Wolembedwa ndi Yohane 1:1-51

  • Mawu anakhala munthu (1-18)

  • Umboni umene Yohane Mʼbatizi anapereka (19-28)

  • Yesu ndi Mwanawankhosa wa Mulungu (29-34)

  • Ophunzira oyambirira a Yesu (35-42)

  • Filipo komanso Natanayeli (43-51)

1  Pachiyambi, panali wina amene ankadziwika kuti Mawu,+ ndipo Mawuyo anali ndi Mulungu+ komanso Mawuyo anali mulungu.*+ 2  Ameneyu anali ndi Mulungu kuyambira pachiyambi. 3  Zinthu zonse zinakhalako kudzera mwa iye+ ndipo palibe chinthu ngakhale chimodzi chimene chinakhalapo popanda iyeyo. 4  Moyo unakhalapo kudzera mwa iye ndipo moyowo unali kuwala kounikira anthu.+ 5  Kuwalako kukuunika mumdima+ koma mdimawo sunagonjetse kuwalako. 6  Kunabwera munthu wina amene anatumidwa monga nthumwi ya Mulungu. Dzina lake anali Yohane.+ 7  Munthu ameneyu anabwera ngati mboni, kuti adzachitire umboni za kuwala+ nʼcholinga chakuti anthu osiyanasiyana akhulupirire kudzera mwa iye. 8  Sikuti iyeyu anali kuwalako,+ koma anangobwera kudzachitira umboni za kuwalako. 9  Kuwala kwenikweni kumene kumaunikira anthu osiyanasiyana kunali kutatsala pangʼono kubwera mʼdziko.+ 10  Iye anali mʼdziko+ ndipo dziko linakhalapo kudzera mwa iye,+ koma dzikolo silinamudziwe. 11  Anabwera kudziko lakwawo, koma anthu akwawo enieniwo sanamulandire. 12  Komabe onse amene anamulandira, anawapatsa mphamvu kuti akhale ana a Mulungu,+ chifukwa choti ankakhulupirira dzina lake.+ 13  Iwowa sanabadwe kuchokera mwa anthu kapena chifukwa cha kufuna kwa anthu kapenanso chifukwa cha kufuna kwa munthu, koma anabadwa kuchokera kwa Mulungu.+ 14  Choncho Mawu ameneyo anakhala ndi thupi la nyama+ ndipo ankakhala pakati pathu. Ife tinaona ulemerero wake, ulemerero wofanana ndi umene mwana wobadwa yekha+ amalandira kuchokera kwa bambo ake. Mulungu ankamukomera mtima kwambiri* komanso ankaphunzitsa choonadi. 15  (Yohane ankachitira umboni za iye, moti ankachita kufuula kuti: “Uyu ndi amene ndinkanena uja kuti, ‘Amene akubwera mʼmbuyo mwangamu ndi wamkulu kuposa ine, chifukwa anakhalapo ine ndisanabadwe.’”)+ 16  Chifukwa chakuti anali ndi kukoma mtima kwakukulu, nthawi zonse tinkalandira kukoma mtima kwakukulu kosefukira. 17  Popeza Chilamulo chinaperekedwa kudzera mwa Mose,+ kukoma mtima kwakukulu+ komanso choonadi zinakhalako kudzera mwa Yesu Khristu.+ 18  Palibe munthu amene anaonapo Mulungu ndi kale lonse,+ mulungu wobadwa yekha+ amene ali pambali pa Atate*+ ndi amene anafotokoza za Mulungu.+ 19  Yohane anapereka umboni pamene Ayuda anatumiza ansembe ndi Alevi kuchokera ku Yerusalemu kukamufunsa kuti: “Kodi ndiwe ndani?”+ 20  Iye anavomera ndipo sanakane. Ananena kuti: “Ine si Khristu.” 21  Iwo anamufunsa kuti: “Nanga ndiwe ndani? Ndiwe Eliya kapena?”+ Iye anayankha kuti: “Ayi.” “Kapena ndiwe Mneneri?”+ Iye anayankha kuti: “Ayi!” 22  Choncho iwo anamufunsa kuti: “Nanga ndiwe ndani? Tiuze kuti tikathe kupereka yankho kwa amene atituma. Mwiniwakewe umati ndiwe ndani?” 23  Iye anati: “Ndine mawu a winawake amene akufuula mʼchipululu kuti, ‘Wongolani njira ya Yehova,’*+ monga mmene mneneri Yesaya ananenera.”+ 24  Anthuwo anatumidwa ndi Afarisi. 25  Choncho anamufunsa kuti: “Nanga nʼchifukwa chiyani umabatiza anthu ngati iweyo si iwe Khristu, Eliya kapena Mneneri?” 26  Yohane anawayankha kuti: “Ine ndimabatiza mʼmadzi. Pakati panu paimirira wina amene inu simukumudziwa. 27  Iye ndi amene akubwera mʼmbuyo mwangamu ndipo ine si woyenera kumasula zingwe za nsapato zake.”+ 28  Zinthu zimenezi zinachitikira ku Betaniya, kutsidya la Yorodano, kumene Yohane ankabatiza anthu.+ 29  Tsiku lotsatira anaona Yesu akubwera kwa iye, ndipo anati: “Taonani, Mwanawankhosa+ wa Mulungu amene akuchotsa uchimo+ wa dziko!+ 30  Uyu ndi amene ndinkanena uja kuti: ‘Amene akubwera mʼmbuyo mwangamu ndi wamkulu kuposa ine,* chifukwa anakhalapo ine ndisanabadwe.’+ 31  Inenso sindinkamudziwa, koma chifukwa chimene ndikubatizira anthu mʼmadzi nʼchakuti iyeyu aonekere kwa Isiraeli.”+ 32  Yohane anachitiranso umboni kuti: “Ndinaona mzimu ukutsika ngati nkhunda kuchokera kumwamba ndipo unakhalabe pa iye.+ 33  Inenso sindinkamudziwa, koma Mulungu amene anandituma kudzabatiza mʼmadzi anandiuza kuti: ‘Ukadzaona mzimu ukutsika nʼkukhazikika pamunthu wina,+ ameneyo ndi amene amabatiza ndi mzimu woyera.’+ 34  Ine ndinaonadi zimenezo ndipo ndachitira umboni kuti iyeyu ndi Mwana wa Mulungu.”+ 35  Tsiku lotsatira Yohane analinso ataima ndi ophunzira ake awiri, 36  ndipo ataona Yesu akuyenda, ananena kuti: “Onani, Mwanawankhosa+ wa Mulungu!” 37  Ophunzira awiriwo atamumva akunena zimenezi, anatsatira Yesu. 38  Kenako Yesu anacheuka, ndipo atawaona akumutsatira, anawafunsa kuti: “Kodi mukufunafuna chiyani?” Iwo anati: “Rabi, (dzina limeneli akalimasulira limatanthauza, “Mphunzitsi”) kodi mumakhala kuti?” 39  Iye anawauza kuti: “Tiyeni mukaoneko.” Choncho anapita kukaona kumene ankakhala ndipo anakhala naye tsiku limenelo. Apa nʼkuti nthawi ili cha mʼma 4 koloko madzulo.* 40  Andireya,+ mchimwene wake wa Simoni Petulo anali mmodzi wa awiriwo, amene anamva zimene Yohane ananena nʼkutsatira Yesu. 41  Choyamba iyeyu anakumana ndi mchimwene wake Simoni ndipo anamuuza kuti: “Ifetu tapeza Mesiya”+ (dzina limeneli akalimasulira limatanthauza, “Khristu”), 42  ndipo anapita naye kwa Yesu. Yesu atamuyangʼana anati: “Iwe ndiwe Simoni+ mwana wa Yohane, dzina lako likhala Kefa” (limene kumasulira kwake ndi “Petulo”).+ 43  Tsiku lotsatira, Yesu anaganiza zoti apite ku Galileya. Ndiyeno anakumana ndi Filipo+ nʼkumuuza kuti: “Ukhale wotsatira wanga.” 44  Filipo anali wochokera ku Betsaida, mzinda umene kunkachokera Andireya ndi Petulo. 45  Kenako Filipo anakumana ndi Natanayeli+ nʼkumuuza kuti: “Ife tapeza Yesu, mwana wa Yosefe,+ wa ku Nazareti. Chilamulo cha Mose komanso zimene aneneri analemba zimanena za iyeyu.” 46  Koma Natanayeli anamufunsa kuti: “Kodi mu Nazareti mungatuluke munthu aliyense wabwino?” Filipo anamuuza kuti: “Tiye ukaone.” 47  Yesu ataona Natanayeli akubwera kumene iye anali, ananena kuti: “Onani Mwisiraeli ndithu, amene mwa iye mulibe chinyengo.”+ 48  Natanayeli anamufunsa kuti: “Mwandidziwa bwanji?” Yesu anamuyankha kuti: “Filipo asanakuitane, ine ndinakuona uli pansi pa mtengo wamkuyu paja.” 49  Natanayeli anamuyankha kuti: “Rabi, ndinu Mwana wa Mulungu, ndinu Mfumu ya Isiraeli.”+ 50  Yesu anamuyankha kuti: “Kodi wakhulupirira chifukwa choti ndakuuza kuti ndinakuona uli pansi pa mtengo wamkuyu? Udzaona zinthu zazikulu kuposa zimenezi.” 51  Kenako anamuuza kuti: “Ndithu ndikukuuzani anthu inu, mudzaona kumwamba kutatseguka, angelo a Mulungu akukwera ndi kutsika kupita kumene kuli Mwana wa munthu.”+

Mawu a M'munsi

^ Kapena kuti, “anali ngati mulungu.”
^ Kapena kuti, “ankamusonyeza kukoma mtima kwakukulu.”
^ Kapena kuti, “pachifuwa cha Atate.” Izi zikusonyeza kuti ankakondedwa mwapadera.
^ Kapena kuti, “mwangamu wandipitirira.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 10,” kuwerenga kuchokera mʼma 6 koloko mʼmawa.