Machitidwe a Atumwi 1:1-26

  • Mawu oyamba opita kwa Teofilo (1-5)

  • Kulalikira mpaka kumalekezero a dziko lapansi (6-8)

  • Yesu anapita kumwamba (9-11)

  • Ophunzira anasonkhana mogwirizana (12-14)

  • Matiya anasankhidwa kuti alowe mʼmalo mwa Yudasi (15-26)

1  A Teofilo, munkhani yoyamba ija, ndinalemba zinthu zonse zimene Yesu anachita ndiponso kuphunzitsa,+  mpaka tsiku limene anatengedwa kupita kumwamba,+ atapereka malangizo kudzera mwa mzimu woyera kwa atumwi amene iye anawasankha.+  Pambuyo pa mavuto amene anakumana nawo, iye anaonekera wamoyo kwa atumwiwo pogwiritsa ntchito maumboni ambiri otsimikizirika.+ Iwo anamuona masiku onse 40 ndipo ankawauza za Ufumu wa Mulungu.+  Pa nthawi imene anasonkhana ndi ophunzirawo, anawapatsa malangizo akuti: “Musachoke mu Yerusalemu,+ koma muyembekezere zimene Atate analonjeza,+ zomwe ndinakuuzani.  Chifukwa Yohane ankabatiza ndi madzi, koma inu mudzabatizidwa ndi mzimu woyera+ pasanathe masiku ambiri.”  Choncho atasonkhana, anamufunsa kuti: “Ambuye, kodi mubwezeretsa ufumu kwa Aisiraeli panopa?”+  Iye anawayankha kuti: “Simukufunika kudziwa nthawi kapena nyengo imene Atate wasankha mu ulamuliro wake.+  Koma mukadzalandira mzimu woyera, mudzakhala ndi mphamvu.+ Ndipo mudzakhala mboni+ zanga mu Yerusalemu,+ ku Yudeya konse ndi ku Samariya,+ mpaka kumalekezero* a dziko lapansi.”+  Atamaliza kulankhula zimenezi, anatengedwa kupita mumlengalenga iwo akuona, ndipo mtambo unamuphimba moti sanathenso kumuona.+ 10  Pamene iwo ankayangʼanitsitsa kumwamba, iye akukwera kumwambako, mwadzidzidzi azibambo awiri ovala zoyera+ anaima pambali pawo. 11  Azibambowo anawafunsa kuti: “Amuna inu a ku Galileya, nʼchifukwa chiyani mwangoima nʼkumayangʼana kumwamba? Yesu, amene watengedwa pakati panu kupita kumwambayu, adzabwera mʼnjira yofanana ndi mmene mwamuonera akupita kumwamba.” 12  Kenako anabwerera ku Yerusalemu,+ kuchokera kuphiri la Maolivi. Phiri limeneli lili pafupi ndi Yerusalemu, pa mtunda wa ulendo wa tsiku la sabata.* 13  Atafika mumzindawo anapita mʼchipinda chamʼmwamba, mmene ankakhala. Panali Petulo, Yohane, Yakobo, Andireya, Filipo, Tomasi, Batolomeyo, Mateyu, Yakobo mwana wa Alifeyo, Simoni wodzipereka uja komanso Yudasi mwana wa Yakobo.+ 14  Mogwirizana, onsewa ankalimbikira kupemphera pamodzi ndi Mariya mayi a Yesu, azimayi ena+ komanso azichimwene ake a Yesu.+ 15  Mʼmasiku amenewa, Petulo anaimirira pakati pa abalewo (gulu lonselo linali la anthu pafupifupi 120) nʼkunena kuti: 16  “Abale anga, zinali zofunika kuti lemba likwaniritsidwe, limene mzimu woyera unaneneratu kudzera mwa Davide. Lembali ndi lokhudza Yudasi,+ amene anatsogolera anthu okagwira Yesu.+ 17  Iye anali mmodzi wa ife,+ ndipo ankatumikira nafe limodzi. 18  (Munthu ameneyu, anagula munda ndi malipiro a ntchito zosalungama.+ Anagwa chamutu nʼkuphulika mimba ndipo matumbo ake onse anakhuthuka.+ 19  Izi zinadziwika kwa anthu onse a ku Yerusalemu, moti munda umenewo anaupatsa dzina la chilankhulo chawo lakuti A·kelʹda·ma, kutanthauza “Munda wa Magazi.”) 20  Mʼbuku la Masalimo analembamo kuti, ‘Malo ake okhala asanduke bwinja, ndipo pasapezeke aliyense wokhalamo,’+ komanso kuti, ‘Udindo wake monga woyangʼanira utengedwe ndi munthu wina.’+ 21  Choncho nʼkofunika kuti alowedwe mʼmalo ndi mmodzi mwa anthu amene ankayenda nafe pa nthawi yonse imene Ambuye Yesu ankachita zinthu zosiyanasiyana pakati pathu. 22  Munthu wake akhale amene ankayenda nafe kuyambira pamene Yesu anabatizidwa ndi Yohane,+ kudzafika tsiku limene anatengedwa kupita kumwamba kuchoka pakati pathu.+ Munthu ameneyu akhale mboni ya kuuka kwa Yesu pamodzi ndi ife.”+ 23  Choncho panatchulidwa anthu awiri, Yosefe wotchedwa Barasaba, amene amadziwikanso kuti Yusito, ndi Matiya. 24  Kenako anapemphera kuti: “Inu Yehova,* mumadziwa mitima ya anthu onse,+ tisonyezeni amene mwamusankha pa anthu awiriwa 25  kuti atenge malo amene Yudasi anawasiya nʼkuyenda njira zake ndipo atenge utumikiwu komanso akhale mtumwi.”+ 26  Atatero anachita maere+ ndipo maerewo anagwera Matiya. Choncho iye anamuphatikiza pa atumwi 11 aja.*

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “kumadera akutali.”
Ulendo umenewu unali wautali pafupifupi kilomita imodzi.
Kapena kuti, “ankaonedwa ngati atumwi ena 11 aja.”