Kwa Akolose 4:1-18

  • Malangizo opita kwa ambuye (1)

  • “Muzilimbikira kupemphera” (2-4)

  • Kuchita zinthu mwanzeru pokhala ndi anthu akunja (5, 6)

  • Moni womaliza (7-18)

4  Inu anthu amene ndinu ambuye, muzichitira akapolo anu zinthu zachilungamo ndi zoyenera, chifukwa mukudziwa kuti inunso muli ndi Ambuye kumwamba.+  Muzilimbikira kupemphera.+ Mukhale maso pa nkhani ya kupemphera ndipo muziyamikira.+  Komanso muzitipempherera ifeyo+ kuti Mulungu atitsegulire khomo kuti tithe kulalikira mawu ndi kulankhula za chinsinsi chopatulika chokhudza Khristu, chimene chinachititsa kuti ndimangidwe nʼkukhala mʼndende muno,+  kuti ndidzalalikire za chinsinsicho momveka bwino ngati mmene ndiyenera kuchitira.  Pitirizani kuchita zinthu mwanzeru pamene mukukhala ndi anthu akunja, ndipo muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.*+  Nthawi zonse mawu anu azisonyeza kuti ndinu okoma mtima ndipo azikhala okoma ngati kuti mwawathira mchere,+ kuti mudziwe mmene mungayankhire munthu aliyense.+  Tukiko+ amene ndi mʼbale wanga wokondedwa, mtumiki wokhulupirika komanso kapolo mnzanga mwa Ambuye, adzakuuzani zonse zokhudza ine.  Ndikumutumiza kwa inu kuti mudziwe mmene tilili komanso kuti alimbikitse mitima yanu.  Abwera limodzi ndi Onesimo,+ mʼbale wanga wokhulupirika ndi wokondedwa, amene anachokera pakati panu. Iwo adzakuuzani zonse zimene zikuchitika kuno. 10  Arisitako+ mkaidi mnzanga akuti moni nonse. Komanso Maliko+ msuweni wa Baranaba, (amene ndinakulangizani kuti mumulandire+ nthawi iliyonse akadzafika kwa inu), 11  ndi Yesu, amene amadziwikanso kuti Yusito, akuti moni. Iwowa ali mʼgulu la anthu odulidwa. Amenewa okha ndi antchito anzanga pa zinthu zokhudzana ndi Ufumu wa Mulungu ndipo amandilimbikitsa kwambiri. 12  Epafura,+ amene anachokera pakati panu, kapolo wa Khristu Yesu, akuti moni. Iye amakupemphererani mwakhama nthawi zonse kuti mupitirize kukhala olimba mwauzimu komanso kuti musamakayikire ngakhale pangʼono zinthu zonse zimene Mulungu adzachite. 13  Ndikumuchitiradi umboni kuti amadzipereka kwambiri chifukwa cha inu komanso chifukwa cha abale a ku Laodikaya ndi ku Herapoli. 14  Luka,+ dokotala wokondedwa, akuti moni nonse. Dema+ nayenso akupereka moni. 15  Mundiperekere moni kwa abale a ku Laodikaya komanso kwa Numfa ndi mpingo umene umasonkhana panyumba pake.+ 16  Kalatayi mukaiwerenga kwanuko, konzani zoti ikawerengedwenso+ kumpingo wa Alaodikaya, ndiponso kuti inuyo muwerenge yochokera ku Laodikaya. 17  Komanso Arikipo+ mumuuze kuti: “Uonetsetse kuti utumiki umene unaulandira mwa Ambuye ukuukwaniritsa.” 18  Tsopano landirani moni wanga wolemba ndekha ndi dzanja langa,+ ineyo Paulo. Pitirizani kukumbukira maunyolo amene andimanga nawo kundende kuno.+ Kukoma mtima kwakukulu kukhale nanu.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndipo muzigula nthawi yoikidwiratu.”