Machitidwe a Atumwi 13:1-52

  • Baranaba ndi Saulo anatumizidwa kuti akakhale amishonale (1-3)

  • Utumiki wa ku Kupuro (4-12)

  • Zimene Paulo analankhula ku Antiokeya wa ku Pisidiya (13-41)

  • Ulosi woti ayambe kulalikira kwa anthu a mitundu ina (42-52)

13  Mumpingo wa ku Antiokeya munali aneneri ndi aphunzitsi.+ Iwo anali Baranaba, Sumiyoni wotchedwa Nigeri, Lukiyo wa ku Kurene, Saulo ndiponso Manayeni amene anaphunzira pamodzi ndi Herode wolamulira chigawo.  Pamene iwo ankatumikira Yehova* ndiponso kusala kudya, mzimu woyera unawauza kuti: “Mundipatulire Baranaba ndi Saulo+ kuti agwire ntchito imene ndinawaitanira.”+  Atamaliza kusala kudya ndiponso kupemphera, anawagwira pamutu* nʼkuwalola kuti apite.  Choncho anthu amenewa, omwe anatumizidwa ndi mzimu woyera, anapita ku Selukeya ndipo kuchokera kumeneko anayenda ulendo wapamadzi kupita ku Kupuro.  Atafika mumzinda wa Salami anayamba kulalikira mawu a Mulungu mʼmasunagoge a Ayuda. Iwo analinso ndi Yohane yemwe ankawatumikira.*+  Iwo anayenda pachilumba chonse cha Kupuro mpaka kukafika ku Pafo. Kumeneko anakumana ndi Myuda wina wamatsenga dzina lake Bara-Yesu, yemwe analinso mneneri wabodza.  Iyeyu anali limodzi ndi bwanamkubwa Serigio Paulo, yemwe anali munthu wanzeru. Bwanamkubwayu anaitana Baranaba ndi Saulo, chifukwa ankafunitsitsa kumva mawu a Mulungu.  Koma Elima, wamatsenga, (chifukwa dzina lakeli amalimasulira chonchi) anayamba kutsutsana nawo. Iye ankayesetsa kuti bwanamkubwayo asakhulupirire Ambuye.  Koma Saulo, wotchedwanso Paulo, atadzazidwa ndi mzimu woyera, anamuyangʼanitsitsa 10  nʼkunena kuti: “Iwe munthu wodzaza ndi chinyengo chamtundu uliwonse ndiponso zoipa, mwana wa Mdyerekezi+ komanso mdani wa chinthu chilichonse cholungama, kodi udzasiya liti kupotoza njira zowongoka za Yehova?* 11  Tsopano tamvera! Dzanja la Yehova* lili pa iwe ndipo ukhala wakhungu. Kwakanthawi, suthanso kuona kuwala kwa dzuwa.” Nthawi yomweyo anaona nkhungu* yamphamvu mʼmaso mwake ndiponso mdima wandiweyani, ndipo anayamba kufufuza anthu oti amugwire dzanja ndi kumutsogolera. 12  Bwanamkubwa uja ataona zimenezi, anakhala wokhulupirira, chifukwa anadabwa kwambiri ndi zimene anaphunzira zokhudza Yehova.* 13  Kenako Paulo ndi anzakewo, anayamba ulendo wa panyanja kuchoka ku Pafo, ndipo anakafika ku Pega, ku Pamfuliya. Koma Yohane+ anawasiya nʼkubwerera ku Yerusalemu.+ 14  Atachoka ku Pega anakafika ku Antiokeya wa ku Pisidiya. Kumeneko analowa mʼsunagoge+ tsiku la Sabata nʼkukhala pansi. 15  Chilamulo ndi zimene aneneri analemba zitawerengedwa pamaso pa anthu,+ atsogoleri a sunagoge anatuma munthu kukawauza kuti: “Abale inu, ngati muli ndi mawu alionse amene angalimbikitse anthuwa, lankhulani.” 16  Choncho Paulo anaimirira ndipo anakweza dzanja lake nʼkunena kuti: “Anthu inu, Aisiraeli, ndiponso ena nonsenu amene mumaopa Mulungu, tamverani. 17  Mulungu wa anthu awa Aisiraeli, anasankha makolo athu akale. Pamene iwo ankakhala mʼdziko lachilendo la Iguputo, iye anawasandutsa mtundu wamphamvu, ndipo anawatulutsa mʼdzikomo ndi dzanja lake lamphamvu.+ 18  Kwa zaka pafupifupi 40, iye anapirira khalidwe lawo mʼchipululu.+ 19  Ndipo atawononga mitundu 7 ya anthu mʼdziko la Kanani, anapereka dzikolo kwa Aisiraeli kuti likhale cholowa chawo.+ 20  Zonsezi zinachitika mʼzaka pafupifupi 450. Zimenezi zitatha anawapatsa oweruza mpaka kudzafika pa nthawi ya mneneri Samueli.+ 21  Koma kenako anthuwo ananena kuti akufuna mfumu.+ Choncho Mulungu anawapatsa Sauli mwana wa Kisi, munthu wa fuko la Benjamini,+ ndipo anakhala mfumu yawo kwa zaka 40. 22  Atamuchotsa ameneyu, anawapatsa Davide kuti akhale mfumu yawo.+ Iyeyu Mulungu anamuchitira umboni kuti, ‘Ndapeza Davide mwana wa Jese,+ munthu wapamtima panga.+ Ameneyu adzachita zonse zimene ndikufuna.’ 23  Mogwirizana ndi lonjezo lake, kuchokera pa mbadwa* za munthu ameneyu, Mulungu wabweretsa mpulumutsi mu Isiraeli, amene ndi Yesu.+ 24  Mpulumutsi ameneyu asanafike, Yohane analalikira kwa anthu onse a ku Isiraeli za ubatizo, ngati chizindikiro cha kulapa.+ 25  Koma pamene Yohane ankamaliza utumiki wake, ankanena kuti, ‘Kodi mukuganiza kuti ndine ndani? Amene mukumuganizirayo si ine ayi. Koma wina akubwera pambuyo panga, amene ine si woyenera kumasula nsapato zake.’+ 26  Anthu inu, abale anga, inu mbadwa za Abulahamu, ndi anthu onse oopa Mulungu amene muli nawo pamodziwa, mawu a chipulumutso chimenechi atumizidwa kwa ife.+ 27  Chifukwa anthu a ku Yerusalemu ndi olamulira awo sanamuzindikire. Koma pamene ankamuweruza, anakwaniritsa zimene aneneri ananena,+ zomwe zimawerengedwa mokweza sabata lililonse. 28  Ngakhale kuti sanapeze chifukwa chomuphera,+ anaumiriza Pilato kuti ameneyu aphedwe.+ 29  Ndiyeno atakwaniritsa zinthu zonse zimene zinalembedwa zokhudza iyeyo, anamutsitsa pamtengo nʼkumuika mʼmanda.*+ 30  Koma Mulungu anamuukitsa.+ 31  Ndipo kwa masiku ambiri anaonekera kwa anthu amene anayenda naye kuchokera ku Galileya kupita ku Yerusalemu. Panopa amenewa ndi mboni zake kwa anthu.+ 32  Choncho ife tikulengeza kwa inu uthenga wabwino wonena za zinthu zimene makolo athu analonjezedwa. 33  Uthengawo ndi wakuti Mulungu wakwaniritsa zonse zimene anawalonjezazo kwa ife ana awo poukitsa Yesu,+ mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mu salimo lachiwiri kuti: ‘Iwe ndiwe mwana wanga. Lero ine ndakhala bambo ako.’+ 34  Ndipo mfundo yakuti iye anamuukitsa ndipo sangabwererenso kuthupi limene limavunda,* anaifotokoza chonchi: ‘Ine ndidzakusonyezani anthu inu chikondi chokhulupirika chimene ndinalonjeza Davide. Lonjezo limeneli ndi lodalirika.’+ 35  Ndipo salimo lina limanenanso kuti, ‘Simudzalola kuti thupi la wokhulupirika wanu livunde.’+ 36  Davide anachita chifuniro cha Mulungu pa nthawi ya mʼbadwo wake, anamwalira nʼkuikidwa mʼmanda a makolo ake ndipo thupi lake linavunda.+ 37  Koma amene Mulungu anamuukitsa uja thupi lake silinavunde.+ 38  Tsopano dziwani abale anga kuti, ife tikulalikira kwa inu za kukhululukidwa kwa machimo kudzera mwa ameneyu.+ 39  Dziwaninso kuti pa zinthu zonse zimene kunali kosatheka kuti muonedwe opanda mlandu kudzera mʼChilamulo cha Mose,+ aliyense wokhulupirira akuonedwa wopanda mlandu kudzera mwa iyeyu.+ 40  Choncho samalani kuti zimene aneneri analemba zisakugwereni, zomwe zimati: 41  ‘Inu onyoza onani zimene ine ndikuchita nʼkudabwa nazo. Kenako mudzatha, chifukwa simudzakhulupirira ngakhale pangʼono zimene ndidzachite mʼmasiku anu, ngakhale wina atakufotokozerani mwatsatanetsatane.’”+ 42  Tsopano pamene ankatuluka, anthu anawachonderera kuti adzawafotokozerenso nkhani zimenezi Sabata lotsatira. 43  Choncho msonkhano wamʼsunagoge utatha, Ayuda ndi anthu ambiri omwe analowa Chiyuda amene ankalambira Mulungu anatsatira Paulo ndi Baranaba. Ndipo iwo anauza anthuwo kuti apitirize kukhala oyenera kulandira kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.+ 44  Sabata lotsatira, pafupifupi mzinda wonse unasonkhana kudzamvetsera mawu a Yehova.* 45  Ayuda ataona gulu la anthulo, anachita nsanje ndipo anayamba kutsutsa mwamwano zimene Paulo ankalankhula.+ 46  Choncho Paulo ndi Baranaba analankhula molimba mtima kuti: “Inu munali oyenera kuti muyambe kuuzidwa mawu a Mulungu.+ Koma popeza mukuwakana ndipo mukudziweruza nokha kuti ndinu osayenera moyo wosatha, ife tikupita kwa anthu a mitundu ina.+ 47  Ndipotu Yehova* watilamula kuti, ‘Ndakupatsani udindo woti mukhale kuwala kwa anthu a mitundu ina, kuti mukhale chipulumutso mpaka kumalekezero a dziko lapansi.’”+ 48  Anthu a mitundu inawo atamva zimenezi, anasangalala ndipo anatamanda mawu a Yehova.* Anthu onse amene anali ndi maganizo abwino amene akanawathandiza kukapeza moyo wosatha anakhala okhulupirira. 49  Komanso, mawu a Yehova* anapitiriza kufalitsidwa mʼdziko lonselo. 50  Koma Ayuda anauza zoipa amayi otchuka oopa Mulungu komanso amuna olemekezeka amumzindawo. Choncho iwo anachititsa kuti Paulo ndi Baranaba ayambe kuzunzidwa+ ndipo anawaponya kunja kwa mzinda wawo. 51  Koma Paulo ndi Baranaba anasansa fumbi kumapazi awo kuti ukhale umboni wowatsutsa nʼkupita ku Ikoniyo.+ 52  Ndipo ophunzirawo anapitiriza kukhala osangalala+ komanso mzimu woyera unkawathandiza kwambiri.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “anawaika manja.”
Kapena kuti, “ankawathandiza.”
Ena amati “chifunga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Kapena kuti, “mʼmanda achikumbutso.”
Kapena kuti, “limawola.”