Kwa Akolose 1:1-29

  • Moni (1, 2)

  • Kuthokoza chifukwa cha chikhulupiriro cha Akolose (3-8)

  • Kuwapempherera kuti akule mwauzimu (9-12)

  • Udindo waukulu wa Khristu (13-23)

  • Paulo anagwira ntchito mwakhama pothandiza mpingo (24-29)

1  Ine Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa kufuna kwa Mulungu, ndili limodzi ndi Timoteyo+ mʼbale wathu.  Ndikulembera oyera ndi abale okhulupirika amene ali ogwirizana ndi Khristu ku Kolose kuti: Mulungu Atate wathu akupatseni kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere.  Nthawi zonse tikamakupemphererani, timathokoza Mulungu, Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.  Timachita zimenezi chifukwa tinamva za chikhulupiriro chanu mwa Khristu Yesu komanso za chikondi chimene mukusonyeza oyera onse  chifukwa cha chiyembekezo chodzalandira zinthu zimene akusungirani kumwamba.+ Munamva za chiyembekezo chimenechi mʼmbuyomu pamene munamva uthenga wa choonadi, womwe ndi uthenga wabwino  umene unafika kwa inu. Uthenga wabwino ukubala zipatso ndiponso kufalikira padziko lonse.+ Zimenezi ndi zimenenso zakhala zikuchitika kwa inu kuyambira tsiku limene munamva ndi kudziwa molondola za kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu komwe ndi kwenikweni.  Zimenezi ndi zimene munaphunzira kwa Epafura,+ kapolo mnzathu wokondedwa, amene ndi mtumiki wokhulupirika wa Khristu mʼmalo mwa ife.  Iye ndi amenenso anatidziwitsa za chikondi chanu chimene munachisonyeza mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu.*  Nʼchifukwa chake ifenso, kuyambira tsiku limene tinamva zimenezo, sitinasiye kukupemphererani.+ Takhala tikupempha kuti mudziwe molondola+ chifuniro cha Mulungu ndiponso kuti mukhale ndi nzeru zonse komanso muzimvetsetsa zinthu zauzimu.+ 10  Tachita zimenezi nʼcholinga choti mukhale ndi khalidwe logwirizana* ndi zimene Yehova* amafuna, kuti muzimusangalatsa pa chilichonse, pamene mukupitiriza kubala zipatso pantchito iliyonse yabwino ndi kuwonjezera kumudziwa Mulungu molondola.+ 11  Tikupemphanso kuti mulandire mphamvu zazikulu mogwirizana ndi mphamvu zake zochititsa mantha,+ nʼcholinga choti muthe kupirira zinthu zonse moleza mtima ndiponso mwachimwemwe, 12  komanso muzithokoza Atate, amene anapangitsa kuti mukhale oyenerera kulandira nawo cholowa cha oyera+ amene ali mʼkuwala. 13  Iye anatipulumutsa ku ulamuliro wa mdima,+ nʼkutisamutsira mu ufumu wa Mwana wake wokondedwa. 14  Kudzera mwa Mwana wakeyo, tinamasulidwa ndi dipo* ndipo machimo athu amakhululukidwa.+ 15  Iye ndi chifaniziro cha Mulungu wosaonekayo,+ woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.+ 16  Kudzera mwa iye, Mulungu analenga zinthu zina zonse kumwamba ndi padziko lapansi. Analenga zinthu zooneka ndi zinthu zosaoneka,+ kaya ndi mipando yachifumu, ambuye, maboma komanso maulamuliro. Inde, analenga zinthu zina zonse kudzera mwa iye+ ndiponso chifukwa cha iye. 17  Ndiponso iye analipo kale zinthu zina zonse zisanakhaleko+ ndipo zinthu zina zonse zinakhalapo kudzera mwa iye. 18  Iye ndi mutu wa thupi, lomwe ndi mpingo.+ Iye ndi chiyambi, woyamba kubadwa kuchokera kwa akufa,+ kuti adzakhale woyamba pa zinthu zonse. 19  Zili choncho chifukwa chakuti Mulungu zinamusangalatsa kuti makhalidwe ake onse akhale mwa Khristu.+ 20  Komanso kuti kudzera mwa mwana wakeyo agwirizanitsenso zinthu zina zonse+ ndi iyeyo, kaya zinthuzo ndi zapadziko lapansi kapena zakumwamba. Anachita zimenezi pokhazikitsa mtendere kudzera mʼmagazi+ amene Khristu anakhetsa pamtengo wozunzikirapo.* 21  Ndithudi, inu amene kale munali otalikirana ndi Mulungu ndiponso adani ake chifukwa maganizo anu anali pa ntchito zoipa, 22  tsopano wagwirizana nanunso kudzera mu imfa ya mwana wake amene anapereka thupi lake lanyama nʼcholinga choti akuperekeni pamaso pa Mulunguyo, muli opatulika ndi opanda chilema ndiponso opanda chifukwa chokunenezerani.+ 23  Koma mukuyenera kupitiriza kukhala mogwirizana ndi chikhulupiriro chanu,+ muli okhazikika pamaziko,+ muli olimba+ komanso muli osasunthika pa chiyembekezo cha uthenga wabwino umene munamva, umenenso unalalikidwa padziko lonse.*+ Ineyo Paulo ndinakhala mtumiki wa uthenga wabwino umenewu.+ 24  Tsopano ndikusangalala ndi mavuto amene ndikukumana nawo chifukwa cha inu.+ Ndipo inenso ndikuona kuti sindinazunzikebe mokwanira monga chiwalo cha thupi la Khristu,+ limene ndi mpingo.+ 25  Ndinakhala mtumiki wa mpingo umenewu mogwirizana ndi udindo+ umene Mulungu anandipatsa woti ndilalikire mawu a Mulungu mokwanira, kuti inuyo mupindule. 26  Mawuwo akuphatikizapo chinsinsi chopatulika+ chimene dziko silinachidziwe+ ndiponso chinali chobisika kwa mibadwo yakale. Koma tsopano chaululidwa kwa oyera ake.+ 27  Mulungu zinamusangalatsa kuululira oyera pakati pa anthu a mitundu ina chinsinsi chopatulikachi,+ chomwe chili ndi ulemerero wochuluka komanso chuma chauzimu. Chinsinsi chimenechi ndi Khristu amene ndi wogwirizana ndi inuyo, kutanthauza kuti muli ndi chiyembekezo chodzalandira ulemerero limodzi ndi Khristuyo.+ 28  Tikulengeza, kuchenjeza ndi kuphunzitsa munthu aliyense za iyeyu mu nzeru zonse, kuti tipereke munthu aliyense kwa Mulungu ali wolimba mwauzimu mogwirizana ndi Khristu.+ 29  Kuti ndikwanitse kuchita zimenezi, ndikugwira ntchito mwakhama ndipo ndikuyesetsa kwambiri podalira mphamvu zake zimene zikugwira ntchito mwamphamvu mwa ine.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mumzimu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “muziyenda mogwirizana.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼchilengedwe chonse cha pansi pa thambo.”