Machitidwe a Atumwi 7:1-60

  • Zimene Sitefano ananena polankhula ndi Khoti Lalikulu la Ayuda (1-53)

    • Nthawi ya makolo akale (2-16)

    • Mose anali mtsogoleri; Aisiraeli ankalambira mafano (17-43)

    • Mulungu sakhala mu akachisi omangidwa ndi anthu (44-50)

  • Sitefano anaponyedwa miyala (54-60)

7  Koma mkulu wa ansembe anati: “Kodi zimenezi nʼzoona?”  Sitefano anati: “Anthu inu, abale anga ndi abambo anga, mvetserani. Mulungu waulemerero anaonekera kwa kholo lathu Abulahamu pamene anali ku Mesopotamiya, asanapite kukakhala ku Harana.+  Ndipo anamuuza kuti, ‘Samuka mʼdziko lako ndipo uchoke pakati pa abale ako. Upite kudziko limene ndidzakuonetse.’+  Choncho anasamuka mʼdziko la Akasidi nʼkukakhala ku Harana. Kumeneko, bambo ake atamwalira,+ Mulungu anamuuza kuti asamukire mʼdziko lino limene inu mukukhala panopa.+  Koma sanamʼpatsemo cholowa chilichonse, ngakhale kadera kakangʼono. Mʼmalomwake anamulonjeza kuti adzamupatsa dzikoli kuti likhale cholowa chake, ndi cha mbadwa* zake,+ ngakhale kuti pa nthawiyo analibe mwana.  Ndipo Mulungu anamuuzanso kuti mbadwa* zake zidzakhala alendo mʼdziko la eni, ndipo anthu adzawasandutsa akapolo ndi kuwazunza kwa zaka 400.+  Mulungu anati, ‘Ndidzaweruza mtundu umene adzautumikire monga akapolowo,+ ndipo kenako adzatuluka nʼkudzanditumikira pamalo ano.’+  Anamupatsanso pangano la mdulidwe.+ Kenako anabereka Isaki+ ndipo anamudula pa tsiku la 8.+ Nayenso Isaki anabereka* Yakobo ndipo Yakobo anabereka mitu ya mabanja 12 ija.  Mitu ya mabanjayo inachitira nsanje Yosefe+ nʼkumugulitsa ku Iguputo.+ Koma Mulungu anali naye,+ 10  ndipo anamupulumutsa mʼmavuto ake onse. Komanso ankamukonda ndipo ankamuthandiza kuti azichita zinthu mwanzeru pamaso pa Farao mfumu ya Iguputo. Faraoyo anapatsa Yosefe udindo woti aziyangʼanira Iguputo ndi nyumba yake yonse.+ 11  Kenako ku Iguputo ndi ku Kanani konse kunagwa njala moti kunali mavuto aakulu. Ndipo makolo athuwo sankapeza chakudya.+ 12  Koma Yakobo anamva kuti ku Iguputo kuli chakudya, ndipo anatuma makolo athu aja kwa nthawi yoyamba.+ 13  Pa ulendo wachiwiri Yosefe anadziulula kwa azichimwene ake, ndipo Farao anadziwa za abale ake a Yosefe ndi makolo ake.+ 14  Choncho Yosefe anatumiza anthu ku Kanani kukatenga bambo ake Yakobo ndiponso abale ake onse.+ Ndipo onse pamodzi analipo anthu 75.+ 15  Ndiyeno Yakobo anapita ku Iguputo+ kumene iye ndi makolo athu aja anafera.+ 16  Kenako mafupa awo anawatenga nʼkupita nawo ku Sekemu. Anakawaika mʼmanda amene Abulahamu anagula ndi ndalama zasiliva kwa ana a Hamori ku Sekemuko.+ 17  Nthawi itayandikira, yoti lonjezo limene Mulungu anapereka kwa Abulahamu likwaniritsidwe, mbadwa za Yakobo zinachuluka kwambiri ku Iguputo. 18  Kenako, mfumu ina yomwe sinkadziwa za Yosefe inayamba kulamulira ku Iguputo.+ 19  Mfumu imeneyi inachenjerera anthu a mtundu wathu komanso inakakamiza makolo athuwo kuti azitaya makanda awo nʼcholinga choti asakhale ndi moyo.+ 20  Mose anabadwa pa nthawi imeneyi, ndipo Mulungu ankamuona kuti ndi wokongola. Iye analeredwa mʼnyumba ya bambo ake kwa miyezi itatu.+ 21  Koma pamene anamusiya yekha,+ mwana wamkazi wa Farao anamutenga nʼkumamulera ngati mwana wake.+ 22  Choncho Mose anaphunzira nzeru zonse za Aiguputo. Iye ankalankhula mwamphamvu ndiponso ankachita zinthu zazikulu.+ 23  Atakwanitsa zaka 40, anaganiza zokaona* abale ake, Aisiraeli.+ 24  Ataona mmodzi wa abale akewo akuzunzidwa ndi munthu wa ku Iguputo, anamuteteza ndipo anabwezera popha munthu wa ku Iguputoyo. 25  Mose ankaganiza kuti abale akewo azindikira kuti Mulungu akuwapulumutsa pogwiritsa ntchito dzanja lake, koma iwo sanaizindikire mfundo imeneyi. 26  Tsiku lotsatira iye anapitanso kukawaona ndipo anapeza Aisiraeli ena akumenyana. Mose anayesa kuwathandiza kuti agwirizane ponena kuti, ‘Anthu inu, ndinu pachibale. Nʼchifukwa chiyani mukumenyana chonchi?’ 27  Koma amene ankamenya mnzakeyo anamukankha nʼkunena kuti, ‘Ndani anakupatsa udindo woti uzitilamulira komanso kutiweruza? 28  Kodi ukufuna kundipha ngati mmene unaphera munthu wa ku Iguputo dzulo lija?’ 29  Atamva zimenezi, Mose anathawa nʼkukakhala mʼdziko la Midiyani. Kumeneko anabereka ana aamuna awiri.+ 30  Patapita zaka 40, mngelo anaonekera kwa iye mʼchipululu paphiri la Sinai, pachitsamba chaminga chimene chinkayaka moto.+ 31  Mose ataona zimenezi, anadabwa kwambiri. Koma pamene ankayandikira kuti aonetsetse, anamva mawu a Yehova* akuti, 32  ‘Ine ndine Mulungu wa makolo ako, Mulungu wa Abulahamu, wa Isaki ndi wa Yakobo.’+ Mose anayamba kunjenjemera ndipo sanafunenso kupita pafupi ndi chitsambacho kuti akaonetsetse. 33  Yehova* anamuuza kuti, ‘Vula nsapato zako, chifukwa malo waimawo ndi malo oyera. 34  Ine ndaona kuti anthu anga omwe ali ku Iguputo akuzunzidwa kwambiri. Ndamva kubuula kwawo+ ndipo ndabwera kudzawapulumutsa. Ndiye ndikufuna ndikutume ku Iguputo.’ 35  Mose yemweyo, amene iwo anamukana nʼkunena kuti, ‘Ndani anakupatsa udindo woti uzitilamulira komanso kutiweruza?’+ ndi amene Mulungu anamutumiza+ ngati wolamulira ndi mpulumutsi kudzera mwa mngelo amene anaonekera kwa iye pachitsamba chaminga chija. 36  Munthu ameneyo anawatsogolera nʼkutuluka nawo+ ndipo anachita zodabwitsa ndi zizindikiro ku Iguputo,+ pa Nyanja Yofiira+ ndiponso mʼchipululu kwa zaka 40.+ 37  Ameneyu ndi Mose amene anauza Aisiraeli kuti, ‘Mulungu adzakupatsani mneneri ngati ine, kuchokera pakati pa abale anu.’+ 38  Ameneyu ndi amene anali ndi Aisiraeli mʼchipululu limodzi ndi mngelo+ amene analankhula ndi iyeyu+ komanso makolo athu paphiri la Sinai. Iye analandira mawu opatulika omwe ndi amphamvu kuti atipatsire.+ 39  Koma makolo athu anakana kumumvera. Mʼmalomwake, anamukankhira kumbali+ ndipo mumtima mwawo anabwerera ku Iguputo.+ 40  Anauza Aroni kuti, ‘Tipangire milungu kuti ititsogolere chifukwa sitikudziwa zimene zachitikira Mose, amene ankatitsogolera pochoka ku Iguputo.’+ 41  Choncho iwo anapanga fano la mwana wa ngʼombe mʼmasiku amenewo. Atatero anabweretsa nsembe zopereka kwa fanolo ndipo anasangalala ndi ntchito ya manja awo.+ 42  Choncho Mulungu anawasiya kuti atumikire magulu akumwamba+ ngati mmene malemba amanenera mʼbuku la Aneneri. Malembawo amati, ‘Anthu inu a nyumba ya Isiraeli, kodi mʼchipululu muja munkapereka kwa ine nsembe ndi zopereka zina kwa zaka 40? 43  Inutu munkanyamula chihema cha Moloki+ ndi nyenyezi ya mulungu wotchedwa Refani, mafano amene munapanga kuti muziwalambira. Choncho ndidzakuthamangitsirani kutali kupitirira ku Babulo.’+ 44  Makolo athuwo anali ndi chihema cha umboni mʼchipululu. Anachipanga potsatira malangizo amene Mulungu anapereka kwa Mose mogwirizana ndi chithunzi chimene Moseyo anachiona.+ 45  Makolo athu analandira chihemachi kwa makolo awo ndipo analowa nacho limodzi ndi Yoswa mʼdziko limene munali anthu a mitundu ina.+ Anthu amenewa Mulungu anawathamangitsa pamaso pa makolo athu+ ndipo chihemacho chinakhala mʼdzikoli mpaka nthawi ya Davide. 46  Mulungu anakomera mtima Davide ndipo iye anapempha mwayi woti amange nyumba yoti Mulungu wa Yakobo azikhalamo.+ 47  Koma Solomo ndi amene anamangira Mulungu nyumba.+ 48  Komabe Wamʼmwambamwamba sakhala mʼnyumba zomangidwa ndi manja,+ mogwirizana ndi mawu a mneneri akuti, 49  ‘Yehova* wanena kuti, Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu+ ndipo dziko lapansi ndi chopondapo mapazi anga.+ Ndiye kodi mungandimangire nyumba yotani? Ndipo malo oti ine ndingapumulirepo ali kuti? 50  Kodi si dzanja langa limene linapanga zinthu zonsezi?’+ 51  Anthu okanika inu ndiponso osachita mdulidwe wamumtima ndi mʼmakutu. Nthawi zonse mumatsutsana ndi mzimu woyera. Mukuchita zinthu ngati mmene ankachitira makolo anu.+ 52  Ndi mneneri uti amene makolo anuwo sanamuzunze?+ Iwo anapha anthu amene analengezeratu za kubwera kwa wolungamayo,+ amene inuyo munamupereka ndiponso kumupha.+ 53  Inu munalandira Chilamulo kudzera mwa angelo,+ koma osachitsatira.” 54  Atamva zimenezi, anakwiya koopsa ndipo anayamba kumukukutira mano. 55  Koma iye, atadzazidwa ndi mzimu woyera, anayangʼanitsitsa kumwamba ndipo anaona ulemerero wa Mulungu ndiponso Yesu ataima kudzanja lamanja la Mulungu.+ 56  Ndipo ananena kuti: “Taonani! Ndikuona kumwamba kutatseguka, ndipo Mwana wa munthu+ waima kudzanja lamanja la Mulungu.”+ 57  Iwo atamva zimenezi anafuula kwambiri atatseka mʼmakutu ndi manja awo, ndipo onse anathamangira pamene iye anali. 58  Kenako anamutulutsira kunja kwa mzinda nʼkuyamba kumuponya miyala.+ Ndipo mboni+ zinaika malaya awo akunja pafupi ndi mnyamata wina dzina lake Saulo.+ 59  Pamene ankamuponya miyala, Sitefano anapempha mochonderera kuti: “Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.” 60  Kenako anagwada nʼkufuula ndi mawu amphamvu kuti: “Yehova,* musawaimbe mlandu wa tchimo ili.”+ Atanena zimenezi anafa.*

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mabaibulo ena amati, “Isaki anachitanso chimodzimodzi ndi.”
Kapena kuti, “zokayendera.”
Kapena kuti, “anagona tulo ta imfa.”