Wolembedwa ndi Yohane 3:1-36

  • Yesu ndi Nikodemo (1-21)

    • Kubadwanso (3-8)

    • Mulungu anakonda dziko (16)

  • Umboni womaliza wa Yohane wokhudza Yesu (22-30)

  • Wochokera kumwamba (31-36)

3  Panali Mfarisi wina dzina lake Nikodemo,+ wolamulira wa Ayuda.  Iyeyu anapita kwa Yesu usiku+ nʼkumuuza kuti: “Rabi,+ tikudziwa kuti inu ndi mphunzitsi wochokera kwa Mulungu, chifukwa palibe munthu amene angathe kuchita zizindikiro+ zimene inu mumachita ngati Mulungu sali naye.”+  Poyankha Yesu anamuuza kuti: “Ndithudi ndikukuuza, munthu sangathe kuona Ufumu wa Mulungu+ ngati sangabadwenso.”*+  Nikodemo anafunsa kuti: “Munthu angabadwe bwanji ali wamkulu kale? Kodi angathe kulowa mʼmimba mwa mayi ake nʼkubadwanso?”  Yesu anayankha kuti: “Ndithudi ndikukuuza, munthu sangathe kulowa mu Ufumu wa Mulungu ngati atapanda kubadwa mwa madzi+ ndi mzimu.+  Chimene chabadwa kuchokera mʼthupi nʼchanyama, ndipo chimene chabadwa kuchokera mumzimu nʼchauzimu.  Usadabwe chifukwa ndakuuza kuti: Anthu inu muyenera kubadwanso.  Mphepo imawombera kumene ikufuna ndipo munthu amamva mkokomo wake, koma sadziwa kumene ikuchokera ndi kumene ikupita. Nʼchimodzimodzi ndi aliyense amene wabadwa kuchokera mumzimu.”+  Poyankha Nikodemo anati: “Zimenezi zingatheke bwanji?” 10  Yesu anamufunsa kuti: “Kodi si paja ndiwe mphunzitsi wa Isiraeli, ndiye zikutheka bwanji kuti usadziwe zinthu zimenezi? 11  Ndithudi ndikukuuza, zimene ife tikudziwa timazilankhula, ndipo zimene taona timazichitira umboni. Koma inu simulandira umboni umene timapereka. 12  Ngati ndakuuzani zinthu zapadziko lapansi koma inu simukukhulupirirabe, ndiye mungakhulupirire bwanji nditakuuzani zinthu zakumwamba? 13  Ndipotu palibe munthu amene anakwera kumwamba+ koma Mwana wa munthu yekha, amene anatsika kuchokera kumwambako.+ 14  Mofanana ndi Mose amene anakweza njoka mʼmwamba mʼchipululu,+ Mwana wa munthunso akuyenera kukwezedwa mʼmwamba+ 15  kuti aliyense womukhulupirira akhale ndi moyo wosatha.+ 16  Chifukwa Mulungu anakonda kwambiri dziko moti anapereka Mwana wake wobadwa yekha,+ kuti aliyense womukhulupirira asawonongedwe koma akhale ndi moyo wosatha.+ 17  Mulungu sanatumize Mwana wake mʼdziko kuti mwanayo adzaweruze dziko, koma kuti dzikolo lipulumutsidwe kudzera mwa iye.+ 18  Aliyense amene amamukhulupirira sayenera kuweruzidwa.+ Aliyense amene samukhulupirira waweruzidwa kale, chifukwa sanakhulupirire mʼdzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.+ 19  Kuwala kwafika mʼdziko+ koma mʼmalo mokonda kuwala anthu akukonda mdima popeza ntchito zawo nʼzoipa, nʼchifukwa chake adzaweruzidwe. 20  Amene amachita zinthu zoipa amadana ndi kuwala ndipo safika pamene pali kuwala, kuti ntchito zake zisaonekere.* 21  Koma aliyense amene amachita zinthu zabwino amabwera pamene pali kuwala,+ kuti ntchito zake zionekere kuti anazichita mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.” 22  Zimenezi zitatha Yesu ndi ophunzira ake anapita mʼdera lakumudzi la ku Yudeya. Iye anakhala nawo kumeneko kwa kanthawi ndipo ankabatiza anthu.+ 23  Koma Yohane nayenso ankabatiza anthu ku Ainoni pafupi ndi Salimu, chifukwa kumeneko kunali madzi ambiri+ ndipo anthu ankapita kukabatizidwa.+ 24  Pa nthawiyi nʼkuti Yohane asanamutsekere mʼndende.+ 25  Tsopano ophunzira a Yohane anayamba kukangana ndi Myuda wina pa nkhani yokhudza kukhala oyera pamaso pa Mulungu. 26  Pambuyo pake anapita kwa Yohane nʼkumuuza kuti: “Rabi, munthu amene munali naye kutsidya kwa Yorodano uja, amene munkamuchitira umboni uja,+ iyenso akubatiza ndipo anthu onse akupita kwa iye.” 27  Poyankha Yohane anati: “Munthu sangalandire kanthu kalikonse pokhapokha atapatsidwa kuchokera kumwamba. 28  Inunso ndinu mboni pa zimene ndinanena kuti, ‘Ine si Khristu,+ koma ndinatumizidwa monga kalambulabwalo wake.’+ 29  Munthu amene ali ndi mkwatibwi ndi mkwati.+ Koma mnzake wa mkwati, akaimirira ndi kumvetsera zimene akunena, amasangalala kwambiri chifukwa cha mawu a mkwatiyo. Choncho ine ndikusangalala kwambiri. 30  Iyeyo akuyenera kumawonjezereka, koma ine ndikuyenera kumacheperachepera.” 31  Wochokera kumwamba+ amaposa ena onse. Wochokera padziko lapansi ndi wapadziko lapansi ndipo amalankhula zinthu zapadziko lapansi. Koma wochokera kumwamba ndi woposa ena onse.+ 32  Iye akuchitira umboni zinthu zimene waziona ndi kuzimva,+ koma palibe munthu amene akukhulupirira umboni wake.+ 33  Amene wakhulupirira umboni wakewo watsimikizira* kuti Mulungu amanena zoona.+ 34  Amene anatumidwa ndi Mulungu amalankhula mawu a Mulungu,+ chifukwa Iye akafuna kupereka mzimu sapereka moumira.* 35  Atate amakonda Mwana+ ndipo anapereka zinthu zonse mʼmanja mwake.+ 36  Amene amakhulupirira Mwanayo adzalandira moyo wosatha.+ Wosamvera Mwanayo sadzalandira moyowu,+ koma mkwiyo wa Mulungu udzakhalabe pa iye.+

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “ngati sangabadwe kuchokera kumwamba.”
Kapena kuti, “zisadzudzulidwe.”
Kapena kuti, “waika chidindo chake pa umboniwo.”
Kapena kuti, “akafuna kupereka mzimu sachita kuyeza pamuyezo.”