Machitidwe a Atumwi 21:1-40

  • Ulendo wa ku Yerusalemu (1-14)

  • Anafika ku Yerusalemu (15-19)

  • Paulo anatsatira malangizo a akulu (20-26)

  • Chisokonezo mʼkachisi; Paulo anamangidwa (27-36)

  • Paulo analoledwa kulankhula ndi gulu la anthu (37-40)

21  Titadzikakamiza nʼkusiyana nawo, tinayamba ulendo wathu wapanyanja. Tinayenda osakhota mpaka kukafika ku Ko. Tsiku lotsatira tinafika ku Rode ndipo titachoka kumeneko tinakafika ku Patara.  Kumeneko tinapeza ngalawa imene inkawoloka kupita ku Foinike ndipo tinakwera nʼkunyamuka.  Chilumba cha Kupuro chitayamba kuonekera, tinachisiya kumanzere* nʼkupitiriza ulendo wathu kulowera ku Siriya. Kenako tinaima ku Turo kuti katundu atsitsidwe mʼngalawa.  Tinafufuza ophunzira ndipo titawapeza tinakhala nawo masiku 7. Koma mouziridwa ndi mzimu, iwo anauza Paulo mobwerezabwereza kuti asayerekeze kupita ku Yerusalemu.+  Masiku athu okhala kumeneko atatha, tinanyamuka kuti tipitirize ulendo wathu. Abale onse komanso azimayi ndi ana, anatiperekeza mpaka kunja kwa mzindawo. Kumeneko tinagwada mʼmbali mwa nyanja nʼkupemphera.  Kenako tinatsanzikana ndipo ife tinakwera ngalawa, koma iwo anabwerera kunyumba kwawo.  Choncho tinanyamuka ku Turo pangalawa ndipo tinafika ku Tolemayi. Kumeneko tinapereka moni kwa abale nʼkukhala nawo tsiku limodzi.  Tsiku lotsatira tinanyamuka nʼkukafika ku Kaisareya ndipo tinapita kunyumba kwa mlaliki wina dzina lake Filipo. Iyeyu anali mmodzi wa amuna 7+ a mbiri yabwino aja, ndipo tinakhala naye.  Filipo anali ndi ana aakazi 4 osakwatiwa,* amene ankanenera.+ 10  Koma titakhala masiku ndithu, mneneri wina dzina lake Agabo+ anabwera kuchokera ku Yudeya. 11  Iye anafika kwa ife nʼkutenga lamba wa Paulo. Kenako anadzimanga mapazi ndi manja nʼkunena kuti: “Mzimu woyera wati, ‘Mwiniwake wa lambayu, Ayuda adzamumanga chonchi ku Yerusalemu+ nʼkumupereka kwa anthu a mitundu ina.’”+ 12  Titamva zimenezi, ife ndi anthu amene anali kumeneko, tinayamba kuchonderera Paulo kuti asapite ku Yerusalemu. 13  Koma Paulo anayankha kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukulira ndiponso kufuna kundifooketsa? Inetu ndine wokonzeka osati kumangidwa kokha, komanso kukafa ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.”+ 14  Titalephera kumusintha maganizo, tinasiya kumuletsa* nʼkunena kuti: “Chifuniro cha Yehova* chichitike.” 15  Kenako tinakonzeka nʼkunyamuka ulendo wopita ku Yerusalemu. 16  Koma ophunzira ena a ku Kaisareya ananyamuka nafe kuti atiperekeze kunyumba kwa Mnaso wa ku Kupuro, kuti tikafikire kumeneko. Munthu ameneyu anali mmodzi wa ophunzira oyambirira. 17  Titafika ku Yerusalemu, abale anatilandira mosangalala. 18  Koma tsiku lotsatira, Paulo anapita nafe kwa Yakobo,+ ndipo akulu onse anali komweko. 19  Paulo anawapatsa moni nʼkuyamba kuwafotokozera mwatsatanetsatane zimene Mulungu anachitira anthu a mitundu ina kudzera mu utumiki wake. 20  Iwo atamva zimenezi anayamba kutamanda Mulungu, komabe anamuuza kuti: “Mʼbale, pali Ayuda ambiri okhulupirira ndipo onsewa ndi odzipereka pa nkhani yotsatira Chilamulo.+ 21  Komatu iwo anamva mphekesera zakuti iwe wakhala ukuphunzitsa Ayuda onse amene ali pakati pa anthu a mitundu ina kuti asiye kutsatira Chilamulo cha Mose. Akuti ukuwauza kuti asamachitenso mdulidwe wa ana awo komanso asamatsatire miyambo imene takhala tikuitsatira kuyambira kalekale.+ 22  Ndiye titani pamenepa? Sitikukayikira kuti iwo adzamva kuti iwe wabwera. 23  Choncho uchite zimene tikuuze: Tili ndi amuna 4 amene anachita lumbiro. 24  Utenge anthu amenewa ndipo ukachite nawo mwambo wa kudziyeretsa. Uwalipirire zonse zofunika, kuti amete tsitsi lawo. Ukatero, aliyense adziwa kuti mphekesera zimene anamva za iwe ndi nkhambakamwa chabe. Adzaona kuti ukuchita zinthu motsatira dongosolo komanso kuti umasunga Chilamulo.+ 25  Koma okhulupirira ochokera mʼmitundu inawo, tinawatumizira kalata yonena za chigamulo chathu chakuti apewe zoperekedwa nsembe kwa mafano+ komanso magazi,+ zopotola*+ ndi chiwerewere.”*+ 26  Choncho tsiku lotsatira, Paulo anatenga amunawo nʼkukachita nawo mwambo wa kudziyeretsa.+ Kenako analowa mʼkachisi, kukanena pamene masiku awo a mwambo wa kudziyeretsa adzathere ndiponso pamene adzapereke nsembe ya aliyense. 27  Masiku 7 atatsala pangʼono kutha, Ayuda ochokera ku Asia anaona Paulo ali mʼkachisi. Choncho anachititsa kuti pagulu lonse la anthu payambike chisokonezo ndipo anamugwira. 28  Iwo ankafuula kuti: “Inu Aisiraeli, tithandizeni! Munthu uyu akuphunzitsa zotsutsana ndi anthu a mtundu wathu kulikonse. Iyeyu akuphunzitsanso zotsutsana ndi Chilamulo komanso malo ano. Kuwonjezera pamenepo, watenga Agiriki nʼkuwalowetsa mʼkachisi ndipo waipitsa malo oyerawa.”+ 29  Iwo ananena zimenezi chifukwa tsiku lina anaona Terofimo+ wa ku Efeso ali naye limodzi mumzindawo ndiye anaganiza kuti Paulo analowetsa Terofimo mʼkachisi. 30  Choncho mumzinda wonsewo munali chisokonezo ndipo anthu anathamangira kukachisiko. Kenako anagwira Paulo nʼkumukokera kunja kwa kachisi. Nthawi yomweyo zitseko zinatsekedwa. 31  Pamene ankafuna kumupha, uthenga unafika kwa mkulu wa gulu la asilikali kuti mu Yerusalemu monse muli chisokonezo. 32  Nthawi yomweyo, iye anatenga asilikali ndi atsogoleri awo nʼkuthamangira kumeneko. Anthuwo ataona mkulu wa asilikali uja pamodzi ndi asilikali akewo, anasiya kumenya Paulo. 33  Zitatero mkulu wa asilikaliyo anafika pafupi nʼkumugwira ndipo analamula kuti amumange ndi maunyolo awiri.+ Kenako anafunsa anthu zokhudza iyeyo komanso zimene wachita. 34  Koma ena pagululo anayamba kufuula zinthu zina, ena zina. Choncho atalephera kutolapo mfundo yeniyeni chifukwa cha phokoso, analamula kuti apite naye kumpanda wa asilikali. 35  Atafika pamasitepe, asilikaliwo anachita kumunyamula chifukwa choti gululo linkachita zachiwawa. 36  Anthuwo ankawatsatira, akufuula kuti: “Aphedwe ameneyo!” 37  Koma atatsala pangʼono kulowa naye kumpanda wa asilikali, Paulo anapempha mkulu wa asilikali kuti: “Kodi mungandilole kuti ndilankhule nanu pangʼono?” Iye anati: “Kani umalankhula Chigiriki? 38  Ndiye kuti si iwe munthu wa ku Iguputo amene masiku apitawo unayambitsa chipolowe choukira boma nʼkutsogolera zigawenga 4,000 kupita nazo mʼchipululu?” 39  Paulo anayankha kuti: “Inetu ndine Myuda+ wa ku Tariso,+ ku Kilikiya, nzika ya mzinda wotchuka. Chonde ndikukupemphani, ndiloleni ndilankhule kwa anthuwa.” 40  Atamulola, Paulo anaimirira pamasitepe nʼkukwezera anthuwo dzanja. Onse atakhala chete, analankhula nawo mʼChiheberi+ kuti:

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mbali imene kunali doko.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “omwe anali anamwali.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “tinakhala chete.”
Kapena kuti, “nyama imene yaphedwa osazinga kuti magazi atuluke.” Ena amati kusinga.
MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.