Yeremiya 19:1-15

  • Yeremiya anauzidwa kuti akaswe botolo la dothi (1-15)

    • Kupereka ana nsembe kwa Baala (5)

19  Yehova wanena kuti: “Pita, ukagule botolo ladothi kwa woumba mbiya.+ Utenge ena mwa atsogoleri a anthu ndi ena mwa akuluakulu a ansembe,  nʼkupita ku Chigwa cha Mwana wa Hinomu,+ pakhomo la Geti la Mapale. Kumeneko ukanene mawu onse amene ndikuuze.  Ukawauze kuti, ‘Tamverani mawu a Yehova inu mafumu a Yuda ndi inu anthu amene mukukhala mu Yerusalemu. Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: ‘“Ine ndatsala pangʼono kubweretsa tsoka pamalo ano ndipo aliyense akadzamva za tsoka limeneli, mʼmakutu mwake mudzachita phokoso.  Ndidzachita zimenezi chifukwa iwo andisiya+ ndiponso achititsa kuti malo ano ndisawazindikire.+ Pamalo ano iwo akupereka nsembe kwa milungu ina, imene iwowo, makolo awo komanso mafumu a Yuda sankaidziwa ndipo adzaza malo ano ndi magazi a anthu osalakwa.+  Iwo amangira Baala malo okwera kuti aziwotcha pamoto ana awo aamuna ngati nsembe zopsereza zathunthu zoperekedwa kwa Baala.+ Ine sindinawalamule zimenezi kapena kuzitchula ndipo sindinaziganizirepo mumtima mwanga.+  Choncho taonani! masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene sadzatchulanso malowo kuti Tofeti kapena Chigwa cha Mwana wa Hinomu, koma adzawatchula kuti Chigwa Chopherako Anthu.+  Ndidzasokoneza zolinga za Yuda ndi za Yerusalemu mʼmalo ano, ndipo ndidzachititsa kuti aphedwe ndi lupanga la adani awo komanso ndi anthu amene akufunafuna moyo wawo. Mitembo yawo ndidzaipereka kwa mbalame zamumlengalenga ndi zilombo zakutchire kuti ikhale chakudya chawo.+  Mzindawu ndidzausandutsa chinthu chochititsa mantha komanso chimene anthu azidzachiimbira mluzu. Aliyense wodutsa pafupi ndi mzindawo adzauyangʼanitsitsa mwamantha ndipo adzauimbira mluzu chifukwa cha miliri yake yonse.+  Ndidzawachititsa kudya mnofu wa ana awo aamuna ndi ana awo aakazi. Aliyense adzadya mnzake chifukwa adani adzawazungulira komanso chifukwa chosowa mtengo wogwira. Izi zidzachitika pamene adani awo ndiponso anthu amene akufuna moyo wawo adzawapanikize.”’+ 10  Kenako ukaswe botololo pamaso pa amuna amene akupita nawe, 11  ndiyeno ukawauze kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Mofanana ndi zimenezi, ndidzaswa anthu awa ndi mzinda uwu ngati mmene munthu amaswera botolo lopangidwa ndi woumba mbiya moti silingathe kukonzedwanso. Iwo adzaika maliro ku Tofeti mpaka sipadzapezekanso malo oika maliro kumeneko.”’+ 12  ‘Izi ndi zimene ndidzachite ndi malo awa ndiponso ndi anthu onse amene akukhala mmenemu kuti mzindawu ukhale ngati Tofeti,’ akutero Yehova. 13  ‘Nyumba za mu Yerusalemu ndi nyumba za mafumu a Yuda zidzakhala zodetsedwa ngati malo ano a Tofeti.+ Zimenezi ndi nyumba zonse zimene pamadenga ake ankaperekapo nsembe kwa gulu lonse la zinthu zakuthambo+ ndi kuthirapo nsembe zachakumwa kwa milungu ina.’”+ 14  Yeremiya atabwerako ku Tofeti kumene Yehova anamutuma kuti akalosere, anakaima mʼbwalo la nyumba ya Yehova nʼkuuza anthu onse kuti: 15  “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Ine ndikubweretsera mzinda uwu ndi matauni ake onse masoka onse amene ndinanena, chifukwa anthu ake aumitsa mitima yawo nʼkukana* kumvera mawu anga.’”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “aumitsa nkhosi lawo kuti asamvere.”