1 Mbiri 28:1-21

  • Zimene Davide ananena zokhudza kumanga kachisi (1-8)

  • Solomo anapatsidwa malangizo komanso mapulani omangira (9-21)

28  Kenako Davide anasonkhanitsa akalonga onse a Isiraeli ku Yerusalemu. Akalongawo anali a mafuko ndi a magulu+ otumikira mfumu, atsogoleri a magulu a anthu 1,000, atsogoleri a magulu a anthu 100+ ndiponso atsogoleri oyangʼanira katundu yense ndi ziweto zonse za mfumu+ ndi za ana ake.+ Panalinso nduna zapanyumba ya mfumu ndiponso mwamuna aliyense wamphamvu ndi wodalirika.+  Kenako Mfumu Davide anaimirira nʼkunena kuti: “Ndimvereni inu abale anga ndi anthu anga. Ineyo ndinafunitsitsa kumanga nyumba yoti likasa la pangano la Yehova lizikhalamo ndiponso yoti ikhale ngati chopondapo mapazi cha Mulungu wathu+ ndipo ndinakonzekera kuti ndiimange.+  Koma Mulungu woona anandiuza kuti: ‘Iwe sumanga nyumba ya dzina langa,+ chifukwa wamenya nkhondo zambiri ndiponso wapha anthu ambiri.’+  Komabe, mʼnyumba yonse ya bambo anga Yehova Mulungu wa Isiraeli anasankha ineyo kuti ndikhale mfumu ya Isiraeli mpaka kalekale,+ chifukwa anasankha Yuda kuti akhale mtsogoleri.+ Mʼnyumba ya Yuda anasankhamo nyumba ya bambo anga.+ Pa ana a bambo anga anavomereza ineyo kuti ndikhale mfumu ya Aisiraeli onse.+  Ndipo pa ana anga onse (poti Yehova wandipatsa ana ambiri)+ anasankha mwana wanga Solomo+ kuti akhale pampando wachifumu wa ufumu wa Yehova, kuti alamulire Isiraeli.+  Anandiuza kuti: ‘Mwana wako Solomo ndi amene adzamange nyumba yanga ndiponso mabwalo anga, chifukwa ndamusankha kuti akhale mwana wanga ndipo ine ndidzakhala bambo ake.+  Akamatsatira malamulo anga ndi ziweruzo zanga+ ndi mtima wonse ngati mmene akuchitira panopa, ndidzakhazikitsa ufumu wake ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.’+  Tsopano ndikulankhula pamaso pa Aisiraeli onse, amene ndi mpingo wa Yehova, ndiponso Mulungu wathu akumva zimenezi: Muzifufuza ndi kutsatira mosamala malamulo onse a Yehova Mulungu wanu, kuti dziko labwinoli likhale lanu+ ndi kuti mudzasiyire ana anu obwera pambuyo panu monga cholowa chawo mpaka kalekale.  Ndipo iwe Solomo mwana wanga, dziwa Mulungu wa bambo wako ndipo uzimutumikira ndi mtima wonse+ komanso mosangalala, chifukwa Yehova amafufuza mitima yonse+ ndipo amazindikira maganizo a munthu ndi zolinga zake zonse.+ Ukamufunafuna, adzalola kuti umupeze,+ koma ukamusiya iye adzakusiya mpaka kalekale.+ 10  Tsopano taona, Yehova wakusankha kuti umange nyumba yopatulika yoti azikhalamo. Limba mtima ndipo ugwire ntchitoyi.” 11  Atatero, Davide anapatsa Solomo mwana wake mapulani akamangidwe+ ka khonde+ ndi nyumba zake, zipinda zake zosungiramo katundu, zipinda zake zapadenga, zipinda zake zamkati ndiponso nyumba yokhalamo chivundikiro chophimbira machimo.+ 12  Anamupatsanso mapulani a kamangidwe ka zonse zimene anauzidwa kudzera mwa mzimu zokhudza mabwalo+ a nyumba ya Yehova, zipinda zonse zodyera kuzungulira kachisi, mosungira chuma cha nyumba ya Mulungu woona ndi mosungira zinthu zimene anaziyeretsa kuti zikhale zopatulika.+ 13  Komanso anamʼpatsa malangizo okhudza magulu a ansembe+ ndi a Alevi, ntchito yonse yokhudza utumiki wapanyumba ya Yehova ndiponso malangizo okhudza ziwiya zonse za utumiki wapanyumba ya Yehova. 14  Anamuuzanso kulemera kwa golide, golide wa ziwiya zonse za ntchito zosiyanasiyana ndi siliva wa ziwiya zonse zasiliva za ntchito zosiyanasiyana; 15  kulemera kwa zoikapo nyale zagolide+ ndi nyale zake zagolide, kulemera kwa zoikapo nyale zosiyanasiyana ndi nyale zake, kulemera kwa zoikapo nyale zasiliva komanso kulemera kwa choikapo nyale chilichonse ndi nyale zake mogwirizana ndi ntchito zake; 16  kulemera kwa golide wa tebulo iliyonse yoikapo mkate wosanjikiza*+ ndiponso siliva wa matebulo asiliva; 17  mafoloko, mbale zolowa, mitsuko yagolide woyenga bwino, kulemera kwa mbale iliyonse yagolide yaingʼono yolowa+ komanso kulemera kwa mbale iliyonse yasiliva yaingʼono yolowa. 18  Anamuuzanso za kulemera kwa golide woyengedwa bwino wa guwa lansembe la zofukiza+ ndiponso golide wa chifaniziro cha galeta,+ kutanthauza akerubi+ agolide otambasula mapiko awo kuphimba likasa la pangano la Yehova. 19  Davide anati: “Dzanja la Yehova linali pa ine ndipo anandithandiza kuti ndidziwe zonse zokhudza mapulani a kamangidwe kake+ nʼkuwalemba.”+ 20  Kenako Davide anauza Solomo mwana wake kuti: “Limba mtima ndipo ugwire ntchitoyi mwamphamvu. Usaope kapena kuchita mantha chifukwa Yehova Mulungu, Mulungu wanga, ali nawe.+ Sadzakutaya kapena kukusiya+ mpaka ntchito yonse yokhudza utumiki wa nyumba ya Yehova itatha. 21  Tsopano ndikukupatsa magulu a ansembe+ ndi a Alevi+ ogwira ntchito zonse zapanyumba ya Mulungu woona. Uli ndi amisiri odzipereka komanso aluso amene angagwire ntchito iliyonse+ ndiponso akalonga+ ndi anthu onse amene angatsatire malangizo ako onse.”

Mawu a M'munsi

Umenewu unali mkate wachionetsero.