Wolembedwa ndi Yohane 18:1-40

  • Yudasi anapereka Yesu (1-9)

  • Petulo anagwiritsa ntchito lupanga (10, 11)

  • Yesu anamupititsa kwa Anasi (12-14)

  • Petulo anakana Yesu koyamba (15-18)

  • Yesu anaonekera pamaso pa Anasi (19-24)

  • Petulo anakana Yesu kachiwiri ndi kachitatu (25-27)

  • Yesu anaonekera pamaso pa Pilato (28-40)

    • “Ufumu wanga si wamʼdzikoli” (36)

18  Atamaliza kunena zinthu zimenezi, Yesu anatuluka limodzi ndi ophunzira ake nʼkuwoloka chigwa cha Kidironi+ kupita kumene kunali munda. Iye ndi ophunzira akewo analowa mʼmundamo.+  Yudasi amene anamupereka uja, ankawadziwanso malowo chifukwa nthawi zambiri Yesu ankakumana ndi ophunzira ake kumeneko.  Choncho Yudasi anatenga gulu la asilikali komanso alonda ochokera kwa ansembe aakulu ndi kwa Afarisi. Iwo anafika kumeneko atanyamula miyuni, nyale ndi zida.+  Popeza Yesu ankadziwa zonse zimene zimuchitikire, anawayandikira nʼkuwafunsa kuti: “Mukufuna ndani?”  Iwo anamuyankha kuti: “Yesu Mnazareti.”+ Iye anati: “Ndi ineyo.” Yudasi amene anamupereka uja, analinso pomwepo.+  Koma pamene anawauza kuti: “Ndi ineyo,” iwo anabwerera mʼmbuyo nʼkugwa pansi.+  Kenako anawafunsanso kuti: “Mukufuna ndani?” Iwo anati: “Yesu Mnazareti.”  Yesu anati: “Ndakuuzani kuti ndi ineyo. Choncho ngati mukufuna ine, awa asiyeni azipita.”  Zimenezi zinachitika kuti mawu amene iye ananena akwaniritsidwe akuti: “Pa anthu onse amene munandipatsa sindinatayepo ngakhale mmodzi.”+ 10  Kenako Simoni Petulo, amene anali ndi lupanga, analisolola nʼkutema nalo kapolo wa mkulu wa ansembe mpaka kuduliratu khutu lake lakumanja.+ Kapoloyo dzina lake anali Makasi. 11  Koma Yesu anauza Petulo kuti: “Bwezera lupangalo mʼchimake.+ Kodi sindiyenera kumwa zamʼkapu imene Atate wandipatsa?”+ 12  Kenako asilikali aja, mkulu wa asilikali ndi alonda a Ayuda anagwira Yesu nʼkumumanga. 13  Choyamba anapita naye kwa Anasi, chifukwa anali mpongozi wa Kayafa,+ amene anali mkulu wa ansembe chaka chimenecho.+ 14  Kayafa ameneyu ndi amene analangiza Ayuda uja kuti zinali zothandiza kwa iwo kuti munthu mmodzi afere anthu onse.+ 15  Ndiyeno Simoni Petulo komanso wophunzira wina ankatsatira Yesu.+ Wophunzira winayo ankadziwana ndi mkulu wa ansembe, choncho analowa limodzi ndi Yesu mʼbwalo lapanyumba ya mkulu wa ansembe. 16  Koma Petulo anaima kunja pakhomo. Choncho wophunzira amene ankadziwana ndi mkulu wa ansembe uja, anapita kukalankhula ndi mlonda wapakhomo nʼkumulowetsa Petulo. 17  Mtsikana wantchito amene anali mlonda wa pakhomopo anafunsa Petulo kuti: “Kodi inunso si mmodzi wa ophunzira a munthu ameneyu?” Iye anati: “Ayi si ine.”+ 18  Ndiyeno akapolo ndi alonda anali ataima chapafupi ndi moto wamakala umene anakoleza, chifukwa kunkazizira ndipo ankawotha motowo. Nayenso Petulo anaima nawo limodzi nʼkumawotha motowo. 19  Ndiyeno wansembe wamkulu anafunsa Yesu za ophunzira ake komanso zimene ankaphunzitsa. 20  Yesu anamuyankha kuti: “Ndalankhula poyera ku dzikoli. Nthawi zonse ndinkaphunzitsa mʼmasunagoge ndi mʼkachisi,+ kumene Ayuda onse ankasonkhana, ndipo sindinalankhule chilichonse kumbali. 21  Nʼchifukwa chiyani mukufunsa ine? Funsani amene anamva zimene ndinkawauza. Onani! Onsewa akudziwa zimene ndinanena.” 22  Atanena zimenezi, mmodzi wa alonda amene anaima chapafupi anamenya Yesu mbama+ nʼkunena kuti: “Ungamuyankhe choncho wansembe wamkulu?” 23  Yesu anamuyankha kuti: “Ngati ndanena chilichonse cholakwika, pereka umboni wa cholakwikacho. Koma ngati zimene ndanenazi ndi zoona, nʼchifukwa chiyani wandimenya?” 24  Kenako Anasi anatumiza Yesu kwa Kayafa mkulu wa ansembe ndipo anali atamumanga.+ 25  Pa nthawiyi Simoni Petulo anali ataima pomwepo nʼkumawotha moto. Ndiyeno iwo anamufunsa kuti: “Kodi iwenso si mmodzi wa ophunzira ake?” Iye anakana nʼkunena kuti: “Ayi si ine.”+ 26  Mmodzi wa akapolo a mkulu wa ansembe, amenenso anali wachibale wa munthu amene Petulo anamudula khutu uja,+ anati: “Ndinakuona mʼmunda muja uli naye limodzi, ndikunama kapena?” 27  Koma Petulo anakananso ndipo nthawi yomweyo tambala analira.+ 28  Ndiyeno iwo anatenga Yesu kuchoka kwa Kayafa nʼkupita naye kunyumba ya bwanamkubwa.+ Umenewu unali mʼmawa kwambiri. Koma iwo sanalowe mʼnyumba ya bwanamkubwayo poopa kudetsedwa.+ Iwo ankafuna kuti akathe kudya Pasika. 29  Choncho Pilato anatuluka nʼkuwafunsa kuti: “Kodi mukumuimba mlandu wanji munthu ameneyu?” 30  Iwo anamuyankha kuti: “Munthuyu akanakhala kuti sachita zoipa,* sitikanabwera naye kwa inu.” 31  Ndiyeno Pilato anawauza kuti: “Mutengeni mukamuweruze nokha mogwirizana ndi chilamulo chanu.”+ Ayudawo anamuuza kuti: “Tilibe ulamuliro wopha munthu aliyense.”+ 32  Zimenezi zinachitika kuti mawu amene Yesu ananena osonyeza mmene adzafere, akwaniritsidwe.+ 33  Choncho Pilato analowanso mʼnyumba ya bwanamkubwa nʼkuitana Yesu ndipo anamufunsa kuti: “Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda?”+ 34  Yesu anayankha kuti: “Kodi mukufunsa zimenezi chifukwa mukufunadi kudziwa, kapena chifukwa chakuti ena akuuzani za ine?” 35  Pilato anayankha kuti: “Kodi ine ndine Myuda ngati? Anthu a mtundu wako omwe komanso ansembe aakulu ndi amene akupereka kwa ine. Kodi unachita chiyani?” 36  Yesu anayankha kuti:+ “Ufumu wanga si wamʼdzikoli.+ Ufumu wanga ukanakhala wamʼdzikoli, atumiki anga akanamenya nkhondo kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda.+ Koma Ufumu wanga si wochokera mʼdzikoli.” 37  Pilato anamufunsa kuti: “Chabwino, koma kodi ndiwe mfumu?” Yesu anayankha kuti: “Mukunena nokha kuti ndine mfumu.+ Ndinabadwa komanso ndinabwera mʼdziko kuti ndidzachitire umboni choonadi.+ Aliyense amene ali kumbali ya choonadi amamvetsera mawu anga.” 38  Pilato anamufunsa kuti: “Choonadi nʼchiyani?” Atangofunsa funso limeneli anatuluka nʼkupitanso kumene kunali Ayuda kuja, ndipo anawauza kuti: “Ineyo sindikupeza cholakwa chilichonse mwa munthu ameneyu.+ 39  Pajanso inu muli ndi mwambo wakuti ndizikumasulirani munthu mmodzi pa Pasika.+ Ndiye kodi mukufuna kuti ndikumasulireni Mfumu ya Ayuda?” 40  Anthuwo anafuulanso kuti: “Ameneyo ayi, koma Baraba!” Komatu Baraba ameneyu anali wachifwamba.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “akanakhala kuti si chigawenga.”