Wolembedwa ndi Yohane 4:1-54

  • Yesu ndi mayi wa ku Samariya (1-38)

    • Muzilambira Mulungu “motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi” (23, 24)

  • Asamariya ambiri anakhulupirira Yesu (39-42)

  • Yesu anachiritsa mwana wamwamuna wa mtumiki wa mfumu (43-54)

4  Ambuye atazindikira kuti Afarisi anamva kuti iyeyo* akuphunzitsa anthu ambiri kuti akhale ophunzira ake komanso kuwabatiza+ kuposa Yohane,  ngakhale kuti kwenikweni si Yesu amene ankawabatiza koma ophunzira ake,  anachoka ku Yudeya nʼkupitanso ku Galileya.  Koma anafunika kuti adzere ku Samariya.  Choncho anafika mumzinda wa Samariya wotchedwa Sukari, pafupi ndi munda umene Yakobo anapatsa mwana wake Yosefe.+  Ndipotu kumeneko kunali chitsime cha Yakobo.+ Ndiye Yesu atatopa ndi ulendowo, anakhala pansi pachitsimepo.* Nthawi nʼkuti ili cha mʼma 12 koloko masana.*  Ndiyeno mayi wina wa mu Samariya anafika kudzatunga madzi. Yesu anapempha mayiyo kuti: “Mundigawireko madzi akumwa mayi.”  (Ophunzira ake anali atalowa mumzinda kukagula chakudya.)  Ndiye mayi wa Chisamariyayo anafunsa Yesu kuti: “Popeza inu ndinu Myuda, bwanji mukupempha madzi akumwa kwa ine, mayi wa Chisamariya?” (Chifukwa Ayuda ndi Asamariya sagwirizana.)+ 10  Poyankha Yesu anauza mayiyo kuti: “Mukanadziwa za mphatso yaulere ya Mulungu+ komanso amene akukuuzani kuti, ‘Mundigawireko madzi akumwa,’ mukanamupempha iyeyo ndipo akanakupatsani madzi amoyo.”+ 11  Mayiyo anamuuza kuti: “Bambo, mulibe nʼchotungira chomwe ndipo chitsimechi nʼchozama. Ndiye madzi amoyowo mwawatenga kuti? 12  Kodi ndinu wamkulu kuposa kholo lathu Yakobo, amene anatipatsa chitsimechi, chimenenso iyeyo, ana ake ndi ngʼombe zake ankamwa?” 13  Poyankha, Yesu anamuuza kuti: “Aliyense amene wamwa madzi awa adzamvanso ludzu. 14  Koma amene adzamwe madzi amene ine ndidzamupatse sadzamvanso ludzu ngakhale pangʼono.+ Madzi amene ndidzamupatsewo adzasanduka kasupe wa madzi amene akutuluka mwa iye nʼkumupatsa moyo wosatha.”+ 15  Mayiyo anauza Yesu kuti: “Bambo, ndipatseni madzi amenewo, kuti ndisadzamvenso ludzu komanso kuti ndisamabwerenso kuno kudzatunga madzi.” 16  Iye anauza mayiyo kuti: “Pitani, mukaitane mwamuna wanu abwere kuno.” 17  Mayiyo anayankha kuti: “Ndilibe mwamuna.” Yesu anamuuza kuti: “Mwanena zoona poyankha kuti, ‘Ndilibe mwamuna.’ 18  Chifukwa mwakwatiwapo ndi amuna 5, ndipo mwamuna amene muli naye panopa si mwamuna wanu. Apa mwanenadi zoona.” 19  Mayiyo anamuuza kuti: “Bambo, ndazindikira kuti ndinu mneneri.+ 20  Makolo athu ankalambira mʼphiri ili, koma anthu inu mumanena kuti malo amene anthu akuyenera kulambirirako Mulungu ali ku Yerusalemu.”+ 21  Yesu anauza mayiyo kuti: “Ndithu ndikukuuzani mayi, nthawi idzafika pamene inu simudzalambira Atate mʼphiri ili kapena ku Yerusalemu. 22  Inu mumalambira chimene simuchidziwa.+ Ife timalambira chimene tikuchidziwa, chifukwa chipulumutso chikuyambira kwa Ayuda.+ 23  Komabe nthawi idzafika, ndipo ndi yomwe ino, pamene olambira oona adzalambira Atate motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi, chifukwa Atate akufuna kuti anthu ngati amenewo azimulambira.+ 24  Mulungu ndi Mzimu,+ ndipo amene akumulambira akuyenera kumulambira motsogoleredwa ndi mzimu komanso choonadi.”+ 25  Mayiyo ananena kuti: “Ndikudziwa kuti Mesiya akubwera, amene amadziwikanso kuti Khristu. Ameneyo akadzabwera, adzatifotokozera zonse poyera.” 26  Yesu anamuuza kuti: “Munthu ameneyo ndi ineyo, amene ndikulankhula nanu.”+ 27  Pa nthawiyo ophunzira ake anafika, ndipo anadabwa chifukwa ankalankhula ndi munthu wamkazi. Komabe palibe amene ananena kuti: “Mukufuna chiyani kwa iye?” kapena kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukulankhula ndi mayiyu?” 28  Choncho mayi uja anasiya mtsuko wake wa madzi nʼkukalowa mumzinda ndipo anauza anthu kuti: 29  “Tiyeni mukaone munthu amene wandiuza zonse zimene ndakhala ndikuchita. Kodi ameneyu sangakhale Khristu uja?” 30  Iwo anatuluka mumzindawo nʼkupita kumene kunali Yesu. 31  Apa nʼkuti ophunzira ake akumupempha kuti: “Rabi,+ idyani.” 32  Koma iye anawauza kuti: “Ndili ndi chakudya chimene inu simukuchidziwa.” 33  Ndiyeno ophunzirawo anayamba kufunsana kuti: “Pali amene wamubweretsera chakudya ngati?” 34  Yesu anawauza kuti: “Chakudya changa ndi kuchita zofuna za amene anandituma+ ndi kumaliza ntchito yake.+ 35  Kodi inu simunena kuti kwatsala miyezi 4 kuti tiyambe kukolola? Koma ndikukuuzani kuti: Kwezani maso anu muone mʼmindamo. Muona kuti mwayera kale ndipo mʼmofunika kukolola.+ Moti pano 36  wokolola akulandira malipiro ndipo akusonkhanitsa zipatso ku moyo wosatha, kuti wofesa mbewu ndi wokolola asangalalire limodzi.+ 37  Nʼchifukwa chake mawu akuti: Wina ndi wofesa ndipo wina ndi wokolola, ndi owona. 38  Ine ndakutumizani kukakolola zimene simunakhetsere thukuta. Ena anagwira ntchito mwakhama ndipo inu mukupindula ndi ntchito imene iwo anagwira.” 39  Asamariya ambiri ochokera mumzindawo anakhulupirira mwa iye chifukwa cha mawu a mayi uja. Mayiyo anachitira umboni kuti: “Iyeyu wandiuza zinthu zonse zimene ndakhala ndikuchita.”+ 40  Choncho Asamariyawo atafika kwa iye, anamupempha kuti akhalebe nawo ndipo anakhala kumeneko masiku awiri. 41  Zotsatira zake, anthu ochuluka anakhulupirira chifukwa cha zimene iye ananena, 42  ndipo anauza mayi uja kuti: “Sikuti tikukhulupirira chifukwa cha mawu ako okha aja ayi, chifukwa tadzimvera tokha ndipo tikudziwa kuti munthu uyu ndi mpulumutsidi wa dziko.”+ 43  Masiku awiriwo atatha, iye anachoka kumeneko nʼkupita ku Galileya. 44  Yesu mwiniwakeyo anachitira umboni kuti mneneri salemekezedwa kwawo.+ 45  Choncho atafika ku Galileya, anthu a ku Galileyako anamulandira chifukwa anali ataona zonse zimene anachita pachikondwerero ku Yerusalemu,+ popeza nawonso anapita kuchikondwereroko.+ 46  Kenako anafikanso ku Kana wa ku Galileya, kumene anasandutsa madzi kukhala vinyo kuja.+ Tsopano kumeneku kunali munthu wina amene ankatumikira mfumu, amene mwana wake wamwamuna ankadwala ku Kaperenao. 47  Munthuyu atamva kuti Yesu wafika ku Galileya kuchokera ku Yudeya, anapita kwa iye kukamupempha kuti apite ku Kaperenao nʼkukachiritsa mwana wakeyo, chifukwa anali atatsala pangʼono kumwalira. 48  Koma Yesu anamuuza kuti: “Anthu inu simungakhulupirire ngakhale pangʼono pokhapokha mutaona zizindikiro ndi zodabwitsa.”+ 49  Mtumiki wa mfumu uja anamuuza kuti: “Ambuye, tiyeni mwana wanga asanafe.” 50  Yesu anamuuza kuti: “Pita, mwana wako ali moyo.”+ Munthuyo anakhulupirira mawu amene Yesu anamuuzawo ndipo anapitadi. 51  Koma ali mʼnjira, akapolo ake anamuchingamira kudzamuuza kuti mnyamata wake ali moyo.* 52  Choncho iye anawafunsa ola limene anachira ndipo iwo anamuyankha kuti: “Malungo* ake atha dzulo cha mʼma 1 koloko masana.”* 53  Atatero bamboyo anadziwa kuti linali ola lomwelo pamene Yesu anamuuza kuti: “Mwana wako ali moyo.”+ Choncho iye ndi banja lake lonse anakhulupirira. 54  Chimenechi chinali chizindikiro chachiwiri+ chimene Yesu anachita atachoka ku Yudeya nʼkupita ku Galileya.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Yesu.”
Kapena kuti, “pakasupepo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 6,” kuwerenga kuchokera mʼma 6 koloko mʼmawa.
Kapena kuti, “mnyamata wake wachira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kutentha thupi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 7,” kuwerenga kuchokera mʼma 6 koloko mʼmawa.