Machitidwe a Atumwi 17:1-34

  • Paulo ndi Sila ku Tesalonika (1-9)

  • Paulo ndi Sila ku Bereya (10-15)

  • Paulo ku Atene (16-22a)

  • Zimene Paulo analankhula kubwalo la Areopagi (22b-34)

17  Kenako iwo anayenda kudutsa ku Amfipoli ndi ku Apoloniya ndipo anafika ku Tesalonika,+ kumene kunali sunagoge wa Ayuda.  Choncho mwachizolowezi chake,+ Paulo analowa mʼsunagogemo ndipo kwa milungu itatu anakambirana nawo mfundo za mʼMalemba.+  Iye ankafotokoza ndiponso kusonyeza umboni wolembedwa powatsimikizira kuti zinali zoyenera kuti Khristu avutike,+ kenako auke.+ Ankanena kuti: “Yesu amene ndikumulalikira kwa inu, ndiye Khristu.”  Pamapeto pake, ena mwa iwo anakhala okhulupirira ndipo anagwirizana ndi Paulo ndi Sila.+ Agiriki ambiri opembedza Mulungu komanso azimayi ambiri olemekezeka anachitanso chimodzimodzi.  Koma Ayuda anachita nsanje+ ndipo anasonkhanitsa anthu ena oipa amene ankangokhala pamsika. Iwowa anapanga gulu lachiwawa nʼkuyambitsa chipolowe mumzindamo. Kenako anapita kunyumba ya Yasoni, kukafuna Paulo ndi Sila kuti awatulutse nʼkuwapereka ku gulu limene linkachita chipolowelo.  Atalephera kuwapeza, anakokera Yasoni ndi abale ena kwa olamulira a mzindawo, akufuula kuti: “Anthu awa, amene ayambitsa mavuto kwina konseku, tsopano akupezekanso kuno.+  Ndipo Yasoni wawalandira ngati alendo ake. Anthu onsewa akuchita zotsutsana ndi malamulo a Kaisara. Eti akunena kuti kulinso mfumu ina dzina lake Yesu.”+  Atanena mawu amenewa, gulu la anthu lija komanso olamulira a mzindawo anakwiya kwambiri.  Olamulira a mzindawo analipiritsa Yasoni ndi enawo ndalama,* kenako anawamasula. 10  Kutangoda, abale anatulutsa Paulo ndi Sila nʼkuwatumiza ku Bereya. Iwo atafika kumeneko, analowa mʼsunagoge wa Ayuda. 11  Koma anthu a ku Bereya anali a mtima wofuna kuphunzira kuposa a ku Tesalonika aja. Iwowa analandira mawu a Mulungu ndi chidwi chachikulu kwambiri, ndipo tsiku ndi tsiku ankafufuza Malemba mosamala kuti atsimikizire ngati zimene anamvazo zinalidi zoona. 12  Ambiri mwa anthu amenewa anakhala okhulupirira, chimodzimodzinso akazi ndi amuna ena otchuka a Chigiriki. 13  Koma Ayuda ochokera ku Tesalonika atamva kuti Paulo akufalitsanso mawu a Mulungu ku Bereya, anapitanso kumeneko kukachititsa anthu kuti akwiyire atumwiwo nʼkuyambitsa chipolowe.+ 14  Nthawi yomweyo abale anatumiza Paulo kuti apite kunyanja.+ Koma Sila ndi Timoteyo anatsala komweko. 15  Ndipo anthu amene anaperekeza Paulo anakamufikitsa ku Atene. Koma anabwerera atatumidwa kuti akauze Sila ndi Timoteyo+ kuti atsatire Pauloyo mwamsanga. 16  Pamene Paulo ankawayembekezera ku Atene, mtima unamuwawa kwambiri poona kuti mumzindawo mwadzaza mafano. 17  Atalowa mʼsunagoge anayamba kukambirana ndi Ayuda ndi anthu ena opembedza Mulungu. Ndipo tsiku ndi tsiku ankakambirananso ndi anthu amene ankawapeza pamsika. 18  Koma anthu ena anzeru za Epikureya ndi Sitoiki anayamba kutsutsana naye. Ena ankanena kuti: “Kodi nayenso wobwetuka uyu akufuna kunena chiyani?” Pomwe ena ankanena kuti: “Akuoneka kuti akulalikira za milungu yachilendo.” Ankanena zimenezi chifukwa chakuti Paulo ankalengeza uthenga wabwino wa Yesu ndi za kuuka kwa akufa.+ 19  Choncho anamugwira nʼkupita naye kubwalo la Areopagi nʼkumuuza kuti: “Kodi tingadziweko za chiphunzitso chatsopano chimene ukuphunzitsachi? 20  Chifukwatu zimene ukufotokozazi ndi zinthu zachilendo mʼmakutu mwathu. Ndiye tikufuna tidziwe tanthauzo lake.” 21  Ndipotu anthu onse a ku Atene ndi alendo ogonera kumeneko, ankathera nthawi yawo yonse yopuma akufotokoza kapena kumvetsera nkhani zatsopano. 22  Tsopano Paulo anaima pakati pa bwalo la Areopagi+ nʼkunena kuti: “Inu anthu a ku Atene, ndaona kuti pa zinthu zonse mumaopa kwambiri milungu* kuposa mmene ena amachitira.+ 23  Mwachitsanzo, pamene ndimadutsa nʼkumayangʼanitsitsa zinthu zimene mumalambira, ndapezanso guwa lansembe lolembedwa kuti, ‘Kwa Mulungu Wosadziwika.’ Choncho ine ndikulalikira kwa inu za Mulungu wosadziwika amene mukumulambirayo. 24  Mulungu amene anapanga dzikoli ndi zinthu zonse zili mmenemu, sakhala mu akachisi opangidwa ndi manja.+ Iye ndiye Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi.+ 25  Komanso satumikiridwa ndi manja a anthu ngati kuti amasowa kanthu,+ chifukwa ndi iyeyo amene amapatsa anthu onse moyo, mpweya+ ndi zinthu zonse. 26  Ndipo kuchokera mwa munthu mmodzi+ anapanga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale padziko lonse lapansi.+ Iye anaika nthawi yoti zinthu zina zizichitika komanso anaika malire a malo oti anthu azikhala.+ 27  Anachita zimenezi kuti anthuwo afunefune Mulungu, amufufuzefufuze nʼkumupezadi,+ ngakhale kuti kwenikweni, iye sali kutali ndi aliyense wa ife. 28  Paja chifukwa cha iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo, ngati mmene andakatulo anu ena ananenera kuti, ‘Paja ndife ana ake.’* 29  Choncho, popeza ndife ana a Mulungu,+ tisaganize kuti Mulunguyo ali ngati golide, siliva, mwala kapena chilichonse chosemedwa ndi anthu aluso.+ 30  Nʼzoona kuti Mulungu analekerera nthawi yomwe anthu sankadziwa zinthu,+ koma tsopano akuuza anthu kwina kulikonse kuti onse alape. 31  Chifukwa wakhazikitsa tsiku limene akufuna kudzaweruza+ mwachilungamo dziko lonse lapansi, kudzera mwa munthu amene iye wamusankha. Ndipo watsimikizira anthu onse zimenezi pomuukitsa.”+ 32  Ndiyeno anthuwo atamva za kuuka kwa akufa, ena anayamba kuseka mwachipongwe,+ pomwe ena anati: “Chabwino, udzatiuzenso zimenezi nthawi ina.” 33  Choncho Paulo anawasiya. 34  Koma anthu ena anakhala kumbali yake ndipo anakhala otsatira a Yesu. Ena mwa iwo anali Diyonisiyo, woweruza mʼbwalo la Areopagi, mayi wina dzina lake Damarisi komanso anthu ena.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “ndalama za belo.”
Kapena kuti, “ndinu opembedza kwambiri.”
Kapena kuti, “mbadwa zake.”