Kwa Akolose 3:1-25

  • Umunthu wakale komanso watsopano (1-17)

    • Chititsani ziwalo za thupi lanu kukhala zakufa (5)

    • Chikondi chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse (14)

  • Malangizo opita ku mabanja a Chikhristu (18-25)

3  Komabe, ngati munaukitsidwa limodzi ndi Khristu,+ pitirizani kufunafuna zinthu zakumwamba, kumene Khristu wakhala kudzanja lamanja la Mulungu.+ 2  Pitirizani kuganizira zinthu zakumwamba,+ osati zinthu zapadziko lapansi.+ 3  Chifukwa munafa ndipo moyo wanu wabisidwa limodzi ndi Khristu amene ndi wogwirizana ndi Mulungu. 4  Khristu, amene ndi moyo wathu,+ akadzaonetsa mphamvu zake,* inunso mudzaonetsa naye limodzi mphamvu zanu mu ulemerero.+ 5  Choncho chititsani ziwalo za thupi lanu+ padziko lapansi kukhala zakufa ku chiwerewere,* zinthu zodetsa, chilakolako chosalamulirika cha kugonana,+ kulakalaka zinthu zoipa komanso dyera limene ndi kulambira mafano. 6  Mulungu adzasonyeza mkwiyo wake kwa anthu amene akuchita zimenezi. 7  Inunso munkachita zomwezo, pamene munkakhala moyo wofanana ndi anthu amenewo.+ 8  Koma tsopano muyenera kutaya zonsezo kutali ndi inu. Mutaye mkwiyo, kupsa mtima, kuipa+ komanso mawu achipongwe+ ndipo pakamwa panu pasatuluke nkhani zotukwana.+ 9  Musamanamizane.+ Vulani umunthu* wakale+ pamodzi ndi ntchito zake, 10  ndipo muvale umunthu watsopano+ umene Mulungu amapereka. Umunthu watsopano umenewu ndi wopangidwa mogwirizana ndi chifaniziro cha Mulungu.+ Choncho pamene mukudziwa Mulungu molondola, pitirizani kuchititsa umunthu wanu kukhala watsopano. 11  Mukatero, sipadzakhala Mgiriki kapena Myuda, kudulidwa kapena kusadulidwa, mlendo, Msukuti,* kapolo kapena mfulu, chifukwa Khristu amachita zinthu zonse ndipo ife ndife ogwirizana naye.+ 12  Choncho monga anthu osankhidwa ndi Mulungu,+ oyera ndi okondedwa, valani chifundo chachikulu,+ kukoma mtima, kudzichepetsa,+ kufatsa+ komanso kuleza mtima.+ 13  Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse,+ ngakhale pamene wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake.+ Mofanana ndi Yehova* amene anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso muzichita chimodzimodzi.+ 14  Koma kuwonjezera pa zonsezi, valani chikondi,+ chifukwa chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.+ 15  Komanso lolani kuti mtendere wa Khristu ulamulire mʼmitima yanu,+ popeza munaitanidwa ku mtendere umenewu monga ziwalo za thupi limodzi. Ndipo sonyezani kuti ndinu oyamikira. 16  Mawu a Khristu akhazikike mwa inu ndipo akupatseni nzeru zonse. Pitirizani kuphunzitsana ndi kulimbikitsana* ndi masalimo,+ nyimbo zotamanda Mulungu komanso nyimbo zauzimu zoyamikira. Pitirizani kuimbira Yehova* mʼmitima yanu.+ 17  Chilichonse chimene mukuchita mʼmawu kapena mu ntchito, muzichita zonse mʼdzina la Ambuye Yesu, ndipo muziyamika Mulungu Atate kudzera mwa iye.+ 18  Inu akazi, muzigonjera amuna anu,+ chifukwa zimenezi ndi zoyenera kwa anthu otsatira Ambuye. 19  Inu amuna, pitirizani kukonda akazi anu+ ndipo musamawapsere mtima kwambiri.*+ 20  Ana inu, muzimvera makolo anu pa zinthu zonse,+ chifukwa zimenezi zimasangalatsa Ambuye. 21  Inu abambo, musamakwiyitse* ana anu,+ kuti asakhale okhumudwa. 22  Inu akapolo, muzimvera anthu amene ndi ambuye anu+ pa zinthu zonse, osati pokhapokha pamene akukuonani pongofuna kusangalatsa anthu,* koma moona mtima ndiponso moopa Yehova.* 23  Chilichonse chimene mukuchita, muzichichita ndi moyo wanu wonse ngati kuti mukuchitira Yehova,*+ osati anthu, 24  chifukwa mukudziwa kuti mphoto imene mudzalandire ndi cholowa chochokera kwa Yehova.*+ Tumikirani Ambuye wanu Khristu monga akapolo. 25  Ndithudi, amene akuchita zolakwa adzalandira chilango chifukwa cha zolakwa zimene akuchitazo,+ chifukwa Mulungu sakondera.+

Mawu a M'munsi

^ Mʼchilankhulo choyambirira, “akadzaonetsedwa.”
^ MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “munthu.”
^ Mawu akuti “Msukuti” akutanthauza munthu wachimidzimidzi.
^ Kapena kuti, “kulangizana.”
^ Kapena kuti, “ndipo musamawachitire nkhanza.”
^ Kapena kuti, “musamapsetse mtima.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “osati mwachiphamaso ngati munthu wongofuna kusangalatsa anthu.”