Machitidwe a Atumwi 28:1-31

  • Anafika kugombe la ku Melita (1-6)

  • Bambo ake a Papuliyo anachiritsidwa (7-10)

  • Ulendo wa ku Roma (11-16)

  • Paulo analankhula ndi Ayuda ku Roma (17-29)

  • Paulo analalikira molimba mtima kwa zaka ziwiri (30, 31)

28  Titapulumuka choncho, tinamva kuti chilumbacho chimatchedwa Melita.+  Anthu olankhula chilankhulo chachilendo kumeneko anatisonyeza kukoma mtima kwapadera. Iwo anasonkha moto nʼkutilandira bwino tonse chifukwa kunkagwa mvula ndiponso kunkazizira.  Koma Paulo atatola nkhuni nʼkuziponya pamoto, panatuluka njoka ya mphiri chifukwa cha kutentha ndipo inamuluma nʼkukanirira kudzanja lake.  Anthu achilankhulo chachilendowo ataona njoka yapoizoni ikulendewera kudzanja lake, anayamba kuuzana kuti: “Ndithu munthu uyu ndi wopha anthu chifukwa ngakhale kuti wapulumuka panyanja, Chilungamo* sichinamulole kuti akhalebe ndi moyo.”  Koma iye anakutumulira njokayo pamoto ndipo sinamuvulaze.  Anthuwo ankayembekezera kuti atupa kapena agwa mwadzidzidzi nʼkufa. Koma atayembekezera kwa nthawi yaitali nʼkuona kuti palibe chimene chikumuchitikira, anasintha maganizo nʼkuyamba kunena kuti ndi mulungu.  Pafupi ndi malowa, panali minda ya munthu woyangʼanira chilumbacho, dzina lake Papuliyo. Iyeyu anatilandira bwino kwambiri ndipo anatichereza kwa masiku atatu.  Koma bambo ake a Papuliyo ankadwala malungo* komanso kamwazi ndipo anali chigonere. Choncho Paulo analowa mmene bambowo anali nʼkupemphera ndipo kenako anawagwira pamutu* nʼkuwachiritsa.+  Zitatero, anthu ena onse amene ankadwala pachilumbacho, anabwera kwa iye ndipo anawachiritsa.+ 10  Iwo anatilemekeza potipatsa mphatso zambiri, komanso pamene tinkanyamuka anatipatsa zinthu zambiri zimene tinkafunikira. 11  Patapita miyezi itatu, tinanyamuka pangalawa ya ku Alekizandiriya yokhala ndi chizindikiro cha “Ana a Zeu.” Ngalawa imeneyi inaima pachilumbapo poyembekezera kuti nyengo yozizira ithe. 12  Kenako tinafika padoko lina ku Surakusa ndipo tinakhalapo masiku atatu. 13  Titachoka kumeneko, tinazungulira nʼkukafika ku Regio. Patatha tsiku limodzi, kunayamba kuwomba mphepo yakumʼmwera ndipo tsiku lachiwiri tinafika ku Potiyolo. 14  Kumeneko tinapeza abale ndipo anatipempha kuti tikhale nawo masiku 7. Kenako tinapitiriza ulendo wathu wopita ku Roma. 15  Abale akumeneko atamva za ife, anabwera mpaka kudzafika ku Msika wa Apiyo ndi ku Nyumba Zitatu za Alendo kudzatichingamira. Paulo atawaona, anathokoza Mulungu ndipo analimba mtima.+ 16  Titafika ku Roma, Paulo analoledwa kumakhala yekha ndi msilikali womulondera. 17  Patatha masiku atatu, Paulo anaitanitsa akuluakulu a Ayuda. Atasonkhana, anawauza kuti: “Amuna inu, abale anga, ngakhale kuti sindinachite chilichonse chotsutsana ndi anthu kapena mwambo wa makolo athu,+ anandigwira ku Yerusalemu nʼkundipereka mʼmanja mwa Aroma ngati mkaidi.+ 18  Ndipo atafufuza,+ ankafuna kundimasula chifukwa sanandipeze ndi mlandu woyenera chilango cha imfa.+ 19  Koma Ayuda anatsutsa zimenezo moti ndinakakamizika kupempha kudzaonekera kwa Kaisara.+ Komatu sikuti ndinachita zimenezi chifukwa choti ndinkafuna kudzaneneza mtundu wanga. 20  Pa chifukwa chimenechi, ndinapempha kuti ndidzaonane nanu nʼkulankhula nanu, popeza ndamangidwa ndi unyolo uwu chifukwa cha chiyembekezo cha Aisiraeli.”+ 21  Iwo anamuyankha kuti: “Ife sitinalandire makalata alionse ochokera ku Yudeya onena za iwe. Palibenso aliyense wa abale amene afika kuno, amene watiuza kapena kulankhula choipa chilichonse chokhudza iwe. 22  Komabe tikufuna kumva maganizo ako, chifukwa kunena zoona, ife tonse timadziwa kuti gulu lampatuko limeneli+ amalinenera zoipa kwina kulikonse.”+ 23  Zitatero anapangana tsiku loti adzakumane naye ndipo anabweradi ambiri kumene iye ankakhala. Choncho kuyambira mʼmawa mpaka madzulo, anawafotokozera nkhani yonse ndipo anachitira umboni mokwanira za Ufumu wa Mulungu. Anachita zimenezi pogwiritsa ntchito mfundo zokopa zokhudza Yesu,+ kuchokera mʼChilamulo cha Mose+ ndi zimene aneneri analemba.+ 24  Ena anayamba kukhulupirira zimene Paulo ananenazo, koma ena sanakhulupirire. 25  Choncho, popeza ankatsutsana, anayamba kuchoka. Koma Paulo ananena mawu awa: “Mzimu woyera unanena zoona kwa makolo anu kudzera mwa Yesaya mneneri. 26  Mzimuwo unati, ‘Pita ukauze anthu awa kuti: “Kumva mudzamva ndithu, koma simudzazindikira. Kuyangʼana mudzayangʼana ndithu, koma simudzaona chilichonse.+ 27  Chifukwa anthu awa aumitsa mitima yawo ndipo amva ndi makutu awo, koma osalabadira. Atseka maso awo kuti asaone ndi maso awo komanso kuti asamve ndi makutu awo nʼkumvetsa tanthauzo lake mʼmitima yawo, kenako nʼkutembenuka kuti ine ndiwachiritse.”’+ 28  Choncho dziwani kuti njira ya Mulungu yopulumutsira anthu, yatumizidwa kwa anthu a mitundu ina.+ Ndipo mosakayikira, iwo adzamvetsera.”+ 29 *⁠—— 30  Choncho Paulo anakhalabe kwa zaka ziwiri zathunthu mʼnyumba yomwe ankapanga lendi,+ ndipo anthu onse omwe ankabwera kudzamuona ankawalandira ndi manja awiri. 31  Ankawalalikira za Ufumu wa Mulungu komanso kuwaphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu, ndi ufulu wonse wa kulankhula*+ popanda choletsa.

Mawu a M'munsi

MʼChigiriki Di′ke. Mawuwa mwina akunena za mulungu wamkazi wobwezera kuti chilungamo chioneke. Kapenanso anangowagwiritsa ntchito potanthauza chilungamo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “anatentha thupi.”
Kapena kuti, “anawaika manja.”
Kapena kuti, “molimba mtima kwambiri.”