Wolembedwa ndi Yohane 11:1-57

  • Imfa ya Lazaro (1-16)

  • Yesu anatonthoza Marita ndi Mariya (17-37)

  • Yesu anaukitsa Lazaro (38-44)

  • Chiwembu choti aphe Yesu (45-57)

11  Tsopano panali munthu wina amene ankadwala, dzina lake Lazaro. Anali wamʼmudzi wa Betaniya, kwawo kwa Mariya ndi mchemwali wake Marita.+  Mariya ameneyu ndi uja amene anathira Ambuye mafuta onunkhira nʼkupukuta mapazi awo ndi tsitsi lake.+ Lazaro amene ankadwalayu anali mchimwene wake.  Choncho azichemwali akewo anatumiza uthenga kwa Yesu kuti: “Ambuye! amene mumamukonda uja akudwala.”  Koma Yesu atamva zimenezi ananena kuti: “Kudwala kumeneku si kwa imfa chabe, koma nʼkoti Mulungu alandire ulemerero+ komanso kuti Mwana wa Mulungu alemekezeke chifukwa cha kudwalako.”  Yesu ankakonda Marita ndi mchemwali wake komanso Lazaro.  Koma atamva kuti Lazaro akudwala, anakhalabe masiku ena awiri kumalo kumene iye anali.  Masiku awiriwo atatha, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Tiyeni tipitenso ku Yudeya.”  Ophunzirawo anamuuza kuti: “Rabi,+ posachedwapa Ayudeya amafuna kukugendani ndi miyala,+ ndiye mukufuna kupitanso komweko?”  Yesu anayankha kuti: “Kodi masana sali ndi maola 12?+ Munthu akamayenda masana palibe chimamupunthwitsa, chifukwa amaona kuwala kwa dzikoli. 10  Koma munthu akamayenda usiku, amapunthwa chifukwa mwa iye mulibe kuwala.” 11  Atanena zimenezi, anauza ophunzira akewo kuti: “Mnzathu Lazaro ali mʼtulo,+ koma ndikupita kumeneko kukamudzutsa.” 12  Pamenepo ophunzirawo anati: “Ambuye, ngati akugona apeza bwino.” 13  Apa Yesu ankatanthauza kuti Lazaro wamwalira. Koma iwo ankaganiza kuti akunena za kugona tulo teniteni. 14  Kenako Yesu anawauza mosapita mʼmbali kuti: “Lazaro wamwalira,+ 15  ndipo ine ndikusangalala chifukwa cha inu kuti sindinali kumeneko, kuti inu mukhulupirire. Koma tiyeni tipite kwa iye.” 16  Choncho Tomasi, amene ankadziwikanso kuti Didimo, anauza ophunzira anzakewo kuti: “Ifenso tiyeni tipite, kuti tikafere naye limodzi.”+ 17  Yesu atafika kumeneko, anapeza kuti Lazaro wakhala ali mʼmanda* masiku 4. 18  Mudzi wa Betaniya unali pafupi ndi Yerusalemu pa mtunda wa makilomita pafupifupi atatu.* 19  Tsopano Ayuda ambiri anabwera kwa Marita ndi Mariya kudzawatonthoza chifukwa cha imfa ya mchimwene wawo. 20  Choncho Marita atamva kuti Yesu akubwera, anapita kukamuchingamira, koma Mariya+ anatsala kunyumba. 21  Marita anauza Yesu kuti: “Ambuye, mukanakhala kuno mchimwene wanga sakanamwalira. 22  Komabe, ngakhale panopa ndikudziwa kuti chilichonse chimene mungapemphe kwa Mulungu, iye adzakupatsani.” 23  Yesu anamuuza kuti: “Mchimwene wako auka.” 24  Marita anati: “Ndikudziwa kuti adzauka pa kuuka kwa akufa+ mʼtsiku lomaliza.” 25  Yesu anamuuza kuti: “Ine ndine kuuka ndi moyo.+ Aliyense wokhulupirira ine, ngakhale atamwalira, adzakhalanso ndi moyo. 26  Komanso aliyense amene ali ndi moyo ndipo amandikhulupirira sadzafa.+ Kodi ukukhulupirira zimenezi?” 27  Iye anayankha kuti: “Inde, Ambuye. Ndimakhulupirira kuti ndinu Khristu Mwana wa Mulungu, amene anthu ankayembekezera kuti adzabwera mʼdzikoli.” 28  Atanena zimenezi, anapita kukaitana mchemwali wake Mariya nʼkumuuza mwachinsinsi kuti: “Mphunzitsi+ wabwera ndipo akukuitana.” 29  Mariya atamva zimenezo, ananyamuka mwamsanga nʼkupita kumene iye anali. 30  Pa nthawiyi nʼkuti Yesu asanalowe mʼmudzimo. Iye anali adakali kumalo kumene Marita anakumana naye. 31  Ayuda amene anali naye pamodzi mʼnyumbamo, amene ankamutonthoza, ataona Mariya akunyamuka mofulumira nʼkutuluka kunja, anamutsatira. Iwo ankaganiza kuti akupita kumanda*+ kukalira kumeneko. 32  Mariya atafika kumene kunali Yesu kuja nʼkumuona, anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi pafupi ndi mapazi a Yesu. Kenako anamuuza kuti: “Ambuye, mukanakhala kuno mchimwene wanga sakanamwalira.” 33  Yesu atamuona akulira komanso Ayuda amene anabwera naye pamodzi akuliranso, anadzuma povutika mumtima ndi kumva chisoni. 34  Kenako anafunsa kuti: “Mwamuika kuti?” Iwo anati: “Ambuye tiyeni mukaone.” 35  Yesu anagwetsa misozi.+ 36  Pamenepo Ayudawo anayamba kunena kuti: “Taonani, ankamukondadi kwambiri!” 37  Koma ena mwa iwo anati: “Kodi iyeyu, amene anatsegula maso a munthu wakhungu uja,+ sakanatha kuchita chinachake kuti mnzakeyu asamwalire?” 38  Kenako Yesu atadzumanso povutika mumtima, anafika kumandako.* Kwenikweni linali phanga, ndipo analitseka ndi chimwala. 39  Yesu anati: “Chotsani chimwalachi.” Marita, mchemwali wa womwalirayo anauza Yesu kuti: “Ambuye, pano ayenera kuti wayamba kununkha, chifukwa lero ndi tsiku la 4 chimuikireni mʼmanda.” 40  Yesu anamuuza kuti: “Kodi sindinakuuze kuti ngati ungakhulupirire udzaona ulemerero wa Mulungu?”+ 41  Choncho anachotsa chimwalacho. Kenako Yesu anakweza maso ake kumwamba+ nʼkunena kuti: “Atate, ndikukuyamikani kuti mwandimva. 42  Inde, ndikudziwa kuti mumandimva nthawi zonse, koma ndikunena izi chifukwa cha gulu la anthu amene aimirira panowa, kuti akhulupirire kuti inu munandituma ine.”+ 43  Atanena zimenezi, anafuula mokweza mawu kuti: “Lazaro, tuluka!”+ 44  Munthu amene anali wakufa uja anatuluka. Mapazi ndi manja ake anali okulungidwa ndi nsalu zamaliro, nkhope yakenso inali yomanga ndi nsalu. Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “Mʼmasuleni kuti athe kuyenda.” 45  Choncho Ayuda ambiri amene anabwera kwa Mariya nʼkuona zimene Yesu anachitazo anamukhulupirira.+ 46  Koma ena a iwo anapita kwa Afarisi kukawauza zimene Yesu anachita. 47  Zitatero ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhanitsa Khoti Lalikulu la Ayuda* nʼkunena kuti: “Kodi tichite chiyani pamenepa? Chifukwatu munthu uyu akuchita zizindikiro zochuluka.+ 48  Ngati titamulekerera, onse adzamukhulupirira ndipo Aroma adzabwera kudzatenga malo* athu ndi mtundu wathu.” 49  Koma mmodzi wa iwo, Kayafa,+ amene anali mkulu wa ansembe chaka chimenecho, anati: “Palibe chimene mukudziwa inu 50  ndipo simukuona kuti nʼzothandiza kwa inu kuti munthu mmodzi afere anthu onse mʼmalo moti mtundu wonse uwonongeke.” 51  Zimene ananenazi, sanaziganize pa iye yekha, koma chifukwa anali mkulu wa ansembe chaka chimenecho, analosera kuti Yesu adzafera mtunduwo. 52  Ndipo osati kufera mtundu chabe, komanso kuti asonkhanitse pamodzi ana a Mulungu amene anamwazikana. 53  Ndipo kuyambira tsiku limenelo anapangana zoti amuphe. 54  Choncho, Yesu sankayendayendanso moonekera kwa Ayuda. Koma anachoka kumeneko nʼkupita kudera lina lapafupi ndi chipululu, mumzinda umene unkatchulidwa kuti Efuraimu.+ Ndipo anakhala kumeneko limodzi ndi ophunzira ake. 55  Tsopano Pasika+ wa Ayuda anali atayandikira ndipo anthu ochuluka anachoka mʼmidzi nʼkupita ku Yerusalemu Pasikayo asanafike, kuti akachite mwambo wa kudziyeretsa. 56  Iwo ankafunafuna Yesu ndipo ankaima pamalo amodzi mʼkachisimo nʼkumakambirana kuti: “Mukuganiza bwanji? Kodi iye uja sabwera kuchikondwererochi?” 57  Koma ansembe aakulu ndi Afarisi analamula kuti aliyense amene angadziwe kumene kuli Yesu, aulule kuti iwo akamugwire.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mʼmanda achikumbutso.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “masitadiya pafupifupi 15.” Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “kumanda achikumbutso.”
Kapena kuti, “kumanda achikumbutsowo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Sanihedirini.”
Kutanthauza kachisi.