidzawapatsa mzimu wanga mʼmasiku amenewo ndipo iwo adzanenera.+ 19  Ndidzachita zodabwitsa kumwamba ndiponso zizindikiro padziko lapansi. Padzakhala magazi, moto ndi utsi wokwera mʼmwamba. 20  Dzuwa lidzasanduka mdima ndipo mwezi udzasanduka magazi. Zimenezi zidzachitika tsiku lalikulu ndiponso laulemerero la Yehova* lisanafike. 21  Ndipo aliyense woitana pa dzina la Yehova* adzapulumuka.”’+ 22  Amuna inu a mu Isiraeli, imvani mawu awa: Yesu wa ku Nazareti ndi munthu amene Mulungu anakuonetsani poyera. Anatero kudzera muntchito zamphamvu, zodabwitsa komanso zizindikiro, zimene Mulungu anachita pakati panu kudzera mwa iye,+ ngati mmene inunso mukudziwira. 23  Munthu ameneyu, amene anaperekedwa mwa kufuna kwa Mulungu+ ndi kudziwiratu kwake zamʼtsogolo, munachititsa kuti aphedwe pokhomeredwa pamtengo ndi anthu osamvera malamulo.+ 24  Koma Mulungu anamuukitsa+ pomumasula ku zopweteka* za imfa, chifukwa zinali zosatheka kuti imfa imugwire mwamphamvu.+ 25  Paja Davide ananena za iyeyu kuti, ‘Ndimaika Yehova* patsogolo panga nthawi zonse. Chifukwa iye ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka. 26  Pa chifukwa chimenechi mtima wanga unasangalala ndipo ndinalankhula mosangalala kwambiri. Komanso ine ndidzakhala ndi chiyembekezo, 27  chifukwa simudzandisiya* mʼManda,* ndipo simudzalola kuti thupi la wokhulupirika wanu livunde.*+ 28  Mwandidziwitsa njira za moyo, ndipo mudzachititsa kuti ndizisangalala kwambiri ndikakhala nanu pafupi.’*+ 29  Abale anga, ndilankhula ndithu momasuka za kholo lathu Davide. Iye anamwalira nʼkuikidwa mʼmanda,+ ndipo manda ake tili nawo mpaka lero. 30  Iye anali mneneri ndipo ankadziwa kuti Mulungu anamulonjeza polumbira, kuti pampando wake wachifumu adzakhazikapo mmodzi wa mbadwa zake.+ 31  Iye anadziwiratu zamʼtsogolo ndipo ananeneratu za kuuka kwa Khristu kuti sanasiyidwe mʼManda,* komanso thupi lake silinavunde.+ 32  Yesu ameneyo Mulungu anamuukitsa, ndipo tonsefe ndife mboni za nkhani imeneyi.+ 33  Iye anakwezedwa nʼkukhala kudzanja lamanja la Mulungu+ ndipo analandira mzimu woyera wolonjezedwawo kuchokera kwa Atate.+ Choncho iye watipatsa* mzimu woyera umene mukuuona ndi kuumvawu. 34  Ndipotu Davide sanapite kumwamba, koma iyeyo anati, ‘Yehova* anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja 35  mpaka nditaika adani ako kuti akhale chopondapo mapazi ako.”’+ 36  Choncho nyumba yonse ya Isiraeli idziwe ndithu kuti Yesu ameneyu, amene inu munamuphera pamtengo,+ Mulungu anamuika kukhala Ambuye+ ndi Khristu.” 37  Iwo atamva mawu amenewa, anavutika kwambiri mumtima ndipo anafunsa Petulo ndi atumwi enawo kuti: “Abale athu, tichite chiyani pamenepa?” 38  Petulo anawayankha kuti: “Lapani,+ ndipo aliyense abatizidwe+ mʼdzina la Yesu Khristu kuti machimo anu akhululukidwe.+ Mukatero mudzalandira mphatso yaulere ya mzimu woyera. 39  Chifukwa lonjezoli+ laperekedwa kwa inu, kwa ana anu ndiponso kwa anthu onse akutali, onse amene Yehova* Mulungu wathu angawasankhe.”+ 40  Ndipo ndi mawu enanso ambiri, Petulo anachitira umboni mokwanira. Komanso sanaleke kuwadandaulira kuti: “Dzipulumutseni ku mʼbadwo wa maganizo olakwikawu.”+ 41  Choncho amene analandira mawu akewo mosangalala anabatizidwa,+ moti tsiku limenelo chiwerengero cha ophunzirawo chinawonjezereka ndi anthu pafupifupi 3,000.+ 42  Choncho iwo anapitiriza kutsatira zimene atumwiwo ankaphunzitsa, kucheza,* kudyera limodzi+ komanso kupemphera.+ 43  Anthu onse anayamba kuchita mantha kwambiri ndipo atumwiwo anayamba kuchita zinthu zodabwitsa ndiponso zizindikiro zambiri.+ 44  Onse amene anakhala okhulupirira ankakhala limodzi ndipo ankagawana zinthu zonse zimene anali nazo. 45  Ankagulitsa malo awo ndi zinthu zina zimene anali nazo+ nʼkugawa kwa onse zimene apeza, mogwirizana ndi zimene aliyense akufunikira.+ 46  Tsiku lililonse ankasonkhana mʼkachisi mogwirizana. Ankaitanirana chakudya mʼnyumba zawo ndiponso ankagawana zakudya mosangalala komanso ndi mtima wonse. 47  Ankatamanda Mulungu ndiponso ankakondedwa ndi anthu onse. Komanso tsiku lililonse, Yehova* anapitiriza kuwonjezera anthu amene ankawapulumutsa.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “kulankhula malilime.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ola lachitatu,” kuwerenga kuchokera 6 koloko mʼmawa.
Kapena kuti, “ndidzatsanulira.”
Mabaibulo ena amati, “zingwe.”
Kapena kuti, “simudzasiya moyo wanga.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “liwole.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndikakhala pafupi ndi nkhope yanu.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “watitsanulira.”
Kapena kuti, “kugawana zinthu.”