1 Mbiri 16:1-43
16 Choncho anabweretsa Likasa la Mulungu woona pamalo amene Davide anakonza nʼkuliika mutenti imene iye anamanga kuti lizikhalamo.+ Kenako iwo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamgwirizano kwa Mulungu woona.+
2 Davide atamaliza kupereka nsembe zopsereza+ ndi nsembe zamgwirizano,+ anadalitsa anthu mʼdzina la Yehova.
3 Komanso anapatsa Aisiraeli onse mikate yozungulira, makeke a zipatso za kanjedza ndi makeke a mphesa. Anapereka zimenezi kwa aliyense, mwamuna ndiponso mkazi.
4 Kenako Davide anaika Alevi ena kuti azitumikira kumene Likasa la Yehova+ linkakhala ndiponso kuti azilemekeza,* kuyamika komanso kutamanda Yehova Mulungu wa Isiraeli.
5 Mtsogoleri wawo anali Asafu,+ wachiwiri wake anali Zekariya. Ndipo Yeyeli, Semiramoti, Yehiela, Matitiya, Eliyabu, Benaya, Obedi-edomu ndi Yeyeli+ ankaimba ndi zoimbira za zingwe ndiponso azeze.+ Asafu ankaimba zinganga.+
6 Benaya ndi Yahazieli, omwe anali ansembe, ankaimba malipenga nthawi zonse patsogolo pa likasa la pangano la Mulungu woona.
7 Pa tsiku limeneli mʼpamene Davide kwa nthawi yoyamba anathandiza nawo kuimba nyimbo yothokoza Yehova kudzera mwa Asafu+ ndi abale ake yakuti:
8 “Yamikani Yehova,+ itanani pa dzina lake,Dziwitsani mitundu ya anthu ntchito zake!+
9 Muimbireni, muimbireni nyimbo* zomutamanda,+Ganizirani mozama* ntchito zake zonse zodabwitsa.+
10 Nyadirani dzina lake loyera.+
Mitima ya anthu ofunafuna Yehova isangalale.+
11 Funafunani Yehova+ ndipo muzidalira mphamvu zake.
Nthawi zonse muzimupempha kuti akuthandizeni.*+
12 Kumbukirani ntchito zodabwitsa zimene wachita,+Kumbukirani zozizwitsa zake ndi ziweruzo zimene wanena,
13 Inu mbadwa* za Isiraeli mtumiki wake,+Inu ana a Yakobo, osankhidwa ake.+
14 Iye ndi Yehova Mulungu wathu.+
Ziweruzo zake zili padziko lonse lapansi.+
15 Kumbukirani pangano lake mpaka kalekale,Lonjezo limene anapereka ku mibadwo 1,000,+
16 Kumbukirani pangano limene anapangana ndi Abulahamu,+Komanso lumbiro limene analumbira kwa Isaki.+
17 Pangano limene analikhazikitsa monga lamulo kwa Yakobo,+Komanso monga pangano lokhalapo mpaka kalekale kwa Isiraeli,
18 Pamene anati: ‘Ndidzakupatsa dziko la Kanani,+Kuti likhale cholowa chako.’+
19 Pamene ankanena zimenezi nʼkuti inu mulipo ochepa,Nʼkuti mulipo ochepa kwambiri komanso muli alendo mʼdzikolo.+
20 Iwo ankayendayenda kuchokera ku mtundu wina kupita ku mtundu wina,Komanso kuchokera mu ufumu wina kupita kwa anthu a mtundu wina.+
21 Mulungu sanalole kuti munthu aliyense awapondereze,+Koma anadzudzula mafumu chifukwa cha iwo.+
22 Iye anati: ‘Musakhudze odzozedwa anga,Ndipo aneneri anga musawachitire choipa chilichonse.’+
23 Dziko lonse lapansi liimbire Yehova!
Tsiku ndi tsiku muzilengeza za chipulumutso chake!+
24 Lengezani ulemerero wake pakati pa anthu a mitundu ina,Lengezani ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu.
25 Chifukwa Yehova ndi wamkulu komanso woyenera kutamandidwa,
Iye ndi wochititsa mantha kwambiri kuposa milungu ina yonse.+
26 Milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi milungu yopanda pake.+Koma Yehova ndi amene anapanga kumwamba.+
27 Pamene amakhala pali ulemu ndi ulemerero,+Pokhala pake pali mphamvu ndi chimwemwe.+
28 Mʼpatseni Yehova zimene akuyenera kulandira, inu mabanja a mitundu ya anthu,Mʼpatseni Yehova zimene akuyenera kulandira chifukwa cha ulemerero ndi mphamvu zake.+
29 Mʼpatseni Yehova ulemerero woyenera dzina lake,+Bweretsani mphatso pamaso pake.+
Weramirani* Yehova mutavala zovala zokongola ndi zopatulika.+
30 Dziko lonse lapansi linjenjemere pamaso pake!
Dziko lapansi lakhazikika moti silingasunthidwe.*+
31 Kumwamba kukondwere ndipo dziko lapansi lisangalale,+Lengezani kwa anthu a mitundu ina kuti: ‘Yehova wakhala Mfumu!’+
32 Nyanja ichite mkokomo ndi zonse zimene zili mmenemo,Mtunda, ndi zonse zili mmenemo, zikondwere.
33 Pa nthawi imodzimodziyo mitengo yamʼnkhalango ifuule mosangalala pamaso pa Yehova,Chifukwa iye akubwera* kudzaweruza dziko lapansi.
34 Yamikani Yehova chifukwa iye ndi wabwino,+Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.+
35 Nenani kuti: ‘Tipulumutseni, inu Mulungu wachipulumutso chathu,+Tisonkhanitseni ndi kutipulumutsa kwa anthu a mitundu ina,Kuti titamande dzina lanu loyera,+Ndiponso kuti tikutamandeni mosangalala.+
36 Atamandidwe Yehova Mulungu wa Isiraeli,Atamandidwe mpaka kalekale.’”
Ndiyeno anthu onse ananena kuti, “Ame!”* ndipo anatamanda Yehova.
37 Kenako Davide anasiya Asafu+ ndi abale ake kumeneko pamaso pa likasa la pangano la Yehova, kuti azitumikira nthawi zonse kumene Likasalo linkakhala,+ mogwirizana ndi zofunika kuchita pa tsikulo.+
38 Anasiyanso Obedi-edomu ndi abale ake okwana 68. Ndipo Obedi-edomu mwana wa Yedutuni ndi Hosa anali alonda apageti.
39 Zadoki+ wansembe ndi ansembe anzake anawasiya kuchihema cha Yehova chimene chinali pamalo okwezeka a ku Gibiyoni,+
40 Anawasiya kuti azipereka nsembe zopsereza kwa Yehova nthawi zonse paguwa lansembe zopsereza, mʼmawa ndi madzulo, mogwirizana ndi zonse zolembedwa mʼChilamulo cha Yehova chimene analamula Aisiraeli.+
41 Iwowa anali limodzi ndi Hemani ndi Yedutuni+ ndiponso amuna onse amene anawasankha mochita kuwatchula mayina kuti azithokoza Yehova,+ chifukwa “chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.”+
42 Hemani+ ndi Yedutuni anawasiya kuti aziimba malipenga, zinganga ndi zipangizo zina zimene ankagwiritsa ntchito potamanda Mulungu woona* ndipo ana a Yedutuni+ anali alonda apageti.
43 Kenako anthu onse anapita kunyumba kwawo. Nayenso Davide anapita kunyumba kwake kukadalitsa banja lake.
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “azikumbukira.”
^ Kapena kuti, “mupekereni nyimbo.”
^ Mabaibulo ena amati, “Nenani zokhudza.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “muzifunafuna nkhope yake.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
^ Kapena kuti, “Lambirani.”
^ Kapena kuti, “silingagwedezeke.”
^ Kapena kuti, “wabwera.”
^ Kapena kuti, “Zikhale momwemo!”
^ Kapena kuti, “zipangizo zina zoimbira nyimbo ya Mulungu woona.”