Yeremiya 7:1-34

  • Kukhulupirira kachisi wa Yehova sikunawathandize (1-11)

  • Kachisi adzakhala ngati Silo (12-15)

  • Mulungu sasangalala ndi kulambira kwachinyengo (16-34)

    • “Analambira “Mfumukazi Yakumwamba” (18)

    • Ankapereka nsembe ana ku Hinomu (31)

7  Awa ndi mawu amene Yehova anauza Yeremiya. Iye anamuuza kuti:  “Ukaime pageti la nyumba ya Yehova ndipo ukalengeze uthenga uwu, ‘Tamverani mawu a Yehova inu anthu nonse a mu Yuda, amene mumalowa pamageti awa kuti mukalambire Yehova.  Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Sinthani njira zanu komanso zochita zanu ndipo muzichita zabwino. Mukatero ine ndidzakulolani kuti mupitirize kukhala mʼdziko lino.+  Musamakhulupirire mawu achinyengo nʼkumanena kuti, ‘Uyu* ndi kachisi wa Yehova, inde ndi kachisi wa Yehova, ndithudi ndi kachisi wa Yehova!’+  Ngati mutasinthadi njira zanu ndi zochita zanu kuti zikhale zabwino, ngati mutamaweruza mwachilungamo pakati pa munthu ndi mnzake,+  ngati simudzapondereza alendo okhala pakati panu, ana amasiye ndi akazi amasiye,+ komanso ngati simudzakhetsa magazi a munthu wosalakwa mʼdziko lino ndiponso ngati simudzatsatira milungu ina, zimene zingakubweretsereni mavuto,+  inenso ndidzakulolani kuti mupitirize kukhala mʼdziko lino, dziko limene ndinapatsa makolo anu, kuti azikhalamo mpaka kalekale.”’”  “Koma inu mukukhulupirira mawu achinyengo+ ndipo sakuthandizani ngakhale pangʼono.  Kodi mungamabe,+ kupha, kuchita chigololo, kulumbira monama,+ kupereka nsembe* kwa Baala+ ndiponso kutsatira milungu ina imene simunkaidziwa, 10  kenako nʼkubwera kudzaima pamaso panga mʼnyumba iyi, imene imatchedwa ndi dzina langa nʼkumanena kuti, ‘Tidzapulumutsidwa,’ ngakhale kuti mukuchita zinthu zonyansa zonsezi? 11  Kodi nyumba iyi, imene imatchedwa ndi dzina langa, mwayamba kuiona ngati phanga la achifwamba?+ Inetu ndaona zimene mukuchita,” akutero Yehova. 12  “‘Pitani kumalo anga ku Silo,+ kumene poyamba kunali dzina langa,+ ndipo mukaone zimene ndinachitira malowo chifukwa cha kuipa kwa anthu anga Aisiraeli.+ 13  Koma inu munapitiriza kuchita zinthu zonsezi,’ akutero Yehova, ‘ndipo ngakhale kuti ndinkalankhula nanu mobwerezabwereza,* inu simunamvere.+ Ndinapitiriza kukuitanani koma inu simunayankhe.+ 14  Choncho nyumba imene ikudziwika ndi dzina langa,+ imene mukuidalira+ ndiponso pamalo awa amene ndinawapereka kwa inu ndi makolo anu, ndidzachita zofanana ndi zimene ndinachita ku Silo.+ 15  Ine ndidzakuchotsani pamaso panga ngati mmene ndinachotsera abale anu onse, mbadwa zonse za Efuraimu.’+ 16  Koma iwe usawapempherere anthu awa. Usafuule kwa ine, kuwapempherera kapena kundichonderera kuti ndiwathandize,+ chifukwa ine sindidzakumvetsera.+ 17  Kodi sukuona zimene akuchita mʼmizinda ya Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu? 18  Ana aamuna akutola nkhuni, abambo akuyatsa moto ndipo akazi awo akukanda ufa kuti apange makeke okapereka nsembe kwa ‘Mfumukazi Yakumwamba.’*+ Ndipo akuthira pansi nsembe zachakumwa kwa milungu ina kuti andikhumudwitse.+ 19  ‘Koma kodi iwo akukhumudwitsa ine?’ akutero Yehova. ‘Kodi iwo sakudzikhumudwitsa okha nʼkudzichititsa manyazi?’+ 20  Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Taonani! Mkwiyo wanga ndi ukali wanga zidzatsanulidwa pamalo awa,+ pamunthu, pachiweto, pamitengo yakuthengo ndi pachipatso chilichonse chochokera mʼnthaka. Mkwiyowo udzayaka ndipo sudzazimitsidwa.’+ 21  Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Wonjezerani nsembe zanu zopsereza zathunthu pansembe zanu zinazo ndipo muzidye nokha.+ 22  Chifukwatu pa tsiku limene ndinatulutsa makolo anu mʼdziko la Iguputo, sindinalankhule nawo chilichonse kapena kuwalamula zokhudza kupereka nsembe zopsereza zathunthu ndi nsembe zina.+ 23  Koma ndinawalamula kuti: “Muzimvera mawu anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu, inuyo mudzakhala anthu anga.+ Muziyenda mʼnjira imene ndakulamulani, kuti zinthu zikuyendereni bwino.”’+ 24  Koma iwo sanamvere kapena kutchera khutu.+ Mʼmalomwake, anayenda motsatira zofuna zawo. Mouma khosi anatsatira zofuna za mtima wawo woipawo,+ moti anabwerera mʼmbuyo mʼmalo mopita patsogolo, 25  kuchokera tsiku limene makolo anu anatuluka mʼdziko la Iguputo mpaka pano.+ Choncho ndinapitiriza kukutumizirani atumiki anga onse omwe ndi aneneri, ndinkawatumiza tsiku lililonse, mobwerezabwereza.*+ 26  Koma iwo anakana kundimvera ndipo sanatchere khutu lawo.+ Mʼmalomwake anaumitsa khosi lawo ndipo ankachita zinthu zoipa kuposa makolo awo. 27  Udzawauza mawu onsewa,+ koma iwo sadzakumvera. Udzawaitana koma sadzakuyankha. 28  Ndipo udzawauze kuti, ‘Uwu ndi mtundu wa anthu umene sunamvere mawu a Yehova Mulungu wawo, ndipo anakana kulandira malangizo.* Palibe munthu wokhulupirika pakati pawo ndipo satchulanso nʼkomwe za kukhulupirika.’*+ 29  Meta tsitsi lako lalitalilo* nʼkulitaya ndipo ukwere pamapiri opanda mitengo nʼkukaimba nyimbo yoimba polira, chifukwa Yehova wakana ndiponso wasiya mʼbadwo uwu umene wamukwiyitsa. 30  ‘Chifukwa mbadwa za Yuda zachita zinthu zoipa mʼmaso mwanga,’ akutero Yehova. ‘Aika mafano awo onyansa mʼnyumba imene imadziwika ndi dzina langa nʼcholinga choti aidetse.+ 31  Iwo amanga malo okwera ku Tofeti, mʼChigwa cha Mwana wa Hinomu,*+ kuti aziwotcha ana awo aamuna ndi ana awo aakazi pamoto,+ chinthu chimene sindinawalamule kuti azichita ndiponso chimene sindinachiganizirepo mumtima mwanga.’*+ 32  ‘Choncho taonani! Masiku akubwera,’ akutero Yehova, ‘pamene sadzatchulanso malowo kuti Tofeti kapena kuti Chigwa cha Mwana wa Hinomu,* koma adzawatchula kuti Chigwa Chopherako Anthu. Iwo adzaika anthu mʼmanda ku Tofeti mpaka malo onse adzatha.+ 33  Mitembo ya anthu awa idzakhala chakudya cha mbalame zouluka mumlengalenga ndi cha zilombo ndipo sipadzakhala woziopseza.+ 34  Ndidzathetsa phokoso lachikondwerero, phokoso lachisangalalo, mawu a mkwati ndi mawu a mkwatibwi,+ mʼmizinda ya Yuda ndi mʼmisewu ya Yerusalemu, chifukwa dzikoli lidzawonongedwa nʼkukhala mabwinja okhaokha.’”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Nyumba izi,” kutanthauza nyumba zonse zimene zinali pakachisi.
Kapena kuti, “nsembe zautsi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ngakhale kuti ndinkadzuka mʼmamawa nʼkulankhula nanu.”
Limeneli ndi dzina laulemu la mulungu wamkazi amene Aisiraeli opanduka ankamulambira. Iwo ankakhulupirira kuti ameneyu ndi mulungu amene ankathandiza akazi kuti azibereka.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Tsiku lililonse ndinkadzuka mʼmamawa nʼkuwatumiza.”
Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga, kapena uphungu.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndipo kukhulupirika kwachotsedwa mʼkamwa mwawo.”
Kapena kuti, “tsitsi lomwe ndi chizindikiro cha kudzipereka.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena, “Gehena.”
Kapena kuti, “chimene sichinabwerepo mʼmaganizo mwangamu.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena, “Gehena.”